Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kutsatira Mfundo za m’Baibulo?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kutsatira Mfundo za m’Baibulo?

Mutu 34

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kutsatira Mfundo za m’Baibulo?

Yerekezerani kuti muli ndi atsikana anzanu awiri m’chipinda chodyera kusukulu ndipo mukudya chakudya chamasana. Kenako Brett, mnyamata yemwe wangobwera kumene pasukulupo, akulowa m’chipindamo.

Ndiyeno mmodzi mwa atsikanawo akukuuzani kuti, “Ukudziwa, Brett amakufunatu. Ndimaona mmene amakuyang’anira. Ndikuona kuti wadyerera maso pa iwe.”

Mtsikana winayo akukunong’onezani kuti, “Komanso Brett alibe chibwenzitu.”

Inunso mukudziwa kuti zimene akunenazo n’zoona, chifukwa tsiku lina Brett anakuitanirani kuphwando kunyumba kwawo. Ngakhale kuti munakana, koma pansi pamtima munkafuna mutapita.

Pamene inu mukuganiza zimenezi mnzanu wina uja akukuuzani kuti, “Zangovuta kuti ine ndili ndi chibwenzi kale.”

Ndiyeno akukuyang’anani modabwa ndipo mukudziwiratu zimene akufuna kufunsa.

Iye akuti, “Kodi n’chifukwa chiyani ulibe chibwenzi?”

Funso limeneli mumadana nalo kwambiri. N’zodziwikiratu kuti mumafuna mutakhala ndi chibwenzi. Koma munauzidwa kuti mudikire kaye mpaka mutaona kuti mwafika poti mungathe kukwatiwa. Koma kungoti . . .

Ndiyeno mnzanu wachiwiriyo akunena kuti, “Chifukwa cha chipembedzo chako, eti?”

Mukulankhula chamumtima kuti, ‘Koma ndiye ngati walowa mu mtima mwangatu.’

Iye akulankhula monyoza kuti, “Iwe ndiye umangoganiza za Baibulo basi. Kumasangalalako nthawi zina.”

KODI munanyozedwapo chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo? Ngati ndi choncho, mwina munaganiza kuti mukumanidwa chinachake. Izi n’zimene mtsikana wina dzina lake Deborah anaganizapo. Iye anati: “Ndinkaona kuti mfundo za m’Baibulo n’zopanikiza, ndipo ndinkasirira anzanga chifukwa choti ankachita zomwe akufuna, popanda wowaletsa.”

Muziganizira Zimene Zinachitikira Ena

Ndi bwino kuti tiziphunzirapo pa zolakwa za anthu ena ngati mmene Asafu anachitira. Ndipotu, zimenezi ndi zimene Baibulo limatilimbikitsa kuti tizichita. Panthawi ina, Asafu ankaganiza kuti mfundo za m’Baibulo n’zopanikiza kwambiri. Koma kuganizira zimene zinachitikira anthu amene anasiya kutsatira malamulo a Mulungu kunamuthandiza kwambiri. Ndipo iye anazindikira kuti anthuwo anali “poterera.”—Salmo 73:18.

Kuti tiphunzirepo pa zolakwa za anthu ena, tiyeni tione zimene achinyamata ena ananena. Panthawi ina, iwo anasiya kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo anachita chiwerewere.

Kodi n’chiyani chinakuchititsani kuyamba kuganizira zogonana mpaka kufika pochita chiwerewere?

Deborah: “Kusukulu kwathu aliyense anali ndi chibwenzi ndipo ankaoneka kuti akusangalala. Ndikamacheza ndi anzanga, n’kumawaona akupsompsonana ndi kukumbatirana ndi zibwenzi zawo, ndinkasirira kwabasi ndipo nanenso ndinkafuna nditakhala ndi chibwenzi. Nthawi zambiri ndinkangoganiza za mnyamata winawake yemwe ndinkamufuna. Zimenezi zinandichititsa kufuna kuti ndizingokhala naye pafupi.”

Mike: “Ndinkawerenga mabuku ndiponso kuonera mapulogalamu a pa TV olimbikitsa kugonana. Ndipo kukambirana ndi anzanga nkhani za kugonana kunandichititsa kufuna kudziwa kuti zimakhala bwanji. Ndiyeno, ndikakhala ndi mtsikana kwatokha, ndinkaganiza kuti tingathe kuchita chilichonse koma osagonana naye.”

Andrew: “Ndinkakonda kuonera zithunzi zolaula pa Intaneti. Ndinayambanso kumwa mowa kwambiri. Ndipo ndinkapita ku zisangalalo ndi achinyamata omwe sankatsatira malangizo a m’Baibulo.”

Tracy: “Ndinkadziwa kuti kugonana musanakwatirane n’koipa, koma sindinkadana nako. Ndinalibe maganizo okhala ndi chibwenzi choti ndizigona nacho koma ndinalephera kudziletsa. Nditayamba kuchita zimenezi, kwa kanthawi ndithu chikumbumtima changa sichinkagunda n’komwe.”

Kodi zochita zanuzo zinakuchititsani kukhala osangalala?

Deborah: “Poyamba ndinkaona kuti ndili ndi ufulu ndipo ndinali wosangalala kuti ndikuchita zomwe anzanga amachita. Koma maganizo amenewa sanakhalitse. Ndinayamba kudziona kuti ndine wauve, wakhalidwe loipa, ndipo sindinkasangalala ngakhale pang’ono. Ndinkanong’oneza bondo chifukwa cholephera kudzisunga.”

Andrew: “Pang’ono ndi pang’ono ndinazolowera kuchita zoipa. Komabe, ndinkadziimba mlandu ndipo sindinkasangalala ndi zochita zangazo.”

Tracy: “Moyo wanga wachitsikana unawonongeka chifukwa chochita chiwerewere. Ndinkaganiza kuti ine ndi chibwenzi changa tizisangalala. Koma sizinatero. M’malo mwake, tinkangopsetsana mitima, tinali osasangalala ndipo tinkangokhumudwitsana. Usiku uliwonse ndinkangokhalira kulira, ndipo ndinkadziimba mlandu kuti sindinatsatire malangizo a Yehova.”

Mike: “Ndinayamba kudzimva ngati kuti mbali ina ya thupi langa yafa. Ndinayesetsa kunyalanyaza mmene zochita zanga zinkakhudzira ena, koma sizinatheke. Ndinkavutika maganizo kuona kuti chifukwa chofuna kusangalala ndinakhumudwitsa anthu ena.”

Kodi mungawalangize chiyani achinyamata anzanu amene amaganiza kuti malangizo a m’Baibulo ndi opanikiza?

Tracy: “Muzitsatira malangizo a Yehova ndiponso muzicheza ndi anthu amene amachita zimenezo. Mukamatero mudzakhala wosangalala.”

Deborah: “Kumbukirani kuti zimene mukufuna komanso zochita zanu zimakhudzanso anthu ena. Ndipotu, mukamanyalanyaza malangizo a Mulungu, mumadzipweteka nokha.”

Andrew: “Ukakhala kuti sukudziwa zambiri, ungaone ngati zimene anzako akuchita n’zosangalatsa. Ndiyeno ungatengere zochita zawozo. Choncho, muzisankha mwanzeru anzanu ocheza nawo. Muzikhulupirira Yehova, ndipo simudzanong’oneza bondo.”

Mike: “Kudzisungira ulemu wanu ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene Yehova anakupatsani. Choncho, kulephera kudziletsa n’kupanda nzeru ndipo kumabweretsa mavuto ambiri. Motero, kambiranani ndi makolo anu ndiponso anthu ena achikulire za mavuto anu. Ndipo mukalakwitsa zinthu, musamabise komanso muzikonza zolakwazo mwamsanga. Mukamatsatira malangizo a Yehova, mudzapeza chimwemwe chenicheni.”

Kodi Malangizo a M’Baibulo Amakupherani Ufulu Kapena Amakutetezani?

Yehova ndi “Mulungu wa chisangalalo,” ndipo amafuna kuti inunso muzisangalala. (1 Timoteyo 1:11; Mlaliki 11:9) Malangizo amene ali m’Baibulo ndi oti akupindulitseni. N’zoona kuti nthawi zina mungawaone ngati akukupherani ufulu. Koma kunena zoona, malangizo amenewa ali ngati lamba wa m’galimoto amene amateteza munthu kuti asavulale.

Ndi bwino kuti muzikhulupirira zimene Baibulo limanena. Ndipotu mukasankha kutsatira malangizo ake, Yehova adzasangalala komanso inuyo mudzapindula.—Yesaya 48:17.

M’MUTU WOTSATIRA

Mungathe kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Onani mmene mungachitire zimenezi.

LEMBA LOFUNIKA

“Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula.”—Yesaya 48:17.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ganizirani zimene munganene pofotokozera mng’ono wanu kufunika kotsatira malangizo a m’Baibulo. Kulankhula za chikhulupiriro chanu kungakuthandizeni kwambiri kulimbitsa chikhulupiriro chanucho.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Mungawononge ubwenzi wanu ndi Yehova m’kanthawi kochepa kwambiri, koma zingakutengereni zaka zambiri kuti muukonzenso.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndizimvetsa kufunika kotsatira mfundo za m’Baibulo ndizichita izi: ․․․․․

Ngati nditayamba kusirira anthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo ndidzachita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● Mukaganizira zotsatirapo za kuchita zinthu mosatsatira malamulo a Mulungu, n’chifukwa chiyani simuyenera kudikira kuti mulakwitse chinachake kaye kuti muphunzirepo kanthu?

● Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene Deborah, Mike, Andrew ndi Tracy ananena?

● N’chifukwa chiyani anthu ena angaone kuti malangizo a m’Baibulo amawaphera ufulu, komano kodi n’chifukwa chiyani kuganiza mwanjira imeneyi sikwanzeru?

[Mawu Otsindika patsamba 285]

“Ululu umene munthu umamva ukadzudzulidwa kapena kulangizidwa chifukwa chochita tchimo, umakhala wochepa poyerekezera ndi umene umamva ukabisa tchimolo.”—Anatero Donna

[Chithunzi patsamba 288]

Malangizo a m’Baibulo sakupherani ufulu, koma amakutetezani