SIERRA LEONE NDI GUINEA
Kusiya Usilikali N’kuyamba Upainiya Wokhazikika
NDINAYAMBA usilikali ndili ndi zaka 16, zigawenga zitandikakamiza kuti ndiyambe kumenya nawo nkhondo. Iwo ankandipatsa mowa komanso mankhwala osokoneza bongo moti nthawi zambiri ndinkakamenya nkhondo nditamwa mankhwala osokoneza bongo. Ndinamenya nkhondo zambiri ndipo ndinkawachitira anthu nkhanza zoopsa. Ndimamva chisoni kwambiri ndikakumbukira zimene ndinkachitazi.
Tsiku lina wa Mboni wina wachikulire anabwera kudzalalikira pamalo omwe tinkakhala. Popeza kuti anthu ambiri ankatiopa ndipo sankatikonda, ndinaona kuti wa Mboniyu anatiganizira ndipo ankafuna kutithandiza mwauzimu. Choncho atandipempha kuti ndipite ku misonkhano yawo ndinavomera. Sindikukumbukira zomwe tinaphunzira koma chomwe ndikukumbukira n’chakuti anandilandira bwino kwambiri.
Nkhondo itafika povuta, ndinasiya kukumana ndi a Mboni. Komanso ndinavulala kwambiri ndipo ananditumiza kudera lomwe linali m’manja mwa zigawenga kuti ndikalandire thandizo. Kenako nkhondo itatsala pang’ono kutha, ndinathawira kudera lomwe linali m’manja mwa boma. Ndili kumeneko ndinayamba kugwira nawo ntchito yolimbikitsa anthu kuti asiye usilikali, asiye kugwiritsa ntchito zida za nkhondo komanso yothandiza zigawenga kuti ziyambirenso kugwirizana ndi anthu.
Ndinkamva kuti ndikusoweka zinthu zauzimu. Choncho ndinayamba kupita kutchalitchi cha Pentekosite koma anthu akumeneko anayamba kunditchula kuti ndine Satana. Zimenezi zinandichititsa kuti ndifufuzenso a Mboni za Yehova. Nditawapeza ndinayamba kuphunzira komanso kusonkhana nawo. Ndinawafotokozera zonse zimene ndinkachita m’mbuyomo koma abalewo anandiwerengera mawu olimbikitsa a Yesu akuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. . . . Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”—Mat. 9:12, 13.
Mawu amenewo anandilimbikitsa kwambiri. Ndinkayenda ndi mpeni m’thumba, koma tsiku lina ndinaupereka kwa m’bale amene ankaphunzira nane n’kumuuza kuti: “Ndinkayenda ndi mpeni uwu kuti ndizidzitetezera. Koma popeza ndadziwa kuti Yehova komanso Yesu amandikonda, sindikuufunanso.”
Abalewo anandiphunzitsa kuwerenga ndi kulemba. Patapita nthawi ndinabatizidwa ndipo kenako ndinakhala mpainiya wokhazikika. Masiku ano ndikamalalikira anzanga amene ndinkamenya nawo nkhondo, amandiuza kuti amandilemekeza chifukwa ndinasankha kukhala moyo wosangalatsa Mulungu. Ndinkaphunziranso ndi mtsogoleri wawo.
Pa nthawi yomwe ndinali msilikali ndinabereka ana atatu aamuna. Ndiye nditaphunzira choonadi, ndinkafunitsitsa kuwathandizanso mwauzimu. Ndimasangalala kuti ana anga awiri analola kuphunzira Baibulo. Panopa mwana wanga woyamba ndi mpainiya wothandiza ndipo wina ndi wofalitsa wosabatizidwa.