SIERRA LEONE NDI GUINEA
Tinkafunitsitsa Kutumikira Yehova
Philip Tengbeh
CHAKA CHOBADWA 1966
CHAKA CHOBATIZIDWA 1997
MBIRI YAKE Anathawa kwawo chifukwa cha nkhondo ndipo anathandiza kumanga Nyumba za Ufumu zokwana 5.
MU 1991, ine ndi mkazi wanga, Satta, tinachoka mumzinda wa Koindu m’dziko la Sierra Leone, pothawa zigawenga zomwe zinabwera mumzindawo. Kwa zaka 8 tinakhala m’makampu osiyanasiyana a anthu othawa kwawo. Tinkavutika ndi njala, matenda komanso tinkakhala ndi anthu amakhalidwe oipa kwambiri.
Tinkati tikafika pakampu, tinkapempha otiyang’anira kuti atipatse malo amene tingamangepo Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina ankatilola koma nthawi zina ankatikaniza. Komabe, tinkayesetsa kupeza malo oti tizisonkhana. Tinkafunitsitsa kutumikira Yehova. Pamapeto pake tinapezeka kuti tamanga Nyumba za Ufumu 4 m’makampu osiyanasiyana.
Nkhondo itatha sitikanathanso kubwerera ku Koindu chifukwa mzindawu unali utawonongeka kwambiri. Choncho, anatitumiza kukampu ya ku Bo. Ofesi ya nthambi inatumiza ndalama zomwe tinagwiritsa ntchito kumanga Nyumba ya Ufumu ya nambala 5.