Chitsanzo Chabwino—Yobu
Chitsanzo Chabwino—Yobu
Pa nthawi ina, zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wa Yobu. Choyamba, ziweto zake zonse zinafa. Chachiwiri, ana ake onse anamwalira. Chachitatu, anadwala matenda aakulu. Zonsezi zinachitika motsatizanatsatizana komanso modzidzimutsa. Kenako atathedwa nzeru ananena kuti: “Ineyo ndikunyansidwa ndi moyo wanga.” Pofotokoza mmene ankamvera, ananenanso kuti: “Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.” (Yobu 10:1, 15) Ngakhale pamene ankakumana ndi mavuto onsewo, Yobu anakana kuchimwira Mlengi wake. (Yobu 2:10) Mavuto amene anakumana nawo pa moyo wake sanamusinthe. N’chifukwa chake Yobu ali chitsanzo chabwino pa nkhani yopirira.
N’kutheka kuti nanunso mukakumana ndi mavuto mukhoza ‘kunyansidwa ndi moyo wanu.’ Koma potengera Yobu, musalole kuti mavuto amene mukukumana nawo akusintheni n’kuyamba kuchita zinthu mokayikira potumikira Yehova Mulungu. Yakobo analemba kuti: “Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawatcha odala. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa, mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Yehova anathandiza Yobu, inunso adzakuthandizani.