Kodi Ndingatani Kuti Kulambira Mulungu Kuzindisangalatsa?
Mutu 38
Kodi Ndingatani Kuti Kulambira Mulungu Kuzindisangalatsa?
Josh, wazaka 16, wangogona pabedi pake. Mayi ake aima pakhomo la chipinda chake ndipo akumuuza mwamphamvu kuti: “Tadzuka iwe. M’mesa kodi lero ndi la misonkhano?” Josh amapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova limodzi ndi makolo ake ndipo banja lawo limapita kumisonkhanoyi mlungu uliwonse. Koma masiku ano, Josh sakumafuna zopita kumisonkhanoko.
Josh akuyankha monyinyirika kuti: “Bwanji ine nditsale pakhomo? Ndatopatu ine.”
Mayi ake akumuuza kuti: “Tangodzuka uzikakonzeka uko iwe. Kuvuta bwanji? Ukufuna undichedwetsenso lero?” Akutembenuka kuti azipita.
Mayi ake asanapite patali Josh akulankhula mokwiya kuti: “Ine sindikufuna zopita kumisonkhano kwanuko. Chipembedzochitu ndi chanu si changa.” Iye wadziwa kuti mayi akewo amva zimene wanenazo chifukwa zikumveka kuti aima. Kenako mayi akewo akupitiriza kuyenda osamuyankha.
Josh wazindikira kuti sanalankhule bwino. Samadziwa kuti mayi ake akhumudwa ndi zimene walankhulazo komabe sakufuna kupepesa.
M’malo mopepesa, Josh akudzuka monyinyirika n’kuyamba kukonzeka kwinaku akudzilankhulira yekha kuti: “Yembekezani, posachedwapa ndiyamba kusankha ndekha zochita. Amene zimawakomera zopita ku Nyumba ya Ufumuwo ndi omwewo, ine ayi. Enafe zopempherazi si kwenikweni.”
KODI inuyo munayamba mwakhalapo ndi maganizo ofanana ndi amenewa? Kodi pena mumaona kuti pamene ena akusangalala ndi zochitika za kumpingo inu mumangochita nawo mokakamizika? Mwachitsanzo:
● Kodi mukamawerenga Baibulo mumamva ngati mukulemba homuweki?
● Kodi simusangalala ndi zolalikira khomo ndi khomo?
● Kodi nthawi zambiri mumaona kuti zochitika za kumisonkhano zimakutopetsani?
Ngati mwayankha kuti inde, musakhumudwe. Mukhoza kuyamba kusangalala potumikira Mulungu. Tiyeni tione zimene zingakuthandizeni.
CHOYAMBA Kuphunzira Baibulo
N’chifukwa chiyani si kophweka? Mwina inuyo simukonda zowerengawerenga. Mukati muwerenge mumapezeka kuti maganizo anu sakhazikika ndipo mumavutika kuti muwerenge kwa nthawi yaitali. Komanso mwina mumaona kuti muli kale ndi zinthu zambiri za kusukulu zoti muwerenge.
Chifukwa chimene muyenera kuphunzirira Baibulo. Tiyenera kuliwerenga chifukwa linalembedwa ndi Mulungu komanso chifukwa chakuti ‘ndi lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.’ (2 Timoteyo 3:16) Kuphunzira Baibulo komanso kusinkhasinkha zimene mwawerengazo kukhoza kukuthandizani kuti mumvetse bwino zinthu zina. Palibe amene angatsutse kuti ngati tikufuna zinthu zabwino komanso zapamwamba tiyenera kuchita khama kuti tizipeze. Mwachitsanzo, ngati munthu amafuna kuti azisewera bwino masewera enaake, ayenera kuphunzira malamulo a masewerawo komanso ayenera kumayeserera pafupipafupi. Ngati munthu akufuna kukhala wathanzi, ayenera kumachita masewera olimbitsa thupi. Ndi mmenenso zilili ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Mlengi wanu, muyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu.
Zimene anzanu amanena. “Ndinafunika kupanga chosankha nditafika ku sekondale. Achinyamata a kusukulu kwathu ankangochita zilizonse zomwe
akufuna, ndi zoipa zomwe. Choncho ndinafunika kuganiza mofatsa kuti: ‘Kodi zimenezi n’zimene nanenso ndikufuna kuchita? Kodi zimene makolo anga amandiphunzitsa ndi zoonadi?’ Ndinafunika kufufuza pandekha mayankho a mafunsowa.”—Anatero Tshedza.“Kuyambira kale ndinkaona kuti zimene ndinkaphunzira ndi zoona, komabe ndinkafunika kupeza umboni pandekha wotsimikizira zimenezi. Ndinkafunika kuti pandekha ndizikonda kulambira Mulungu, osati kumangochita zinthu potsatira zimene makolo anga komanso abale anga akuchita.”—Anatero Nelisa.
Zimene mungachite. Konzani pulogalamu yanuyanu yowerengera Baibulo yogwirizana ndi zinthu zimene zimakusangalatsani. Muyenera kusankha nkhani zimene mukufuna kufufuza. Koma kodi mungayambire pati? Mungayambe ndi nkhani zimene zingakuthandizeni kulidziwa bwino Baibulo komanso zimene zingakuthandizeni kutsimikizira kuti zimene mumakhulupirira ndi zoona. Mukhoza kugwiritsira ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *
Poyambira. Ikani chizindikiro ichi ✔ pa nkhani ziwiri kapena zitatu zimene mukufuna kufufuza kapena lembani m’munsi mwakemo.
□ Kodi Mulungu alikodi?
□ Kodi ndingatsimikize bwanji kuti anthu amene analemba Baibulo anachita kuuzidwadi ndi Mulungu?
□ N’chiyani chimandichititsa kutsimikizira kuti zinthu zinachita kulengedwa osati kusintha kuchokera ku zinthu zina?
□ Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani ndipo ndingadziwe bwanji kuti ndi weniweni?
□ Kodi ndingafotokoze bwanji zimene ndimakhulupirira pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira?
□ N’chifukwa chiyani ndiyenera kukhulupirira kuti anthu akufa adzaukitsidwa?
□ Kodi ndingadziwe bwanji chipembedzo chimene chimaphunzitsa zoona?
□․․․․․
CHACHIWIRI Kugwira Ntchito Yolalikira
N’chifukwa chiyani si kophweka? Kuuza anthu nkhani za m’Baibulo si nkhani yophweka, makamakanso ukakumana ndi mnzako wa kusukulu.
Chifukwa chimene muyenera kulalikirira. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mukaphunzitse anthu . . . , kuti akhale ophunzira anga. . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20) Koma pali zifukwa zinanso. Kafukufuku wina anasonyeza kuti m’madera ena, achinyamata ambiri amakhulupirira Mulungu komanso zimene Baibulo limanena. Komabe, achinyamata sakhulupirira ndi mtima wonse kuti zinthu zidzasintha n’kuyamba kuyenda bwino kutsogoloku. Mukamaphunzira Baibulo panokha, mudzadziwa zinthu zimene achinyamata ambiri amafuna atazidziwa. Ndipo mukamauza anthu ena zimene inuyo mumakhulupirira, mumakhala wosangalala komanso mumasangalatsa mtima wa Yehova, chomwe ndi chinthu chofunika kwambiri.—Miyambo 27:11.
Zimene anzanu amanena. “Ine ndi mnzanga tinakonzekera mawu amene tinganene kuti tiyambe kukambirana ndi munthu mosavuta. Tinakambirananso zimene tingayankhe ngati anthu atayamba kutitsutsa komanso zimene tinganene kwa munthu amene tikukamulalikira kachiwiri. Pamene ndinayamba kuchita khama pogwira ntchitoyi m’pamenenso ndinayamba kuikonda kwambiri.”—Anatero Nelisa.
“Mlongo wina, yemwe ndimasiyana naye zaka 6, ndi amene anandithandiza kuti ndizikonda kwambiri kulalikira. Nthawi zambiri amanditenga kokalalikira komanso nthawi zina timadyera limodzi chakudya cham’mawa. Nthawi ina anandionetsa malemba amene anandithandiza kusintha mmene ndinkaonera ntchito yolalikira. Panopa ndimaona kuti chitsanzo chake chinandithandiza kwambiri kuti nanenso ndizikonda kuthandiza anthu. Ndimamuthokoza kwambiri mlongo ameneyu.”—Anatero Shontay.
Zimene mungachite. Pezani munthu amene makolo anu amuvomereza yemwe ndi wamkulu kwa inuyo woti muzilowa naye muutumiki. (Machitidwe 16:1-3) Baibulo limati: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.” (Miyambo 27:17) Mukhoza kuphunzira zambiri ngati mumacheza ndi anthu achikulire chifukwa amadziwa zambiri. Ndipotu mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Alexis, ananena kuti: “Sindivutika kucheza ndi anthu omwe ndi aakulu kuposa ineyo.”
Poyambira. Kuwonjezera pa makolo anu, lembani dzina la munthu wina wa mumpingo mwanu amene angamakuthandizeni pogwira ntchito yolalikira.
․․․․․
CHACHITATU Kupita Kumisonkhano
N’chifukwa chiyani si kophweka? Zikhoza kukhala zovuta kuti mumvetsere nkhani zonse pambuyo poti mwakhalanso pansi tsiku lonse m’kalasi.
Chifukwa chimene muyenera kupitira kumisonkhano. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane Aheberi 10:24, 25.
pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”—Zimene anzanu amanena. “Ngati mukufuna kuti muzisangalala ndi misonkhano muyenera kukonzekera. Nthawi zina umafunika kuchita kudzikakamiza kuti ukonzekere. Koma umati ukakonzekera, misonkhanoyo imakusangalatsa chifukwa umadziwa nkhani zimene zikukambidwa komanso umatha kuyankhapo.”—Anatero Elda.
“Nditayamba kupereka ndemanga pamisonkhano, m’pamene ndinayambanso kuikonda kwambiri.”—Anatero Jessica.
Zimene mungachite. Muzipeza nthawi yokonzekera misonkhano tsiku la misonkhanolo lisanafike ndipo ngati n’zotheka, muzipereka ndemanga. Kuchita zimenezi kukhoza kukuthandizani kuti muzipindula ndi misonkhanoyo.
Tiyerekezere chonchi: Kodi chingakusangalatseni kwambiri n’chiyani, kuonera mpira pa TV kapena kusewera nawo mpirawo? Ambiri angavomereze kuti amasangalala kwambiri akamasewera nawo kusiyana n’kuti azingoonerera. Mungachite bwino kugwiritsanso ntchito mfundo imeneyi kuti muzisangalala ndi misonkhano yachikhristu.
Poyambira. Lembani m’munsimu nthawi imene mukuona kuti mungamakonzekere misonkhano mlungu uliwonse. Mukhoza kukonzekera kwa mphindi 30 zokha.
․․․․․
Achinyamata ambiri akuona kuti mawu opezeka pa Salimo 34:8 ndi oona. Mawuwa amati: “Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.” Munthu sangasangalale ngati atangomva kuti pali chakudya chokoma kwambiri koma osachilawa. Zingakhale bwino ngati atalawa yekha chakudyacho kuti atsimikizire kuti n’chokomadi. Ndi mmenenso zilili pa nkhani ya kulambira Mulungu. Talawani kuti muone mmene kupezeka pamisonkhano komanso kuchita nawo zinthu zauzimu kumasangalatsira. Baibulo limanena kuti amene amachita, osati wongomva, ndi amene adzakhale “wosangalala.”—Yakobo 1:25.
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukhale ndi zolinga komanso mmene mungazikwaniritsire.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 19 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
LEMBA
“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”—Aroma 12:2.
MFUNDO YOTHANDIZA
Khalani ndi buku loti muzilembamo notsi pamisonkhano. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti musamaone misonkhanoyo kuchedwa komanso kuti mupeze mfundo zambiri zimene zingakuthandizeni.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Si kulakwa kukhala ndi mafunso pa zimene mumakhulupirira komanso kufufuza kuti mudziwe chifukwa chimene mumakhulupirira zimenezo. Ndipotu kufunsa mafunso komanso kufufuza ndi njira yabwino kwambiri yodziwira kuti zimene mumakhulupirira zokhudza Mulungu ndi zoonadi.—Machitidwe 17:11.
ZOTI NDICHITE
Ndizipatula mphindi ․․․․․ zowerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo ndizipatula ․․․․․ mlungu uliwonse kuti ndizikonzekera misonkhano yachikhristu.
Ndizichita zotsatirazi kuti ndizimvetsera ndikakhala pamisonkhano: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani wachinyamata angamaone kuti kuchita zinthu zauzimu n’kosasangalatsa?
● Pa zinthu zitatu zimene takambirana m’mutuwu, n’chiti chimene mukuona kuti mukufunika kusintha?
[Mawu Otsindika patsamba 278]
“Ndine wa Mboni osati chifukwa chakuti makolo anga ndi a Mboni. Mulungu wanga ndi Yehova ndipo sindikufuna kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wanga ndi iyeyo.”—Anatero Samantha
[Bokosi/Chithunzi patsamba 280, 281]
Anadziikira Zolinga
Baibulo limati: “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.” (Yakobo 4:14) Nthawi zina zimachitika kuti munthu amatha kumwalira mwadzidzidzi akadali wachinyamata. Pamene mukuwerenga zimene Catrina ndi Kyle anakumana nazo, onani zimene anachita kuti akhale ndi mbiri yabwino kwa Yehova Mulungu pa nthawi yochepa imene anakhala ndi moyo. Achinyamatawa anadziikira zolinga zauzimu ndipo anayesetsa kuzikwaniritsa.—Mlaliki 7:1.
Catrina anamwalira ali ndi zaka 18, koma ali ndi zaka 13 anali atalemberatu zinthu zimene ankafuna kudzachita pa moyo wake. Zina mwa zolinga zake zinali kudzachita utumiki wa nthawi zonse, kukatumikira kudera limene kukufunika anthu ambiri ophunzitsa Baibulo komanso kugwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi bambo ake. Iye analemba kuti: “Ndinadzipereka kuti ndidzatumikire Yehova Mulungu kwa moyo wanga wonse.” Catrina anali ndi cholinga “chotsatira mfundo za Yehova pa moyo wake komanso kuti azichita zinthu zomusangalatsa.” Pa mwambo wa maliro ake, wokamba nkhani anafotokoza kuti Catrina anali “mtsikana wokongola amene cholinga chake chinali kudzatumikira Yehova kwa moyo wake wonse.”
Kyle anaphunzitsidwa kukhala ndi zolinga kuyambira ali mwana. Ali ndi zaka 20, Kyle anamwalira pa ngozi ya galimoto. Achibale ake anapeza kabuku kamene analembamo zimene ankafuna kudzachita pa moyo wake. Analemba zolingazo ali ndi zaka 4 ndipo mayi ake ndi amene anamuthandiza kulemba. Zolinga zake zinali kubatizidwa, kukamba nkhani ku Nyumba ya Ufumu komanso kupita kulikulu la Mboni za Yehova kukagwira ntchito yopanga mabuku amene amathandiza anthu kuphunzira za Mulungu. Mayi ake ataona kabukuko anati: “Anakwaniritsadi zolinga zonse zimene analemba m’kabukuka.”
Kodi inuyo muli ndi zolinga zotani? Muziyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe chifukwatu chakudza sichiimba ng’oma. Muzigwiritsa ntchito nthawi yanu kuchita zinthu zomwe zingakubweretsereni madalitso, ngati mmene anachitira Catrina ndi Kyle. Muzitsanzira chitsanzo cha mtumwi Paulo yemwe, atatsala pang’ono kumwalira, ananena kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro.” (2 Timoteyo 4:7) Mutu wotsatirawu ukuthandizani kuchita zimenezi.
[Chithunzi patsamba 274, 275]
Ngati mukufuna kukhala wathanzi, muyenera kumachita masewera olimbitsa thupi. Ngatinso mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Mulungu, muyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu