Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Chizolowezi Choseweretsa Maliseche?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Chizolowezi Choseweretsa Maliseche?

Mutu 25

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Chizolowezi Choseweretsa Maliseche?

“Ndinayamba zoseweretsa maliseche ndili ndi zaka 8. Patapita nthawi ndinadziwa kuti Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. Ndinkadziimba mlandu nthawi iliyonse ndikachita zimenezi moti ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu angakonde munthu wochita khalidwe limeneli?’”​—Anatero Luiz.

WACHINYAMATA akamakula, amafika msinkhu winawake pamene amakhala ndi chilakolako cha mphamvu chofuna kugonana. Zimenezi zimachititsa kuti achinyamata ena ayambe kuseweretsa maliseche. * Ambiri anganene kuti kuchita zimenezi kulibe vuto lililonse chifukwa palibe amene ukumulakwira. Komabe, pali zifukwa zomveka zomwe ziyenera kutichititsa kupewa khalidwe limeneli. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chititsani ziwalo za thupi lanu . . . kukhala zakufa ku . . . chilakolako cha kugonana.” (Akolose 3:5) Kuseweretsa maliseche sikumathetsa chilakolako chofuna kugonana koma kumangochiwonjezera. Komanso ganizirani mfundo zotsatirazi:

● Kuseweretsa maliseche kumalimbikitsa maganizo odzikonda. Mwachitsanzo, munthu akamaseweretsa maliseche amakhala kuti akungoganizira zokhutiritsa zimene thupi lake likufuna.

● Akakhala mwamuna, kuseweretsa maliseche kumam’pangitsa kuona akazi ngati ofunika pogonana pokha. Akazinso amene ali ndi khalidwe limeneli amawaona choncho amuna.

● Kudzikonda kumene munthu amayamba chifukwa choseweretsa maliseche kumam’pangitsa kuti asamadzakhutitsidwe pogonana ndi mwamuna kapena mkazi wake.

M’malo moseweretsa maliseche pofuna kuthetsa chilakolako champhamvu chimene mungakhale nacho, yesetsani kukhala wodziletsa. (1 Atesalonika 4:4, 5) Pofuna kukuthandizani kuchita zimenezi, Baibulo limakulimbikitsani kupewa kuchita zinthu kapena kukhala pamalo amene angakuchititseni kuti mukhale ndi chilakolako chofuna kugonana. (Miyambo 5:8, 9) Koma kodi mungatani ngati munazolowera khalidwe limeneli moti zikukuvutani kusiya? Ngati munayesa kuti musiye khalidwe limeneli n’kulephera, n’zotheka kuyamba kuganiza kuti simungasinthe n’kuyamba kutsatira mfundo zimene Mulungu amafuna. Mnyamata wina, dzina lake Pedro, ankadzionanso choncho. Iye anati: “Ndikayambiranso khalidweli, ndinkavutika kwambiri mumtima mwanga. Ndinkaona kuti Mulungu sangandikhululukirenso moti ndinkakanika kupemphera.”

Ngati nanunso mumamva choncho musataye mtima, n’zotheka kusintha. Achinyamata ambiri, ngakhalenso achikulire, anakwanitsa kusiya chizolowezi choseweretsa maliseche. Nanunso mukhoza kusiya.

Zimene Mungachite Ngati Mumangodziimba Mlandu

Zimene zafotokozedwa m’mbuyomu zikusonyeza kuti nthawi zambiri anthu amene ali ndi chizolowezi choseweretsa maliseche amadziimba mlandu. Kukhala ndi “chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu” kungakuthandizeni kuti muyesetse kusiya khalidwe limeneli. (2 Akorinto 7:11) Komabe si bwino kumangokhalira kudziimba mlandu chifukwa zingakuchititseni kugwa ulesi n’kusiya kulimbana ndi vutolo.​—Miyambo 24:10.

Choncho, yesetsani kumaiona nkhaniyi moyenera. Kuseweretsa maliseche kuli m’gulu la zinthu zonyansa zimene Mulungu amadana nazo. Kukhoza kukuchititsani kukhala “akapolo a zilakolako ndi zosangalatsa zosiyanasiyana,” ndiponso kungakuchititseni kukhala ndi maganizo olakwika. (Tito 3:3) Ngakhale zili choncho, kuseweretsa maliseche sikuli m’gulu la dama loipitsitsa. (Yuda 7) Choncho, ngati muli ndi chizolowezi choseweretsa maliseche musafulumire kuganiza kuti mwachita tchimo limene simungakhululukidwe. Chofunika ndi kuyesetsa kulamulira mtima wanu komanso kupitirizabe kulimbana ndi vutolo.

N’zosavuta kukhumudwa ngati mutayambiranso khalidweli. Zimenezi zikachitika, kumbukirani mawu a pa Miyambo 24:16 omwe amati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso. Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa.” Kulephera kutsatira mfundo inayake kamodzi kokha sikungakupangitseni kukhala m’gulu la anthu oipa. Choncho musafooke. Ganizirani chimene chachititsa kuti muyambirenso khalidwelo ndipo muyesetse kuchipewa kuti musadzachitenso.

Muzipeza nthawi yoganizira mofatsa za chikondi cha Mulungu ndiponso za chifundo chake. Davide, yemwe analemba buku la masalimo, ankalakwitsa zinthu kawirikawiri koma ananena kuti: “Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake, Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:13, 14) Yehova amaganizira zoti anthufe ndi ochimwa n’kale ndipo ndi ‘wokonzeka kutikhululukira.’ (Salimo 86:5) Komabe amafuna kuti patokha tiziyesetsa kukonza vutolo. Ndiye kodi mungachite chiyani kuti musiye chizolowezi choseweretsa maliseche?

Ganizirani zinthu zosangalatsa zimene mumakonda. Kodi mumaonera mafilimu, mapulogalamu a pa TV kapena kutsegula zinthu za pa intaneti zomwe zimakuchititsani kuti mukhale ndi chilakolako chogonana? Wamasalimo anapemphera kwa Mulungu kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.” *​—Salimo 119:37.

Muzidzikakamiza kuganiza zinthu zabwino. Mkhristu wina, dzina lake William, ananena kuti: “Musanagone muziwerenga kaye zinthu zauzimu. Ndi bwino kuti muzigona m’maganizo mwanu muli mfundo za m’Malemba.”​—Afilipi 4:8.

Kambiranani ndi munthu wina za vuto lanulo. Manyazi akhoza kukuchititsani kuti muziopa kumuuza munthu wina za vutoli. Komabe kufotokozera munthu wina kungakuthandizeni kusiya chizolowezi chimenechi. Izi ndi zimene Mkhristu wina, dzina lake David anachita. Iye anati: “Ndinafotokozera bambo anga tili awiri ndipo sindidzaiwala zimene ananena. Anandiuza mawu olimbikitsa akuti: ‘Zimene umachita zimandipangitsa kuti ndizikukonda kwambiri.’ Ndipo ananena mawu amenewa kwinaku akumwetulira. Ankadziwa kuti zinali zovuta kuti ndilimbe mtima kuwafotokozera zimenezi. Zimene anandiuzazi zinandilimbikitsa kwambiri kuti ndiziyesetsa kulimbana ndi vutoli.

“Kenako anandisonyeza malemba angapo amene anandithandiza kudziwa kuti ndikhoza kusintha, komanso ena ondithandiza kudziwa kuipa kwa zomwe ndimachitazo. Atachita zimenezi, anandiuza kuti tidzakambirananso nkhaniyo nthawi ina. Anandiuza kuti ndisadzakhumudwe kwambiri ngati nthawi ina nditakanika kupirira n’kuchitanso khalidweli. Ndidzangoyesetsa kuti papite nthawi yaitali zimenezi zisanachitikenso.” Kodi zimenezi zinamuthandiza bwanji David? Iye anati: “Kuzindikira kuti pali munthu wina amene akudziwa za vuto langa ndipo akundithandiza kunandilimbikitsa kwambiri.” *

M’MUTU WOTSATIRA

Anthu ena amagonana n’cholinga choti angothandizana basi. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake kuchita zimenezi kuli kulakwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Tikamanena za kuseweretsa maliseche sitikutanthauza kukhala ndi chilakolako chofuna kugonana kumene kumatha kuchitika mwachibadwa komanso mosayembekezereka. Mwachitsanzo, nthawi zina mnyamata akhoza kudzuka m’mawa zitamusokonekera polota. Atsikana enanso chilakolako chikhoza kuwapeza mosayembekezereka, makamaka akatsala pang’ono kuyamba kusamba kapena akangomaliza kumene. Tikamanena za kuseweretsa maliseche tikutanthauza kuchita zinthu mwadala zomwe zingakupangitse kumva ngati ukugonana ndi munthu.

^ ndime 15 Kuti mumve zambiri, werengani Mutu 33, m’Buku Lachiwiri.

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri, werengani Buku Lachiwiri tsamba 239-241.

LEMBA

“Thawa zilakolako zaunyamata, koma tsatira chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, ndi mtendere limodzi ndi anthu oitana pa Ambuye ndi mtima woyera.”​—2 Timoteyo 2:22.

MFUNDO YOTHANDIZA

Muzipemphera chilakolako chisanafike poipa. Muzipempha Yehova Mulungu kuti akupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa” imene ingakuthandizeni kupirira mayesero.​—2 Akorinto 4:7.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Munthu amene amalephera kupirira akakhala ndi chilakolako si mwamuna kapena mkazi weniweni. Mwamuna kapena mkazi weniweni amatha kudziletsa, ngakhale akakhala kwa yekha.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndisamaganizire zinthu zoipa ndizichita izi: ․․․․․

Kuti ndisagonje pamene chilakolako chikundivutitsa ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani muyenera kukumbukira kuti Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka”?​—Salimo 86:5.

● Ngati Mulungu, yemwe analenga anthu ndi zilakolako zogonana, amanena kuti tiziyesetsa kudziletsa, ndiye kuti amatikhulupirira kuti tikhoza kuchita chiyani?

[Mawu Otsindika patsamba 182]

“Kuchokera pamene ndinathana ndi vutoli ndimadzimva kuti ndili ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Yehova ndipo sindingalole kuti chilichonse chisokoneze zimenezi.”​—Anatero Sarah

[Chithunzi patsamba 180]

Munthu ukagwa pothamanga sizitanthauza kuti ukufunika kubwerera n’kukayambiranso. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene waseweretsanso maliseche pambuyo poti anasiya khalidwe limeneli. Sizitanthauza kuti zonse zimene wakhala akuyesetsa kuchita m’mbuyomu n’zopanda phindu