Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 2)

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 2)

Kulimbana ndi Anthu Otsutsa

Atsogoleri achipembedzo a ku Freetown ataona kuti anthu awo akukonda nkhani za M’bale Brown anayamba kuchita nsanje ndipo anakwiya kwambiri. Mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1923, munali mawu akuti: “Atsogoleri a zipembedzo akugwiritsa ntchito nyuzipepala ngati chibonga potsutsa choonadi. M’bale Brown wakhala akuwayankha ndipo olemba nyuzipepala akulembanso mfundo zake.” Atsogoleriwo anafika posowa chonena ndipo zinadziwika kuti ankanena zabodza. Mfundo za choonadi cha m’Baibulo zinafalitsidwa kwambiri moti anthu ankhaninkhani owerenga nyuzi ankapempha mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Atsogoleriwa ankafuna kusokoneza anthu a Mulungu koma Yehova ‘anawabwezera zoipa zawo.’—Sal. 94:21-23.

Achinyamata ena amene anali mbali ya atsogoleriwo analengeza zoti achititsa misonkhano yotsutsa uthenga wa Ufumu umene ankautcha kuti “uthenga wa anthu otsatira Russell.” Ndiyeno M’bale Brown ananena mu nyuzipepala kuti akufuna kuti pakhale mtsutso pa nkhaniyi. Koma achinyamatawo anakana ndipo analusira mkonzi wa nyuzipepala amene analemba zimenezi. Anauzanso M’bale Brown kuti asadzapezekenso pa misonkhano yawo moti Alfred Joseph ndi amene ankapita.

Misonkhanoyi inkachitikira kutchalitchi cha Methodist chotchuka ku Freetown chotchedwa Buxton Memorial Chapel. Alfred anati: “Pa nthawi ya mafunso, ndinafunsa atsogoleri a chipembedzo cha Anglican za Utatu komanso ziphunzitso zina zabodza. Kenako tcheyamani anangonena kuti pasakhalenso aliyense wofunsa mafunso.”

Pa gulu la achinyamata otsutsa aja amene analipo usikuwo panali Melbourne Garber yemwe anali atamvetsera nkhani za “Baibulo” Brown. Iye ndi amene ananena kuti, “Komatu a Brown amalidziwa bwino Baibulo.” Gerber  ataganizira bwinobwino zimene anamva anazindikira kuti wapeza chipembedzo choona. Ndiyeno anapempha M’bale Brown kuti azimuphunzitsa Baibulo. M’baleyo anamuitanira ku Phunziro la Nsanja ya Olonda lomwe linkachitikira kunyumba kwake. Achibale ake ankamutsutsa kwambiri koma iye sanabwerere m’mbuyo moti pasanapite nthawi anabatizidwa limodzi ndi anthu ena.

Apatu Satana analephera kusokoneza ntchito yolalikira imene inali itangoyamba kumene. Ndiyeno meya wa mzinda wa Freetown anauza achinyamata otsutsawo kuti: “Ngati ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali. Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu, simungathe kuwaletsa.”—Mac. 5:38, 39.

Chipembedzo cha a Brown

Chakumayambiriro kwa mwezi wa May, mu 1923, M’bale Brown anapempha mabuku ku ofesi ya nthambi ya ku London. Pasanapite nthawi yaitali kunafika mabuku 5,000. Pambuyo pake kunabweranso mabuku ena. M’baleyu ankachititsanso msonkhano wa onse ndipo anthu ambiri ankabwera kudzamvetsera.

Ndiyeno magazini ina ya Nsanja ya Olonda ya chaka chomwechi inanena kuti: “Ntchito yolalikira yakula kwambiri [ku Sierra Leone] moti M’bale Brown wapempha thandizo. Panopa M’bale Claude Brown wa ku Winnipeg, yemwe poyamba ankakhala ku West Indies, wanyamuka kale kuti akamuthandize.”

M’bale Claude Brown anali atasonyeza kale kuti ndi wokhulupirika pa ntchito yolalikira uthenga wabwino. Iye anakana kulowerera nkhondo yoyamba yapadziko lonse, moti anazunzidwa kwambiri m’ndende za ku Canada komanso ku England. M’baleyu anatumikira ku Sierra Leone kwa zaka 4 ndipo ankalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo.

Mlongo wina dzina lake Pauline Cole anati: “Ndisanabatizidwe mu 1925, M’bale Claude anandifunsa mafunso.

 “Anandifunsa kuti: ‘Mlongo Cole, kodi zimene mwaphunzira m’buku lakuti Studies in the Scriptures mwazimvetsa bwinobwino? Sitikufunatu kuti mudzasiye choonadi chifukwa chakuti simunamvetse zimene Baibulo limaphunzitsa.’

“Poyankha, ndinati: ‘M’bale Claude, buku limeneli ndaliwerenga mobwerezabwereza ndipo ndasankha kutumikira Mulungu.’”

Pauline Cole

Pauline anatumikira Mulungu kwa zaka zoposa 60 ndipo anali mpainiya wapadera kwa zaka zambiri. Mlongoyu anamaliza utumiki wake padziko lapansi mu 1988.

William “Baibulo” Brown ankafunitsitsanso kuthandiza anthu kukhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu. Pa nkhani imeneyi, Alfred Joseph anati: “Ndikakumana ndi M’bale Brown m’mawa uliwonse, ankakonda kunena kuti: ‘Mwadzuka bwanji M’bale Joe? Kodi lemba la tsiku la lero likuti bwanji?’ Ndikalephera kuyankha ankandiuza kuti  ndiziwerenga kabuku kakuti Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku kuti ndizidziwa lemba la tsiku lililonse. [Kale kabukuka kankatchedwa Daily Manna.] Choncho ndinkaoneratu lemba kuti asandichititse manyazi. Poyamba zimenezi sizinkandisangalatsa koma kenako ndinaona ubwino wake.”

Kunena zoona M’bale Brown anandithandiza kwambiri. Mu 1923, mpingo unakhazikitsidwa ku Freetown ndipo anthu 14 anabatizidwa. M’bale wina amene anabatizidwa anali George Brown ndipo izi zinachititsa kuti mumpingomo mukhale mabanja atatu a a Brown. Khama la mabanja atatuwa linachititsa kuti anthu a ku Freetown azinena Ophunzira Baibulo kuti ndi anthu a chipembedzo cha a Brown.