Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Tinapulumuka M’manja mwa Zigawenga

Andrew Baun

Tinapulumuka M’manja mwa Zigawenga
  • CHAKA CHOBADWA 1961

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1988

  • MBIRI YAKE Pamene nkhondo inkayamba mu 1991, iye anali mpainiya wokhazikika m’tauni ya Pendembu ku Sierra Leone.

TSIKU lina masana, zigawenga zinalowa m’tauni yathu ndipo kwa maola awiri zinali zikungowombera m’mwamba. Ena m’gulu lawolo anali ana moti ankavutika kunyamula mfuti. Anali osasamba, tsitsi lawo linali nyankhalala ndipo ankaoneka kuti amwa mankhwala osokoneza bongo.

Tsiku lotsatira anabweranso n’kuyamba kupha anthu. Ankapha anthu mwankhanza ndipo ena ankawaduladula. Akapeza azimayi ankangowagwiririra. Zinthu zinafika poopsa kwambiri. M’bale Amara Babawo ndi banja lake pamodzi ndi anthu ena 4 amene ankaphunzira Baibulo anathawira kunyumba kwathu. Tonse tinali ndi mantha.

Kenako kunabwera mkulu wa zigawengazo, yemwe anatilamula kuti tsiku lotsatira tipite kuti akatiphunzitse usilikali. Sitinkafuna kulowerera nkhondoyi koma tinkadziwanso kuti tikakana ndiye kuti atipha basi. Tinakhalira kupemphera usiku wonse. Kutacha tinakambirana lemba la tsiku n’kumangodikirira kuti zigawenga zija zibweranso. Koma sizinabwere.

“Inu, mukuwerenga lemba la tsiku? Ndiye kuti ndinu a Mboni eti?”

 Patapita nthawi, kunabwera woyang’anira gulu la zigawenga limodzi ndi asilikali ake 4 ndipo analanda nyumbayo, koma anatiuza kuti tikhoza kumakhala momwemo. Zimenezi zinatithandiza kwambiri chifukwa tinapitiriza kuchita misonkhano komanso kukambirana lemba la tsiku. Asilikali ena akationa ankanena kuti: “Inu, mukuwerenga lemba la tsiku? Ndiye kuti ndinu a Mboni eti?” Sankachita chidwi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa koma ankangotipatsa ulemu basi.

Tsiku lina tinangoona kuti kwabwera bwana wamkulu wa zigawengazo kudzayendera asilikali amene analanda nyumba yangayo. Atafika anapereka ulemu kwa M’bale Babawo n’kumugwira chanza. Kenako anawauza asilikaliwo mokuwa kuti: “Awa ndi abwana anga komanso abwana anu. Muwasamalire chifukwa akangovulala pang’ono, olo tsitsi limodzi likangothothoka m’mutu mwawo kapena mwa anthu enawa, muli m’madzi. Tamvana?” Asilikaliwo anayankha kuti: “Inde bwana!” Bwana wamkuluyo anatipatsa kalata yolamula kuti gulu la Revolutionary United Front lisativulaze chifukwa ndife nzika zamtendere.

Patadutsa miyezi ingapo, magulu a zigawenga anayamba kumenyana okhaokha. Zimenezi zinachititsa kuti tithawire ku Liberia. Tili kumeneko tinakumananso ndi gulu lina la zigawenga. Tinawauza kuti: “Ndife a Mboni za Yehova.” Mmodzi mwa zigawengazo anatifunsa kuti: “Ngati ndinu a Mboni, lemba la Yohane 3:16 limati chani?” Titanena zimene lembalo limanena, anatisiya kuti tizipita.

Kenako tinakumana ndi mkulu wa zigawenga zina yemwe analamula ine ndi M’bale Babawo kuti timutsatire. Poyamba tinkaopa poganiza kuti akufuna kutipha. Koma kenako anatiuza kuti ankaphunzira ndi Mboni za Yehova nkhondoyo isanayambe. Anatipatsa ndalama komanso anatenga kalata yathu n’kukapereka kwa abale a mpingo wapafupi. Patangopita nthawi pang’ono, abale amene tinawalembera kalatawo anabwera ndi zinthu zofunika ndipo anatitengera kumalo ena otetezeka.