N’chifukwa Chiyani Banja la Makolo Anga Linatha?
Mutu 4
N’chifukwa Chiyani Banja la Makolo Anga Linatha?
“Ndikukumbukira tsiku limene bambo anachoka panyumba kuti banja latha. N’kuti ndili ndi zaka 6 zokha ndipo sindinkadziwa kuti chikuchitika ndi chiyani. Ndinkaonera TV ndipo ndinamva mayi akusisima n’kumawachonderera bambo kuti asachoke. Anatuluka kuchipinda atanyamula sutikesi n’kudzagwada pambali panga n’kundipsopsona, kenako anandiuza kuti, ‘Ndimakukonda kwambiri mwana wanga.’ Atatero anatuluka panja ndipo panadutsa nthawi yaitali ndisanawaonenso. Kungoyambira nthawi imeneyo, ndimaopa kuti mayi nawonso angachoke n’kundisiya ndekha.”—Anatero Elaine, wazaka 19.
BANJA la makolo anu likatha mungaone ngati chilichonse chasokonekera ndipo zinthu sizidzakuyenderaninso bwino pa moyo wanu. Zimenezi zingapangitse kuti muzichita manyazi, muzikwiya, muzikhala ndi nkhawa, muziona ngati wolakwa ndi inuyo, muziopa kuti kholo linalonso lingakusiyeni ndiponso mwina mungamafune kubwezera.
Ngati banja la makolo anu latha posachedwapa, n’kutheka kuti zimene tatchula pamwambazi zikukuchitikirani. Ndipo zimenezi n’zomveka chifukwa Mlengi wathu amafuna kuti ana aleredwe ndi makolo onse awiri. (Aefeso 6:1-3) Choncho, bambo kapena mayi akachoka mumawasowa kwambiri chifukwa munkawakonda. Mnyamata wina amene banja la makolo ake linatha ali ndi zaka 7, dzina lake Daniel, ananena kuti: “Ndinkafuna kumachita zinthu ngati bambo anga moti ndinkafuna ndizingokhala nawo. Koma banja litatha tinkakhala ndi mayi anga.”
Zimene Zimachititsa Kuti Banja Lithe
Nthawi zambiri banja likatha ana amadabwa kwambiri chifukwa makolo amakhala kuti sankasonyeza kwa anawo kuti banja lawo lili ndi mavuto. Mtsikana wina yemwe banja la makolo ake linatha ali ndi zaka 15, dzina lake Rachel, ananena kuti: “Ndinadabwa kwambiri chifukwa nthawi zonse ndinkaona kuti amakondana.” Ngakhale m’mabanja amene makolo amachita kuonekeratu kuti amakangana, banja lawo likatha zimakhala zopweteka kwambiri kwa ana.
Nthawi zambiri mabanja amatha chifukwa chakuti munthu mmodzi wachita chigololo. Izi zikachitika, Mulungu amalola kuti munthu wosalakwayo athetse banjalo n’kukwatiranso. (Mateyu 19:9) Nthawi zina “mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe” zingachititse kuti munthu ayambe nkhanza kwambiri ndipo kholo linalo lingachoke pofuna kuteteza moyo wake komanso wa ana ake. *—Aefeso 4:31.
Koma ndi zoona kuti mabanja ena amatha pa zifukwa zosamveka. Anthu oterewa amangoganizira zofuna zawo ndipo m’malo moti athetse mavuto awo amangothetsa banjalo chifukwa Malaki 2:16) Yesu anasonyezanso kuti banja likhoza kusokonekera ngati mmodzi wakhala Mkhristu.—Mateyu 10:34-36.
choona kuti sakusangalala kapena sakukondananso. Mulungu ‘amadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja’ mwa njira imeneyi. (Kaya banja latha pa zifukwa zotani, ngati makolo sanakuuzeni zifukwazo kapena sakukuyankhani mogwira mtima, umenewu si umboni wakuti sakukondani. Chifukwa chakuti akhumudwa kwambiri ndi zimene zachitikazo, makolo anu angalephere kukufotokozerani zimene zachititsa kuti banja lawo lithe. (Miyambo 24:10) Mwinanso akhoza kumaona kuti si nzeru komanso n’zochititsa manyazi kuvomereza kuti onse analakwitsa penapake.
Zimene Mungachite
N’chiyani chimakudetsani nkhawa? Chifukwa chakuti kutha kwa banja la makolo anu kukhoza kusokoneza kwambiri zinthu pa moyo wanu, mungayambe kuda nkhawa ndi zinthu zomwe poyamba simunkada nazo nkhawa. Komabe, mukhoza kuchepetsa mantha anu ngati mutaganizira mofatsa zimene zikukudetsani nkhawazo. Ikani chizindikiro ichi ✔ m’kabokosi kamene kali ndi zinthu zimene zimakudetsani nkhawa kwambiri kapena lembani pa “Zina.”
□ Kholo langa lisiya kundisamala.
□ Sitizipeza ndalama zokwanira kuti tizipeza zinthu zofunika.
□ Ineyo ndi amene ndachititsa kuti banjali lithe.
□ Ndikadzakula banja langa likhozanso kudzatha.
□ Zina ․․․․․
Muzikambirana ndi kholo lanu. Mfumu Solomo inanena kuti pali “nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:7) Choncho yesani kupeza nthawi yoyenera yoti mukambirane ndi makolo anu zinthu zimene zikukudetsani nkhawazo. Afotokozereni mmene kutha kwa banjalo kwakukhudzirani. Mwina akhoza kukufotokozerani zimene zachititsa ndipo zingachepetse nkhawa zanu. Ngati makolo anu akuoneka kuti sakukuthandizani mukhoza kuuzako munthu amene mumamudalira. Yesetsani kupeza munthu wodalirika amene mungamuuze mavuto anu. Kupeza munthu womufotokozera mavuto kungakukhazikeni mtima pansi.—Miyambo 17:17.
Komanso dziwani kuti Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” ndi wokonzeka kumva mavuto anu. (Salimo 65:2) Choncho, muzimuuza nkhawa zanu zonse “pakuti amakuderani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.
Zimene Simuyenera Kuchita
Musamasunge chidani. Daniel, yemwe tamutchula kale uja anati: “Makolo anga ankachita zinthu modzikonda, moti akamachita zinthu sankaganizira mmene zingatikhudzire.” Zimene Daniel ananenazi ndi zomveka ndipo n’kutheka kuti ndi zoona. Koma kodi mungayankhe bwanji mafunso otsatirawa? Lembani mayankho anu m’munsimu.
Kodi Daniel angakumane ndi vuto lanji ngati angapitirizebe kukhala wokwiya? (Werengani Miyambo 29:22.) ․․․․․
Ngakhale kuti ndi zovuta, koma n’chifukwa chiyani zingakhale zothandiza kwa Daniel kukhululukira makolo ake? (Werengani Aefeso 4:31, 32.) ․․․․․
Kodi mfundo ya pa Aroma 3:23 ingathandize bwanji Daniel kuti asamakwiyire makolo ake? ․․․․․
Muzipewa kuchita zinthu zomwe zingakuikeni m’mavuto. Denny ananena kuti: “Banja la makolo anga litatha sindinkasangalala komanso ndinkavutika maganizo. Zinthu sizinkandiyendera bwino kusukulu moti chaka china ndinalephera mayeso. Kenako ndinayamba zibwana ndipo ndinkakonda kuchita ndewu.”
Kodi ukuganiza kuti n’chiyani chinachititsa kuti Denny ayambe kuchita zibwana kusukulu? ․․․․․
N’chifukwa chiyani anayamba kuchita ndewu kawirikawiri? ․․․․․
Ngati muli ndi maganizo oyamba khalidwe loipa n’cholinga choti mukhaulitse makolo anu, kodi mfundo ya pa Agalatiya 6:7 ingakuthandizeni bwanji? ․․․․․
Zomwe Mungayembekezere
Munthu akathyoka pamatenga nthawi yaitali kuti achire bwinobwino. N’zimene zimachitikanso munthu akakhumudwa ndi zinazake. Akatswiri ena amanena kuti kukhumudwa kumene munthu amakhala nako banja likatha kumayamba kuchepa pakadutsa zaka zitatu. Nthawi imeneyi ingaoneke yaitali koma kumbukirani kuti pali zinthu zambiri zimene zingafunike kuchitika kuti moyo wanu ubwererenso mwakale.
Mwachitsanzo, banja likatha zochitika zapakhomo zimasokonekera, choncho mumafunika kusintha zina ndi zina kuti zinthu ziyambirenso kuyenda bwino. Komanso pangadutse nthawi yaitali makolo anu adakali okhumudwa chifukwa cha kutha kwa banjalo. Kukhumudwako kukadzatha m’pamene angayambe kukusamalirani bwinobwino. Komabe, moyo wanu ukayamba kubwereranso mwakale mudzayambiranso kukhala wosangalala.
WERENGANI ZAMBIRI PA NKHANI IMENEYI M’MUTU 25 M’BUKU LACHIWIRI
Kodi mungatani ngati mukuda nkhawa chifukwa choti mayi kapena bambo anu akwatiranso?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 24 m’Buku Lachiwiri.
LEMBA
“Chilichonse chili ndi nthawi yake . . . [ndipo pali] nthawi yochiritsa.”—Mlaliki 3:1, 3.
MFUNDO YOTHANDIZA
Ngati banja la makolo anu linatha, zikhoza kukhala kuti mmodzi kapena onse awiri analakwitsa chinachake. Dziwani zimene analakwitsazo kuti inuyo musadzachitenso zomwezo ngati mungadzakwatire.—Miyambo 27:12.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Mukhoza kudzakhala ndi banja losangalala ngakhale zitakhala kuti banja la makolo anu silikuyenda bwino.
ZOTI NDICHITE
Ndikhoza kufotokoza zinthu zimene zimandidetsa nkhawa kwa (lembani dzina la munthu wodalirika amene mungamuuze nkhawa zanu) ․․․․․
Ndikhoza kuchita zotsatirazi ngati nditayamba kuganiza zoyamba khalidwe loipa n’cholinga choti makolo anga akhaule: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi: ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingapangitse makolo anu kuti asakuuzeni zomwe zachititsa kuti banja lawo lithe?
● Kodi kukumbukira kuti banja latha chifukwa cha mavuto a pakati pa mayi ndi bambo anu osati ndi inuyo, kungakuthandizeni bwanji?
[Mawu Otsindika patsamba 32]
Mayi athu atachoka ndinkakhala wokhumudwa ndipo ndinkakhalira kulira tsiku lililonse. Koma ndinkapemphera pafupipafupi, kuthandiza ena ndiponso ndinkacheza kwambiri ndi anthu olimba mwauzimu. Ndimaona kuti Yehova anandithandiza kupirira kudzera m’njira zimenezi.’’—Anatero Natalie
[Chithunzi patsamba 33]
Kuyambiranso kuchita zinthu bwinobwino pambuyo poti banja la makolo anu latha, kumakhala kopweteka komanso kumatenga nthawi ngati mmene zimakhalira kuti munthu wothyoka mkono achire