Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

INDONESIA

Anachita Upainiya Wapadera kwa Zaka 50

Alisten Lumare

Anachita Upainiya Wapadera kwa Zaka 50
  • CHAKA CHOBADWA 1927

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1962

  • MBIRI YAKE Poyamba anali mkulu wa apolisi koma anakhala mpainiya wapadera kwa zaka zoposa 50.

MU 1964, ndinaikidwa kukhala mpainiya wapadera pachilumba cha Manokwari ku West Papua. Mpingo womwe unali pachilumbachi unkatsutsidwa kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo. Nditangofika kumene, m’busa wina watchalitchi chachipulotesitanti anafika kunyumba kwanga atakwiya.

Iye anayankhula mwaukali kuti: “Ndigwetsa nyumba yakoyi komanso ndithetsa gulu la Mboni za Yehova ku Manokwari kuno.”

Chifukwa cha zimene ndinaphunzira ndili wapolisi, sindinachite mantha ndi zimene ananenazo. Ndinamuyankha mwaulemu ndipo ananyamuka n’kumapita.—1 Pet. 3:15.

Nthawi imeneyo ku Manokwari kunali ofalitsa 8 okha basi. Panopa padutsa zaka pafupifupi 50 ndipo tsopano kuli mipingo yokwana 7. M’chaka cha 2014, anthu oposa 1,200 anapezeka pamsonkhano womwe unachitika m’derali. Ndikaona mmene Yehova wathandizira anthu m’dera lakumudzi limeneli, ndimasangalala kwambiri.