N’chiyani Chingandithandize Kupirira Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Anamwalira?
Mutu 16
N’chiyani Chingandithandize Kupirira Ngati Mayi Kapena Bambo Anga Anamwalira?
Ngakhale kuti nkhaniyi ikunena zimene mungachite ngati mayi kapena bambo anu amwalira, koma mfundo zake zikhoza kuthandizanso ngati wachibale kapena mnzanu wapamtima wamwalira.
“Mayi anga atamwalira, ndinasokonezeka maganizo kwambiri moti sindinkadziwa chochita. Iwo ankathandiza kuti banja lathu likhale logwirizana.”—Anatero Karyn.
CHIMODZI mwa zinthu zopweteka kwambiri pa moyo wa munthu ndi imfa ya mayi kapena bambo ake. Zimenezi zikachitika, mukhoza kuyamba kuvutika maganizo. Brian, yemwe anali ndi zaka 13 pamene bambo ake anamwalira ndi matenda a mtima, ananena kuti: “Titazindikira kuti bambo athu amwalira, tinkangolira basi.” Natalie, yemwe anali ndi zaka 10 pamene bambo ake anamwalira
ndi khansa, anati: “Sindinkadziwa chochita komanso sindinkamva chilichonse.”Anthu amavutika mosiyanasiyana wachibale wawo akamwalira. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “aliyense” ali ndi “mliri wake ndi ululu wake.” (2 Mbiri 6:29) Ndiyeno taganizirani mmene munavutikira maganizo ndi imfa ya mayi kapena bambo anu. Lembani m’munsimu (1) mmene munamvera mutangomva za imfa ya mayi kapena bambo anu ndipo (2) mmene mukumvera panopa. *
1 ․․․․․
2 ․․․․․
Mwina zimene mwayankha zikusonyeza kuti panopa simukumvanso chisoni ngati kale. Zimenezi sizikusonyeza kuti mwayamba kuiwala kholo lanulo. Koma mwina zingachitike kuti panopa mukuvutikabe kapena muli ndi chisoni kwambiri kuposa poyamba. Mwina chisoni chanu chili ngati
mafunde amene amayamba kapena kutha mosayembekezereka. Zimenezi zimachitika ngakhale patapita zaka zambiri makolo anu atamwalira. Koma funso n’lakuti: N’chiyani chingakuthandizeni kupirira ngati mayi kapena bambo anu anamwalira?Mukafuna kulira, lirani. Kulira kumathandiza kuti muchepetseko chisoni. Komabe, mwina mungamve ngati mmene mtsikana wina, dzina lake Alicia, anamvera. Mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 19. Alicia ananena kuti: “Ndinkaona ngati ndikalira kwambiri anthu aona ngati ndilibe chikhulupiriro.” Koma taganizirani mfundo iyi: Yesu Khristu anali wangwiro komanso ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Koma Lazaro yemwe anali mnzake wapamtima atamwalira, Yesu “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:35) Choncho, mukafuna kulira, lirani. Kulira sikutanthauza kuti mulibe chikhulupiriro. Alicia ananenanso kuti: “Kenako ndinalira kwambiri, ndipo ndinkalira tsiku lililonse.” *
Musamadziimbe mlandu. Mtsikana wina dzina lake Karyn, yemwe mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 13, ananena kuti:
“Mayi anga asanamwalire, usiku uliwonse ndinkapita kuchipinda kwawo kukawauza kuti agone bwino. Koma tsiku lina sindinapite kuchipinda kwawo. M’mawa mwake mayi anga anamwalira. Ndimadziimba mlandu kuti sindinapite kukawaona usiku woti amwalira mawa lake komanso chifukwa cha zinthu zina zimene zinachitika m’mawa mwake. Tsiku limene mayi anamwalira, bambo anga anali atapita kukagwira ntchito ndipo pochoka anandiuza ineyo ndi mkulu wanga kuti tiziwasamalira. Koma tinadzuka mochedwa moti mmene ndimapita kuchipinda kwawo, ndinapeza atamwalira. Ndinadziimba mlandu chifukwa nthawi imene bambo ankachoka, n’kuti mayi ali bwinobwino.”N’kutheka kuti nanunso mumadziimba mlandu chifukwa cha zimene munalephera kuchita. Mwina nanunso mumavutika maganizo n’kumanena kuti, ‘mwina ndikanachita zakutizakuti.’ Ngati zimenezi zimakuchitikirani, muzikumbukira mfundo iyi: Mwachibadwa, zinthu zoipa zikachitika anthu amadziimba mlandu akayamba kuganiza kuti mwina akanachita zinazake kuti zinthuzo zisachitike. N’zoona kuti mukanachita zinthu m’njira ina mukanadziwa zimene zichitike. Koma simumadziwa. Choncho, palibe chifukwa chodziimbira mlandu. Si inu amene munachititsa kuti mayi kapena bambo anu amwalire. *
Muzifotokoza mmene mukumvera. Lemba la Miyambo 12:25 limanena kuti: ‘Mawu abwino ndi amene amasangalatsa’ mtima. Choncho mukamangosunga nkhawa zanu mumtima zimakhala zovuta kwambiri kuti chisoni chanu chichepe. Koma mukafotokozera munthu wina mmene mukumvera, akhoza kukuuzani “mawu abwino” omwe angakulimbikitseni.
Muzipemphera. Mosakayikira ‘mukakhuthulira’ Yehova Mulungu “za mumtima mwanu” muzikhala wosangalala. (Salimo 62:8) Sikuti pemphero limangothandiza kuti mumveko bwino. Mukamapemphera mumakhala mukulankhula ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Njira ina imene Mulungu amatitonthozera ndi kudzera m’Mawu ake, Baibulo. (Arma 15:4) Mungachite bwino kusunga malemba amene amakutonthozani. *
Musayembekezere kuti chisoni chanu chingathe lero ndi lero. Koma Baibulo limatitonthoza chifukwa limanena za malonjezo amene Mulungu ananena kuti m’dziko lapansi latsopano “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Inunso mukamaganizira za malonjezo amenewa zidzakuthandizani kuti mupirire imfa ya mayi kapena bambo anu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Ngati simungakwanitse kuyankha mafunso amenewa panopo, mukhoza kudzayankha nthawi ina.
^ ndime 10 Musadzikakamize kulira pofuna kusonyeza kuti muli ndi chisoni. Anthufe timasonyeza chisoni mosiyanasiyana. Koma chofunika kwambiri n’chakuti: Ngati misozi yalengeza, imeneyo ikhoza kukhala “nthawi yolira.”—Mlaliki 3:4.
^ ndime 12 Ngati mukupitirizabe kudziimba mlandu, fotokozerani kholo lanu kapena munthu wina wachikulire mmene mukumvera. Pakapita nthawi, mudzayamba kuona zinthu m’njira yoyenera.
^ ndime 14 Ena amaona kuti malemba otsatirawa amawalimbikitsa: Salimo 34:18; 102:17; 147:3; Yesaya 25:8; Yohane 5:28, 29.
LEMBA
“[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
MFUNDO YOTHANDIZA
Khalani ndi kabuku koti muzilemba zimene mukuganiza zokhudza mayi kapena bambo anu amene anamwalira. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kwambiri kupirira imfa yawo.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Kulira sikusonyeza kuti munthuyo ndi wosalimba mtima. Chifukwa ngakhale anthu olimba mtima ngati Abulahamu, Yosefe, Davide ndi Yesu analira atamva chisoni.—Genesis 23:2; 50:1; 2 Samueli 1:11, 12; 18:33; Yohane 11:35.
ZOTI NDICHITE
Ndikamavutika ndi chisoni ndizichita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa kholo limene lili moyo pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani ndi bwino kuganizira zinthu zosangalatsa zomwe munkachita ndi kholo lanu lomwe linamwalira?
● N’chifukwa chiyani kulemba zimene mukuganiza kungakuthandizeni kupirira imfa ya kholo lanu?
[Mawu Otsindika patsamba 112]
“Sindinkauza munthu aliyense nkhawa zimene ndinali nazo. Mwina zikanakhala bwino ndikanauzako munthu wina.”—Anatero David
[Bokosi/Chithunzi patsamba 113]
CHANTELLE
“Bambo anga anali atadwala kwa zaka 5 ndipo tsiku lililonse matendawo ankawonjezereka. Kenako ndili ndi zaka 16 anadzipha. Zimenezi zitachitika, mayi anga anafotokozera ineyo ndi mchimwene wanga chilichonse chimene chinkachitika. Anatifunsanso maganizo pa nkhani yoyendetsa mwambo wa maliro. Zimenezi zinatithandiza kuti mtima wathu ukhale m’malo. Ndikuganiza kuti ana safuna kuti makolo aziwabisira zinthu zina, makamaka zinthu zazikulu ngati zimenezi. Patapita nthawi, ndinayamba kulankhula momasuka za imfa ya bambo anga. Ndikafuna kulira ndinkangopita malo enaake kapena kwa mnzanga kukalira. Anthu ena ndingawauze kuti: Ngati mukufuna kuuzako munthu wina mmene mukumvera, lankhulani ndi wachibale kapena mnzanu. Ndipo ngati mukufuna kulira, lirani.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 113, 114]
LEAH
“Mayi anga anachita sitiroko ndili ndi zaka 19 ndipo anamwalira patapita zaka zitatu. Atamwalira, ndinkaona kuti ndiyenera kuchita zinthu molimba mtima chifukwa ndikanapanda kutero, bambo anga akanavutika kwambiri. Ndili mwana, mayi anga ankandisamalira ndikadwala kapena ndikakhumudwa ndi chinachake. Ndimakumbukira mmene ndinkamvera Yohane 5:28, 29) Chisoni changa chimachepako ndikaganizira zoti ndidzawaonanso mayi anga komanso ndikamaganizira zimene ndiyenera kuchita kuti ndidzawaone.”
akandigwira kuti adziwe ngati ndikutentha thupi. Nthawi zambiri ndikakumbukira zimenezi ndimawasowa kwambiri. Ndimayesetsa kubisa mmene ndikumvera koma zimenezi n’zosathandiza. Nthawi zina ndikafuna kulira ndimaona zithunzi za mayi anga. Ndimaonanso kuti kucheza ndi anzanga kumandithandiza. Baibulo limanena kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kukhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi. ([Bokosi/Chithunzi patsamba 114]
BETHANY
“Sindikukumbukira nthawi imene ndinauza bambo anga kuti, ‘Ndimakukondani.’ Mwina ndinawauza, koma zikanakhala bwino ndikanakumbukira nthawi imene ndinawauza zimenezi. Anamwalira ndili ndi zaka 5 zokha. Bambo anga anapanga sitiroko ali mtulo ndipo anathamangira nawo kuchipatala. M’mawa mwake ndinangomva kuti amwalira. Zimenezi zitachitika, sindinkafuna kulankhula za bambo anga. Koma patapita nthawi ndinayamba kumasangalala kumva nkhani za bambo anga chifukwa zinandithandiza kuwadziwa bwino. Anthu ena ndingawauze kuti ngati mayi kapena bambo anu anamwalira, muziganizira zinthu zimene munkachitira limodzi komanso muzizilemba kuti musadzaziiwale. Muzichita zonse zomwe mungathe kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba n’cholinga choti mudzaonane nawonso Mulungu akadzawaukitsa m’dziko latsopano.”
[Bokosi patsamba 116]
Zoti Muchite
Lembani Zimene Mukuganiza
Lembani zinthu zosangalatsa zomwe mukukumbukira zokhudza mayi kapena bambo anu. ․․․․․
Lembani zimene mukanakonda kufotokozera mayi kapena bambo anu akadali ndi moyo. ․․․․․
Yerekezerani kuti muli ndi mng’ono wanu amene akuvutika maganizo chifukwa cha imfa ya mayi kapena bambo anu. Lembani zimene mungamuuze kuti mumulimbikitse. (Zimenezi zingathandizenso inuyo kuti muyambe kuganiza bwinobwino.) ․․․․․
Lembani zinthu ziwiri kapena zitatu zomwe mukanakonda kudziwa zokhudza mayi kapena bambo anu amene anamwalirawo. Ndiyeno kambiranani chimodzi mwa zinthu zimenezi ndi kholo lomwe lili ndi moyo. ․․․․․
Werengani Machitidwe 24:15. Kodi zimene lemba limeneli limanena zingakuthandizeni bwanji kupirira imfa ya mayi kapena bambo anu? ․․․․․
[Chithunzi patsamba 115]
Chisoni chili ngati mafunde amene amayamba kapena kutha mosayembekezereka