PHUNZIRO 15
Mabwenzi a Mulungu Amachita Zabwino
Pamene muli ndi mnzanu amene mumam’sirira ndi kum’lemekeza, mumayesa kum’tsanzira. Baibulo limanena kuti “Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima.” (Salmo 25:8) Kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenera tikhale abwino ndi owongoka mtima. Baibulo limati: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.” (Aefeso 5:1, 2) Nazi njira zina zochitira zimenezi:
Khalani wothandiza ena. “Tichitire onse chokoma.”—Agalatiya 6:10.
Gwirani ntchito zolimba. “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.”—Aefeso 4:28.
Khalani waukhondo m’thupi ndi m’makhalidwe. “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.”—2 Akorinto 7:1.
Sonyezani chikondi kwa ena. “Tikondane wina ndi mnzake; chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu.”—1 Yohane 4:7.
Mverani malamulo a dziko. “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu [boma] . . . Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho.”—Aroma 13:1, 7.