PHUNZIRO 14
Mabwenzi a Mulungu Amapeŵa Zoipa
Satana amanyengerera anthu kuti achite zinthu zoipa. Munthu amene amafuna kukhala bwenzi la Mulungu ayenera kudana ndi zimene Yehova amadana nazo. (Salmo 97:10) Nazi zina mwa zimene mabwenzi a Mulungu amazipeŵa:
Machimo a chiwerewere. “Usachite chigololo.” (Eksodo 20:14) Kugonana ukwati usanachitike ndi tchimonso.—1 Akorinto 6:18.
Kuledzera. “Oledzera . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:10.
Umbanda, Kuchotsa mimba. “Usaphe.”—Eksodo 20:13.
Kuba. “Usabe.”—Eksodo 20:15.
Kunama. Yehova amadana ndi “lilime lonama.”—Miyambo 6:17.
Salmo 11:5) “Ntchito za thupi [zimaphatikizapo] . . . zopsa mtima.”—Agalatiya 5:19, 20.
Chiwawa ndi Mkwiyo Wopitirira. ‘Yehova adana ndi iye wakukonda chiwawa.’ (Njuga. “Musayanjane ndi . . . wosirira [mwadyera].”—1 Akorinto 5:11.
Chidani chosankhana fuko ndi mtundu. “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.”—Mateyu 5:43, 44.
Zinthu zimene Mulungu amatiuza zimakhala kaamba ka ubwino wathu. Nthaŵi zina kumakhala kovuta kupeŵa zinthu zoipa. Koma ndi chithandizo cha Yehova komanso cha Mboni zake, mukhoza kupeŵa kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo.—Yesaya 48:17; Afilipi 4:13; Ahebri 10:24, 25.