Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

7

Kodi Ndingatani Ngati Wina Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?

Kodi Ndingatani Ngati Wina Akundikakamiza Kuti Ndigone Naye?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Zimene mungasankhe pa nkhaniyi zingakhudze moyo wanu wonse.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tiyerekeze kuti patangodutsa miyezi iwiri kuchokera pamene Hilda anadziwana ndi Mike, anayamba kucheza kwambiri ngati anadziwana kalekale. Ankatumizirana mameseji pafupipafupi ndiponso kucheza pa foni kwa nthawi yaitali. Eniakewo ankangoona kuti zonse zili bwino. Pa miyezi iwiriyo, iwo ankangogwirana manja kapena kukisana pang’ono.

Koma tsiku lina, Mike anayamba kusonyeza kuti akufuna kucheza kwawo kutafika pena. Hilda sankafuna kuchita zimene Mike ankafunazo koma ankaopa kuti akakana chibwenzi chawo chitha. Iye ankamukonda kwambiri Mike chifukwa zimene ankamuchitira zinkamupangitsa kudziona kuti ndi wokongola komanso wofunika. Mumtima mwake ankadziuza kuti, ‘Ine ndi Mike timakondana kwambiri.’

Kodi inuyo mukanakhala Hilda ndipo muli pa msinkhu woti mutha kukhala ndi chibwenzi, mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Kugonana ndi mphatso imene Mulungu anapereka kwa anthu okwatirana. Koma anthu akagonana asanalowe m’banja amakhala kuti akugwiritsa ntchito mphatsoyi molakwika. Zili ngati akutenga malaya okongola amene munthu wina anawapatsa n’kumayeretsera m’nyumba

Munthu akapanda kutsatira lamulo linalake amakumana ndi mavuto. N’zimenenso zingachitike ngati mutapanda kutsatira lamulo la m’Baibulo lakuti: “Mukhale oyera mwa kupewa dama.”—1 Atesalonika 4:3.

Koma kodi munthu amene sangatsatire lamulo limeneli angakumane ndi mavuto otani? Baibulo limanena kuti: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akorinto 6:18) Kodi zimenezi ndi zoona?

Kafukufuku amasonyeza kuti achinyamata ambiri amene amayamba zogonana asanalowe m’banja amakumana ndi mavuto otsatirawa:

  • KUVUTIKA MAGANIZO. Amadziimba mlandu pambuyo pake.

  • KUSAKHULUPIRIRANA. Amayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi amene ndagona nayeyu wagona ndi anthu angati?’

  • KUKHUMUDWA. Atsikana ambiri amafuna mnyamata amene angawateteze, osati kuwadyera masuku pamutu. Anyamata ambiri akagona ndi mtsikana sakopeka nayenso ndipo amayamba kumuona ngati wopanda ntchito.

  • Dziwani izi: Thupi lanu ndi lamtengo wapatali kwambiri. Choncho, mukagona ndi munthu musanalowe m’banja mumakhala kuti mwadzitchipitsa.—Aroma 1:24.

Sonyezani kuti ndinu olimba mtima ndipo mukhoza “kupewa dama.” (1 Atesalonika 4:3) Mukadzalowa m’banja mudzakhala ndi mwayi wogonana popanda kuda nkhawa kapena kudziimba mlandu ngati mmene zimakhalira ndi amene amagonana asanalowe m’banja.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:3.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

  • Kodi munthu amene amakukondanidi angachite zinthu zimene zingakubweretsereni mavuto?

  • Kodi munthu amene amakukondani angakuuzeni kuti muchite zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Mulungu?—Aheberi 13:4.