DOMINICAN REPUBLIC
Panafunika Kumanga Malo Ena Olambirira
Anthu a Mtundu Uliwonse Apulumuke
Cholinga cha Yehova n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) A Mboni za Yehova ku Dominican Republic akhala akuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu chimenechi. Akulalikira pena paliponse ngakhale m’ndende.
Mu 1997 apainiya apadera awiri anapita kundende ya Najayo ku San Cristóbal. Kundendeko anakakumana ndi mtsikana wina wazaka 23 dzina lake Gloria. Mtsikanayu ndi wa ku Colombia ndipo anamangidwa chifukwa chozembetsa mankhwala osokoneza bongo. Iye ankacheza ndi mlongo amene ananamiziridwa zinthu zina n’kumangidwa. Pofuna kuthandiza Gloria kuti apeze mayankho a mafunso ake, abalewo anamupatsa buku lakuti, Kukambitsirana za m’Malemba komanso mabuku ena. Mtsikanayu anachita chidwi kwambiri ndipo izi zinachititsa kuti chiwerengero cha anthu ofuna kuti aziphunzira mlungu uliwonse chiziwonjezeka.
Gloria anasintha kwambiri chifukwa cha zimene ankaphunzira ndipo mu 1999 anavomerezedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Mwezi uliwonse ankalalikira maola oposa 70 ndipo ankaphunzira ndi anthu 6 m’ndende momwemo. Ndiyeno mu 2000, anapempha kuti pulezidenti amukhululukire ndipo zinathekadi chifukwa chakuti anali atasinthiratu. M’chaka chomwechi anamasulidwa n’kubwerera ku Colombia. Iye anabatizidwa mu 2001 ngakhale kuti achibale ake ankadana nazo kwambiri.
Gloria atangobatizidwa anayamba upainiya. Iye anakwatiwa ndi mkulu ndipo onse akuchita upainiya. Iwo anasamukira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri. Gloria wathandiza anthu ambiri kufika podzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. Iye amaona kuti Yehova wamuchitira zambiri ndiye pofuna kumubwezera amaona kuti ndi bwino kuthandizanso anthu ena kuti amudziwe n’kumamutumikira.
Nkhani ya Gloria ikusonyeza kuti ngakhale anthu a kundende akhoza kuphunzira Baibulo n’kusintha. Abale a kunthambi anakambirana ndi akuluakulu a boma oyang’anira ndende kuti awapatse mwayi wokaphunzitsa anthu ambiri m’ndende zosiyanasiyana. Izi zatsegula njira yoti abale 43 ndi alongo 6 apatsidwe mwayi wokaphunzitsa m’ndende 13 za m’dzikoli.
“Talikitsa Zingwe za Hema Wako”
Pamene zinkafika zaka za m’ma 2000, ku Dominican Republic kunali ofalitsa 21,684 m’mipingo 342 omwe ankachititsa maphunziro 34,380. Pa Chikumbutso panafika anthu 72,679. Izi zachititsa kuti a Mboni za Yehova atsatire mawu a Yesaya akuti: “Kulitsa hema wako. Nsalu za hema wako wamkulu zitambasulidwe. Yes. 54:2.
Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za hema wako.”—Vuto limodzi linali loti panalibe Malo a Misonkhano aakulu bwino. Mu 1996, Malo a Msonkhano pafupi ndi nthambi anamalizidwa ndipo anthu a ku Santo Domingo ndi madera ozungulira ankasonkhana pamalowa. Koma malo a ku Villa González, kumene anthu ena onse ankasonkhana sanali bwino ndipo ankafunika kukonzedwa kapena kungomangapo malo atsopano.
Mu 2001, Bungwe Lolamulira linavomereza zoti pamalowo pamangidwe Malo a Msonkhano oti pangasonkhane anthu 2,500. Abale anasangalala kwambiri atamva zimenezi. Panakonzedwanso zoti pamangidwe Sukulu Yophunzitsa Utumiki (imene panopa yalowedwa m’malo ndi Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu). Ananena kuti sukuluyi imangidwe pafupi ndi
Malo a Msonkhanowo ndipo pakhale zipinda zogona, kalasi, laibulale, khitchini ndi chipinda chodyera. Mu 2004, Theodore Jaracz wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yotsegulira malowa. Kuchokera nthawi imeneyo, makalasi 15 amaliza maphunziro awo pasukuluyi.