Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Ndi Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale mu Utumiki

Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Ndi Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale mu Utumiki

Ndife osangalala kwambiri kuti tili ndi kabuku komanso buku latsopano lomwe tizigwiritsa ntchito pochititsa maphunziro a Baibulo. Tikupempha Yehova kuti atidalitse pamene tikuyesetsa kuphunzitsa anthu ambiri. (Mt 28:18-20; 1Ak 3:6-9) Kodi tizigwiritsa ntchito bwanji zinthu zatsopanozi?

Buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale lizitithandiza kuphunzira Baibulo ndi anthu mochita kukambirana. M‘bukuli muli njira yatsopano yophunzitsira anthu, choncho mukamakonzekera komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo muzigwiritsa ntchito njira zotsatirazi. *

  • Muziwerenga ndime komanso kukambirana mafunso

  • Muziwerenga malemba akuti “werengani” ndipo muzimuthandiza wophunzirayo kumvetsa mmene angawagwiritsire ntchito

  • Muzionera komanso kukambirana mavidiyo pogwiritsa ntchito mafunso amene aperekedwa

  • Muziyesetsa kumaliza phunziro lililonse pa ulendo umodzi

Tikakhala mu utumiki tiziyamba ndi kugawira kabuku kuti tione ngati munthu ali ndi chidwi. (Onani bokosi lakuti “ Zimene Tingachite Kuti Tigawire Kabuku Kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pa Ulendo Woyamba.”) Ngati mwamaliza kuphunzira limodzi kabukuka ndipo wophunzirayo akufuna kupitiriza kuphunzira, muzimugawira buku ndi kuyamba kuphunzira naye phunziro 04. Ngati mukuphunzira ndi munthu pogwiritsa ntchito buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa kapena lakuti Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani, yambani kuphunzira naye buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale n’kuona pamene mungayambire.

ONERANI VIDIYO YAKUTI SANGALALANI POPHUNZIRA BAIBULO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

^ ndime 4 DZIWANI IZI: Ngakhale kuti mukhoza kusankha kugwiritsa ntchito kachigawo kakuti “Onani Zinanso” pa nthawi ya phunziro, muziyesetsa kupeza nthawi yowerenga komanso kuonera mavidiyo onse pamene mukukonzekera. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwa zimene zingafike pamtima komanso kuthandiza wophunzira wanuyo. M’kabuku komanso m’buku la pazipangizo zamakono muli malinki a mavidiyo komanso zinthu zina zowonjezera.

 CHOLINGA CHA CHIGAWO CHILICHONSE KOMANSO ZOMWE WOPHUNZIRA AKULIMBIKITSIDWA KUCHITA

PHUNZIRO

CHOLINGA CHAKE

ZOMWE WOPHUNZIRA AKULIMBIKITSIDWA KUCHITA

1

01-12

Kukambirana mmene Baibulo lingakuthandizireni komanso zimene mungachite kuti mudziwe amene analilemba

Kuwerenga Baibulo, kukonzekera phunziro komanso kuyamba kupezeka pamisonkhano

2

13-33

Kukambirana zimene Mulungu watichitira komanso kulambira kumene kumamusangalatsa

Kuuza ena mfundo za choonadi komanso kukhala wofalitsa

3

34-47

Kukambirana zimene Mulungu amafuna kuti anthu omwe amamulambira azichita

Kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa

4

48-60

Kuphunzira zimene mungachite kuti Mulungu apitirize kukukondani

Kuphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu