INDONESIA
Abale Ankalengeza za Yehova Molimba Mtima
Kwa zaka zambiri pamene ntchito ya a Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Indonesia, abale ankayesetsa kutsatira malangizo amene Yesu anapereka akuti, “khalani ochenjera ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.” (Mat. 10:16) Boma litalolanso ntchito yathu, abale ambiri ankafunika kuphunzitsidwa kuti azilalikira “molimba mtima.”—Mac. 4:31.
Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena sankafuna kulalikira kunyumba ndi nyumba, koma ankangopita ku maulendo obwereza komanso kukachititsa maphunziro a Baibulo. Enanso ankaopa kulalikira Asilamu, ndipo akafunsidwa kuti ali m’chipembedzo chanji, sankayankha kuti ndi a Mboni za Yehova koma ankangonena kuti ndi Akhristu. Ambiri ankakonda kugwiritsa ntchito Mabaibulo ena m’malo mogwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano * la Chiindoneziya. Ndipo ena ankakana kugawira anthu mabuku, magazini, timapepala komanso zinthu zina.
Mavuto amenewa anayamba pamene ntchito yathu inali yoletsedwa ndipo anapitirirabe ntchito yathu itavomerezedwa. Abale ndi alongo ankachitanso zimenezi chifukwa cha chikhalidwe cha m’dzikoli. Anthu ambiri m’dzikoli, amaona kuti akasiyana maganizo ndi munthu wina, si bwino kutsutsana naye komanso safotokoza maganizo awo momasuka. Ndiye kodi zikanatheka bwanji kuti abalewa asinthe n’kuyamba kulalikira mopanda mantha?
Yehova anathandiza abalewa kudzera mwa abale okhwima mwauzimu. Abalewa ankalangiza mwachikondi onse amene ankachita mantha akamalalikira. (Aef. 4:11, 12) Mwachitsanzo mu 2010, M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira, analimbikitsa abale kuti azilengeza dzina la Mulungu kwa anthu onse pogwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano. Mmishonale wina, dzina lake Misja Beerens, anati: “Nkhani imene M’bale Lett anakamba, inathandiza kwambiri ofalitsa kuti asamachite mantha akamalalikira. Inawathandizanso kuti asamaope kuuza ena kuti ndi a Mboni za Yehova komanso kuti azithandiza anthu ena kudziwa zimene Baibulo limanena.”
Asilamu ambiri a ku Indonesia amaganiza kuti a Mboni za Yehova ali m’gulu la matchalitchi achikhristu. Choncho pofuna kuthandiza abale kuthana ndi vuto limeneli, Utumiki wa Ufumu wina unanena kuti: “Ndi bwino kuuza anthu zoti ndife a Mboni za Yehova tikangoyamba kuyankhula nawo. . . . Ndife atumiki a Yehova ndipo tiyenera kuthandiza anthu onse a m’dziko lathu kudziwa dzina lake komanso zimene akufuna kudzachitira anthu m’tsogolo.” M’bale wina yemwe amatumikira pa ofesi ya nthambi, dzina lake Shinsuke Kawamoto, anati: “Kutsatira malangizo amenewa kukuthandiza chifukwa Asilamu ambiri akufuna kudziwa kuti a Mboni za Yehova ndi ndani kwenikweni. Akufuna kudziwa kuti timasiyana bwanji ndi matchalitchi achikhristu ndipo zimenezi zikutipatsa mwayi wowalalikira mosavuta.”
Abale ndi alongo analimbikitsidwanso kuti azigawira magazini ambiri a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! M’bale Lothar Mihank, yemwe ndi wogwirizanitsa ntchito za Komiti ya Nthambi, anati: “Kuti anthu atidziwe bwino ayenera kuwerenga magazini athu. Magaziniwa amachititsa anthu kuti azifuna kudziwa zambiri za ifeyo ndiponso kuti azitilandira bwino tikamawalalikira. Ndiye tikamawagawira magaziniwa, timawapatsa mwayi woti nawonso aphunzire za Yehova.”
Kulalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri N’kothandiza
Mu 2013, ofesi ya nthambi ya ku Indonesia inakhazikitsa njira zatsopano ziwiri zomwe abale a m’Bungwe Lolamulira anavomereza kuti tizigwiritsa ntchito polalikira. Njira yoyamba ndi dongosolo lapadera lolalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndipo njira yachiwiri ndi dongosolo la mpingo lolalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Njirazi zikuthandiza anthu ambiri a ku Indonesia kuti amve uthenga wabwino.
Amodzi mwa malo oyambirira omwe abale anakhazikitsa kuti azigwiritsa ntchito njira yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri, anali pamalo ena ogulitsira zipangizo zamakono ku West Jakarta. Kenako mipingo inayamba kulalikira m’gawo lawo pogwiritsa
ntchito timashelefu tamatayala komanso matebulo. Pamene chaka chinkatha, n’kuti abale m’dziko la Indonesia akugwiritsa ntchito matebulo komanso timashelefu topitirira 400. Kodi kulalikira pogwiritsa ntchito njirazi kwathandiza bwanji?M’bale wina, yemwe ndi mkulu mumpingo wina wa ku Jakarta, dzina lake Yusak Uniplaita, anati: “Tisanayambe kulalikira pogwiritsa ntchito njirazi, mpingo wathu unkaitanitsa magazini 1,200 okha pa mwezi. Koma patangotha miyezi 6, tinayamba kuitanitsa magazini okwana 6,000 pa mwezi. Panopa timaitanitsa magazini okwana 8,000. Komanso timagawira mabuku ndi timabuku tambiri.” Apainiya ena a mumzinda wa Medan ku North Sumatra, anayamba kulalikira pogwiritsa ntchito timashelefu tamatayala m’malo ena atatu komwe kumapezeka anthu ambiri. M’mwezi woyamba, apainiyawa anagawira mabuku okwana 115 komanso magazini pafupifupi 1,800. Pamene miyezi iwiri inkatha, apainiya 60 omwe anali m’malo osiyanasiyana 7, anagawira mabuku 1,200 komanso magazini okwana 12,400. Mmishonale wina, dzina lake Jesse Clark, anati: “Abale ndi alongo akusangalala kwambiri kulalikira pogwiritsa ntchito njira zatsopanozi. Zikuonekeratu kuti ntchito yolalikira ipita patsogolo kwambiri m’dziko la Indonesia. Kulalikira pogwiritsa ntchito njirazi n’kosangalatsa kwambiri ndipo tipitirizabe kuzigwiritsa ntchito.”
Anthu Akumva Uthenga Wabwino M’chinenero Chawo
Dziko la Indonesia ndi limodzi mwa mayiko omwe kuli zinenero zochuluka kwambiri padziko lonse lapansi. * Anthu ambiri a m’dzikoli amayankhula Chiindoneziya. Komabe pali enanso ambiri omwe amayankhula zinenero zina.
Mu 2012, abale a ku ofesi ya nthambi ya ku Indonesia, anachita kafukufuku kuti adziwe ngati n’kofunika kuyamba kumasulira mabuku athu m’zinenero zina. M’bale Tom Van Leemputten anati: “Tinayamba kumasulira mabuku athu m’zinenero 12, zomwe anthu pafupifupi 120 miliyoni amayankhula. Chimodzi mwa zinenerozi chinali Chijava. Abale omwe amamasulira mabuku athu m’Chijava, anagwetsa misozi chifukwa cha chisangalalo ataona
kapepala koyambirira komwe anamasulira. Anasangalala chonchi chifukwa anaona kuti tsopano uthenga wabwino wayamba kupezeka m’chinenero chawo.”Mipingo yambiri ya ku Indonesia inapitirizabe kuchita misonkhano m’Chiindoneziya ngakhale kuti m’madera amene amakhalawo, anthu ambiri amayankhula zinenero zina. M’bale Lothar Mihank anati: “Mu 2013, ine ndi mkazi wanga Carmen, tinakachita msonkhano wa masiku awiri pachilumba cha Nias ku North Sumatra. Pamsonkhanowo panali anthu 400 ndipo ambiri ankayankhula Chiniyasi. Tsiku loyamba nkhani zonse zinakambidwa m’Chiindoneziya. Ndiyeno ndinafunsa abale omwe ankafunika kukamba nkhani tsiku lotsatira ngati angakwanitse kukamba nkhani m’Chiniyasi. Atavomera, tinalengeza kuti nkhani za tsiku lotsatiralo zidzakambidwa m’Chiniyasi. Zimenezi zinachititsa kuti anthu oposa 600 abwere tsiku lotsatira moti holo imene tinkachitira msonkhanowo inadzadza kwambiri.” Nayenso mkazi wake Carmen anati: “Zinkachita kuonekeratu kuti tsiku
lachiwirilo, anthu onse akumvetsera kwambiri nkhanizo m’Chiniyasi poyerekeza ndi tsiku loyamba lomwe zinali m’Chiindoneziya. Anthuwo ankasangalala kumvetsera uthenga wa m’Baibulo m’chinenero chimene amachimva bwino.”Nawonso anthu omwe ali ndi vuto losamva, ali ndi mwayi wophunzira Baibulo m’chinenero chawo. Kuyambira mu 2010, omasulira mabuku m’chinenero chamanja cha ku Indonesia, anamasulira timabuku 7 komanso timapepala 8 ta m’chinenerochi. Kuwonjezera pamenepa, ofesi ya nthambi inavomereza kuti pachitike makalasi 24 ophunzitsa anthu chinenero chamanja, ndipo anthu opitirira 750 analowa nawo makalasiwa. Panopa ku Indonesia kuli mipingo ndi magulu okwana 23 omwe amalalikira anthu pafupifupi 3 miliyoni amene ali ndi vutoli.
Panopa, omasulira mabuku ku Indonesia amamasulira mabuku m’zinenero 37 za m’dzikoli. Omasulirawa alipo 117 komanso pali anthu ena 50 omwe amawathandizira. Anthu onsewa amagwira ntchito yomasulirayi m’madera okwana 19.
^ ndime 2 Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu la Chiindoneziya, linatulutsidwa mu 1999. Abale anamasulira Baibuloli pa nthawi imene ntchito yathu inali yoletsedwa ku Indonesia ndipo anagwira ntchitoyi kwa zaka 7. Patatha zaka zingapo, mavoliyumu awiri a Insight on the Scriptures ndiponso Watchtower Library ya pa CD, zinatulutsidwa m’Chiindoneziya. Kunena zoona abale amenewa anagwira ntchito yotamandika zedi.
^ ndime 2 Ku Indonesia kuli zinenero 707 ndipo ku Papua New Guinea, dziko lomwe lili chakum’mawa pafupi ndi dziko la Indonesia, kuli zinenero 838.