Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anyamata Samandifunsira?

N’chifukwa Chiyani Anyamata Samandifunsira?

Mutu 27

N’chifukwa Chiyani Anyamata Samandifunsira?

Amadziwa kuti ndine wotchuka chifukwa ndinamuuzako zoti anyamata ena amandifuna. Ankaseka pamene ndinkamuuza zinthu zopepera zimene anzanga ena amachita. Komanso amadziwa kuti ndine wanzeru chifukwa ndamukonzetsapo zinthu zingapo zimene ananena. Ndikudziwa kuti sipatenga nthawi asanandifunsire.

Mtsikanayu ndi wooneka bwino koma akuoneka ngati alibe nzeru. Amangolankhula yekha osandipatsako mpata woti ndilankhulepo maganizo anga. Ndipo ndikangolankhula chinachake, amandiuza kuti ndalakwitsa. Ndikangomuona ndimalakalaka nditangomuzemba.

KODI mumakhala ndi nkhawa yoti anyamata samakufunani? Atsikana ambiri amakhala ndi nkhawa imeneyi, ngakhale amene mumaona kuti ndi okongola. Mwachitsanzo, taganizirani za Joanne yemwe ndi wooneka bwino, wanzeru komanso wochangamuka. Iye ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimaona kuti anyamata samandifuna. Pali anyamata ochepa amene ineyo ndinkawafuna ndipo nawonso ankaoneka ngati akundifuna koma kenako anasiyiratu kundilankhulitsa.”

Koma kodi n’chiyani chimachititsa kuti mnyamata ayambe kukopeka ndi mtsikana? Nanga ndi atsikana otani omwe sangakopeke nawo? Kodi mtsikana angatani ngati akufuna kuti afunsiridwe ndi mnyamata wabwino?

Zoyenera Kuchita

Dziwani mtima wanu. Muyenera kuti munayamba kukopeka kwambiri ndi anyamata mutangotha msinkhu ndipo mwina munkakopeka ndi anyamata angapo. Zimenezi zimachitika ndipo si zachilendo. Koma ngati mukanangoika maganizo anu onse pa mnyamata woyamba amene munakopeka naye, mukanasokonezeka maganizo komanso moyo wanu wauzimu ukanasokonekera. Zimatenga nthawi kuti munthu afike pokhwima maganizo, ‘asinthe maganizo ake’ n’kuyamba kusankha bwino pa nkhani zofunika kwambiri komanso kuti akwaniritse zolinga zake.Aroma 12:2; 1 Akorinto 7:36; Akolose 3:9, 10.

N’zoona kuti anyamata ambiri amakopeka ndi atsikana amene alibe zolinga zenizeni kapena amene amaoneka ngati osavuta kuwanyengerera. Koma anyamata oterowo amakhala kuti akungofuna kugona ndi mtsikanayo, osati kumukonda ngati munthu. Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti, mnyamata wabwino amafuna mtsikana amene makhalidwe ake abwino angathandize kuti mwamunayonso akhale munthu wabwino.​—Mateyu 19:6.

Zimene anyamata amanena: “Ndimakopeka ndi mtsikana amene amatha kusankha yekha zochita komanso amene amachita zinthu zosonyeza kuti akudziwa zoyenera kuchita.”​—Anatero James.

“Ndikhoza kukopeka ndi mtsikana ngati amafotokoza maganizo ake mwaulemu komanso woti asamangovomera chilichonse chomwe ndanena. Ngakhale atakhala wooneka bwino, sindingasangalale ngati amangonena zinthu zongofuna kundisangalatsa. Mtsikana wotere amandikayikitsa.”​—Anatero Darren.

Kodi mukuganiza bwanji pa zimene anyamatawa ananena?

․․․․․

Muzilemekeza anthu ena. Atsikana amafuna kukondedwa, pomwe anyamata amafuna kulemekezedwa. N’chifukwa chake Baibulo limalangiza amuna kuti azikonda akazi awo koma limati akazi “azilemekeza kwambiri” amuna awo. (Aefeso 5:33) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, kafukufuku wina anasonyeza kuti amuna oposa 60 pa 100 alionse amaona kuti kupatsidwa ulemu n’kofunika kwambiri kuposa kukondedwa. Ndipo azibambo oposa 70 pa 100 alionse ananenanso chimodzimodzi.

Kulemekeza sikutanthauza kuti munthu asamafotokoze maganizo ake ngati ali osiyana ndi a munthu winayo ayi. (Genesis 21:10-12) Koma mmene mungafotokozere maganizo anuwo zingachititse kuti mnyamata akopeke nanu kapena ayi. Ngati nthawi zambiri mumakonda kutsutsa kapena kumukonzetsa zimene wanena, angaone kuti simumamulemekeza. Koma kumvetsera pamene akulankhula komanso kumuyamikira pa zinthu zabwino zimene wanena kungamupangitse kuti avomereze komanso kumvetsera pamene inuyo mukufotokoza maganizo anu. Chinthu chinanso chimene chingamuthandize mnyamata kudziwa ngati muli waulemu ndi kuona mmene mumachitira zinthu ndi abale anu komanso anthu ena.

Zimene anyamata amanena: “Ndimaona kuti anthu akamayamba chibwenzi, chinthu chofunika kwambiri ndi ulemu. Anthuwo ayenera kumalemekezana. Zikatero, chikondi chimayamba chokha kubwera.”​—Anatero Adrian.

“Ngati mtsikana angakwanitse kundilemekeza kapena kundipatsa ulemu, ndiye kuti akhozanso kundikonda mosavuta.”​—Anatero Mark.

Kodi mukuganiza bwanji pa zimene anyamatawa ananena?

․․․․․

Muzivala mwaulemu komanso muzidzisamalira nthawi zonse. Mmene mumavalira komanso kudzisamalira zimasonyezeratu makhalidwe anu komanso mmene mumaganizira. Musanayambe kulankhula ndi mnyamata, zovala zanu zimakhala zitamuuziratu kale kuti ndinu munthu wotani. Ngati mumavala bwino komanso mwaulemu mnyamatayo amadziwa kuti ndinu mtsikana wa makhalidwe abwino. (1 Timoteyo 2:9) Ngati mwavala zovala zoonetsa mbali zina za thupi lanu, mnyamatayo sangavutikenso kudziwa kuti muli ndi makhalidwe enaake oipa.

Zimene anyamata amanena: “Zimene mtsikana amavala zimasonyezeratu mmene amaonera zinthu pa moyo wake. Ngati wavala zoonetsa mbali ina ya thupi lake kapena zosaoneka bwino, ndiye kuti akusakasaka mwamuna woti amufunsire.”​—Anatero Adrian.

“Ndimakopeka ndi mtsikana yemwe amasamalira tsitsi lake, amanunkhira bwino komanso ngati ali ndi timawu tosalala bwino. Nthawi ina ndinakopekapo ndi mtsikana wina wooneka bwino kwambiri koma sizinayende chifukwa anali wauve, sankadzisamalira.”​—Anatero Ryan.

“N’zoona kuti mtsikana akavala zovala zokopa amuna, amakopadi amuna. Koma ameneyo si mtsikana woti ungayambe naye chibwenzi.”​—Anatero Nicholas.

Kodi mukuganiza bwanji pa zimene anyamatawa ananena?

․․․․․

Zimene Simuyenera Kuchita

Musamakope amuna. Mwachibadwa, akazi ali ndi luso lokopa amuna kuti achite zimene akufuna. Akhoza kugwiritsa ntchito luso limenelo kuwakopa kuti achite zinthu zabwino kapena zoipa. (Genesis 29:17, 18; Miyambo 7:6-23) Ngati mutamachita zimenezi ndi mnyamata aliyense amene mwakumana naye, mungamadziwike ndi mbiri yoti mumakopa amuna.

Zimene anyamata amanena: “Kungogundana mapewa ndi mtsikana kukhoza kuchititsa kuti ubalalikiretu. Ndiye ndimaona kuti mtsikana amene amakonda kukugwiragwira mukamacheza amakhala kuti akukukopa.”​—Anatero Nicholas.

“Ngati mtsikana amakonda kugwiragwira mikono ya mnyamata aliyense amene wakumana naye kapena ngati amakonda kuyang’anitsitsa mnyamata aliyense amene wadutsana naye, ndimaona kuti mtsikana ameneyo ndi wokopa amuna ndipo sindingakopeke ndi mtsikana woteroyo.”​—Anatero José.

Musamakakamire anyamata. Mwamuna ndi mkazi akakwatirana, Baibulo limanena kuti amakhala “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Pa nthawi imeneyi, mwamuna ndi mkaziyo amasiya kuchita zinthu zina zimene ankakonda kuchita asanakwatirane ndipo aliyense amayamba kuchita zinthu zosangalatsa mnzakeyo. (1 Akorinto 7:32-34) Koma ngati muli pa chibwenzi, mulibe ufulu woletsa mnyamatayo kuchita zimene akufuna kapena iyeyo kukuletsani inuyo kuchita zimene mukufuna. * Pamenepa mfundo yake ndi yakuti, mukazindikira kuti mnyamatayo ali ndi ufulu wochita zinthu ndi anzake, adzayamba kukukondani kwambiri. Ndipo mmene angagwiritsire ntchito ufulu umenewo zingakuthandizeni kumudziwa bwino kwambiri.​—Miyambo 20:11.

Zimene anyamata amanena: “Ngati mtsikana akufuna kudziwa chilichonse chomwe ndikuchita komanso ngati saganizira zinthu zina koma ine ndekha, mtsikana ameneyo ndi wokakamira.”​—Anatero Darren.

“Ngati ndangodziwana kumene ndi mtsikana, iye n’kuyamba kumanditumizira mameseji pafupipafupi ofuna kudziwa kuti ndili ndi ndani komanso kufuna kudziwa mayina a atsikana amene alipo, ndimaona kuti chimenecho ndi chizindikiro choti ameneyo si mtsikana wolongosoka.”​—Anatero Ryan.

“Mtsikana wokakamira safuna kuti uzicheza ndi anyamata anzako komanso sachedwa kunyanyala ngati sunamutenge kapena kumuitanira kulikonse komwe ukupita. Sindingakopeke ndi mtsikana woteroyo.”​—Anatero Adrian.

Kodi mukuganiza bwanji pa zimene anyamatawa ananena?

․․․․․

Muzidziona Kuti Ndinu Wamtengo Wapatali

Mwina mukudziwapo atsikana ena omwe amalolera kuchita chilichonse kuti mnyamata winawake awafunsire. Ena amasiya makhalidwe awo abwino n’kuyamba makhalidwe oipa kuti angopeza chibwenzi kapena mwamuna woti adzakwatirane naye. Komabe, mfundo yakuti munthu amakolola zimene wafesa imagwiranso ntchito pa nkhaniyi. (Agalatiya 6:7-9) Ngati simumadziona kuti ndinu wamtengo wapatali komanso mumaona kuti mfundo zimene mumatsatira pa moyo wanu sizofunika kwenikweni, amuna amene angakopeke nanu ndi okhawo amene sangakuoneninso kuti ndinu wamtengo wapatali komanso sangaone mfundo zimene mumatsatira kuti ndi zofunika.

Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti, si anyamata onse amene angakufunsireni ndipo zimenezi n’zabwino. Koma ngati mumayesetsa kudzisamalira bwino komanso kukhala ndi makhalidwe abwino, mudzakhala “wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.” Komanso zingachititse kuti mudzafunsiridwe ndi mnyamata wabwino wokuyenererani.—1 Petulo 3:4.

M’MUTU WOTSATIRA

Nanga bwanji ngati ndinu mnyamata ndipo mumadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani atsikana samandifuna?’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 30 Ngati mnyamata ndi mtsikana achita chinkhoswe, aliyense ayenera kuganizira zofuna za mnzake.

LEMBA

“Chikoka chikhoza kukhala chachinyengo ndipo kukongola kukhoza kukhala kopanda phindu, koma mkazi woopa Yehova ndi amene amatamandidwa chifukwa cha zochita zake.”​—Miyambo 31:30.

MFUNDO YOTHANDIZA

Muzipewa kudziphoda kwambiri. Kudziphoda kwambiri kungapangitse anthu ena kuganiza kuti ndinu wonyada kapena mukufuna kukopa amuna.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngati mumafuna zoti nthawi zonse mnyamata azingoganizira za inuyo, mnyamatayo sangafune kukhala nanu pa chibwenzi.

ZOTI NDICHITE

Zinthu zimene ndikuona kuti ndikufunika kusintha ndi ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi mukamacheza ndi mnyamata mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza maganizo ake komanso mmene akumvera?

● Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumadziona kuti ndinu wamtengo wapatali?

[Mawu Otsindika patsamba 190]

“Ndi zoona kuti nthawi zambiri ndimakopeka ndikangoona mtsikana wooneka bwino. Koma chidwi changa sichichedwa kutha ndikangodziwa zoti mtsikanayo alibe zolinga zaphindu. Koma ngati akudziwa zimene akufuna kudzachita pa moyo wake, makamaka ngati wayamba kale kuyesetsa kuti akwaniritse zolinga zakezo, chidwi changa chimawonjezeka.”​—Anatero Damien

[Chithunzi patsamba 191]

Chikondi komanso ulemu zili ngati mateyala awiri a njinga. Onse ndi ofunika kwambiri