Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 7

Kodi Mumalemekeza Moyo Ngati Mmene Mulungu Amachitira?

Kodi Mumalemekeza Moyo Ngati Mmene Mulungu Amachitira?

“Inu ndinu kasupe wa moyo.”—SALIMO 36:9.

1, 2. (a) Kodi Mulungu anatipatsa mphatso iti yamtengo wapatali? (b) N’chifukwa chiyani kumvetsa mfundo za m’Baibulo n’kofunika kwambiri masiku ano?

ATATE wathu wakumwamba anatipatsa mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Mphatso imeneyi ndi moyo ndipo anatipatsanso nzeru zimene zimatithandiza kuti tizitha kutengera makhalidwe ake. (Genesis 1:27) Chifukwa cha nzeru zimenezi, timatha kumvetsa mfundo za m’Baibulo. Ndipo tikamagwiritsa ntchito mfundo zimenezi, timakhala anthu okhwima mwauzimu amene amakonda Yehova ndiponso amene ‘aphunzitsa mphamvu zawo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’—Aheberi 5:14.

2 Kumvetsa mfundo za m’Baibulo n’kofunika kwambiri masiku ano, chifukwa m’dzikoli muli mavuto ambiri moti n’zosatheka kukhala ndi malamulo oti tizitsatira pothana ndi vuto lililonse limene tingakumane nalo. Umboni wa zimenezi ndi nkhani ya zamankhwala ndi njira zothandizira odwala pogwiritsa ntchito magazi. Nkhani yokhudza chithandizo choyenera chamankhwala ndi yofunika kwambiri kwa anthu onse amene akufuna kumvera Yehova. Koma tikamvetsa mfundo za m’Baibulo zokhudza nkhaniyi, tingathe kusankha mwanzeru zinthu zimene zingatithandize kukhalabe ndi chikumbumtima chabwino komanso zimene zingatithandize kuti Mulungu apitirize kutikonda. (Miyambo 2:6-11) Tiyeni tikambirane zina mwa mfundo zimenezi.

MOYO NDI MAGAZI N’ZOPATULIKA

3, 4. Kodi ndi nthawi iti pamene Malemba anatchula koyamba kuti magazi ndi opatulika, ndipo zimenezi zikuchokera pa mfundo ziti?

3 Kaini atapha Abele, Yehova anatchula koyamba kuti pali kugwirizana kwambiri pakati pa moyo ndi magazi, komanso kuti zinthu zimenezi n’zopatulika. Mulungu anauza Kaini kuti: “Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.” (Genesis 4:10) Kwa Yehova, magazi a Abele ankaimira moyo wake umene unachotsedwa mwankhanza. Choncho, tingati magazi a Abele ankafuulira Mulungu kuti Mulunguyo abwezere.—Aheberi 12:24.

4 Pambuyo pa chigumula cha Nowa, Mulungu analola anthu kuti azidya nyama koma sanawalole kudya magazi. Mulungu ananena kuti: “Koma musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake. Kuwonjezera pamenepo, ndidzafunsa za magazi anu.” (Genesis 9:4, 5) Lamulo limeneli limakhudza mbadwa zonse za Nowa, kuyambira nthawi imeneyo mpaka masiku athu ano. Ndiponso limatsimikizira zimene Mulungu anauza Kaini kuti magazi amaimira moyo wa nyama ndi anthu. Lamulo limeneli limatsimikiziranso kuti Yehova, amene ndi Kasupe wa moyo, adzaimba mlandu anthu onse amene salemekeza moyo ndi magazi.—Salimo 36:9.

5, 6. Kodi Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwanji kuti magazi ndi opatulika komanso ndi amtengo wapatali? (Onaninso bokosi “ Muzilemekeza Moyo wa Nyama.”)

5 Chilamulo cha Mose chimasonyezanso mfundo yakuti magazi amaimira moyo ndiponso kuti ndi opatulika. Lemba la Levitiko 17:10, 11 limati: “Munthu aliyense . . . akadya magazi alionse, ndidzam’kana ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo. Zili choncho popeza magazi ndiwo amaphimba machimo, chifukwa moyo uli m’magaziwo.” *—Onani bokosi lakuti, “ Magazi Ali ndi Mphamvu Yophimba Machimo.”

6 Ngati magazi a nyama imene yaphedwa sagwiritsidwa ntchito popereka nsembe, magaziwo ankafunika kuthiridwa panthaka. Choncho, zimenezi zinkakhala ngati kuti moyo wabwezedwa kwa Mwiniwake. (Deuteronomo 12:16; Ezekieli 18:4) Komabe, dziwani kuti Aisiraeli akamapha nyama yoti adye, sankafunika kuchita kuonetsetsa kuti magazi onse achokeretu mu nyamayo. Iwo ankangofunika kuzinga ndiponso kukhetsa magazi bwinobwino. Akatero, ankadya nyamayo popanda kutsutsidwa ndi chikumbumtima chawo chifukwa chakuti akakhetsa magazi, ankadziwa kuti achita zinthu zolemekeza Wopereka Moyo.

7. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti ankadziwa kuti magazi ndi opatulika?

7 Davide, “munthu wapamtima [pa Mulungu],” anamvetsa mfundo za lamulo la Mulungu loletsa kudya magazi. (Machitidwe 13:22) Pa nthawi ina Davide ali ndi ludzu kwambiri, amuna atatu anakakamizika kupita kwa adani kukamutungira madzi. Koma atam’bweretsera madziwo iye sanamwe ndipo anafunsa kuti: “Kodi ndimwe magazi a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Davide anaona kuti kumwa madziwo kunali kofanana ndi kumwa magazi a anthuwo, chifukwa anthuwo anaika moyo wawo pachiswe kuti akatunge madziwo. Choncho, ngakhale kuti anali ndi ludzu, iye “anawathira pansi kwa Yehova.”—2 Samueli 23:15-17.

8, 9. Kodi Mulungu anasintha mmene amaonera moyo ndi magazi mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa? Fotokozani.

8 Patapita zaka zoposa 2,400 kuchokera pamene Nowa anapatsidwa lamulo loletsa kudya magazi lija, ndiponso patapita zaka pafupifupi 1,500 kuchokera pamene pangano la Chilamulo linakhazikitsidwa, Yehova anauzira bungwe lolamulira la mpingo wa Akhristu oyambirira kulemba kuti: “Mzimu woyera pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola, ndi dama.”—Machitidwe 15:28, 29.

9 Bungweli linazindikira kuti magazi ndi opatulika ndipo kusawagwiritsa ntchito bwino kunali kofanana ndi kulambira mafano kapena kuchita dama. Akhristu oona masiku ano amatsatiranso mfundo imeneyi. Komanso chifukwa chakuti amatsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo, amasangalatsa Yehova akamasankha zochita pa nkhani zokhudza magazi.

KUGWIRITSA NTCHITO MAGAZI M’ZIPATALA

Kodi ndingamufotokozere bwanji dokotala zimene ndasankha pa nkhani yokhudza kugwiritsa ntchito tizigawo ting’onoting’ono ta magazi?

10, 11. (a) Kodi Mboni za Yehova zimaona bwanji nkhani ya kuthiridwa magazi kapena zigawo zikuluzikulu za magazi? (b) Kodi ndi mbali ziti za magazi zimene Akhristu angasankhe mosiyanasiyana?

10 Mboni za Yehova zimadziwa kuti “kupewa . . . magazi” kumatanthauza kusalola kuthiridwa magazi ndiponso kupereka magazi kwa anthu ena kapena kusunga padera magazi awo kuti apatsidwenso nthawi ina. Komanso pomvera lamulo la Mulungu limeneli, iwo salola kuthiridwa zigawo zikuluzikulu zinayi za magazi, zomwe ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana ndi madzi a m’magazi.

11 Masiku ano, zigawo zikuluzikulu zimenezi zimagawidwanso m’tizigawo ting’onoting’ono timene timagwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Kodi Mkhristu angalandire tizigawo timeneti? Kodi ayenera kuona tizigawo timeneti monga “magazi”? Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha chochita pa nkhani imeneyi. N’chimodzimodzinso ndi njira zina zothandizira wodwala zofuna kugwiritsa ntchito magazi ake omwe popanda kuwasunga padera. Njira zimenezi ndi monga kusefa magazi, kusungunula magazi ndi kupulumutsa maselo a magazi.—Onani Zakumapeto “Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni.”

12. Kodi nkhani zofuna kuti tisankhe tokha chochita tiyenera kuziona bwanji, ndipo tiyenera kuchita chiyani pa nkhani zimenezi?

12 Ngati tikufunika kusankha tokha chochita pa nkhani inayake, kodi ndiye kuti nkhaniyo ndi yaing’ono kwa Yehova? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti iye amadziwa zimene timaganiza ndi zimene zili mumtima mwathu. (Werengani Miyambo 17:3; 24:12.) Choncho tikapemphera ndi kufufuza mosamala za mankhwala kapena chithandizo chinachake, tiyenera kutsatira chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo posankha chochita. (Aroma 14:2, 22, 23) Anthu ena sayenera kutisankhira chochita, ndipo ifeyo sitiyenera kufunsa wina kuti, “Kodi mukanakhala inuyo, mukanatani?” Pa nkhani ngati zimenezi, Mkhristu aliyense ayenera “kunyamula katundu wake.” *Agalatiya 6:5; Aroma 14:12; onani bokosi lakuti, “ Kodi Ndimaona Kuti Magazi Ndi Opatulika?

MALAMULO A YEHOVA AMASONYEZA KUTI IYE NDI ATATE WACHIKONDI

13. Kodi malamulo ndiponso mfundo za Yehova zimasonyeza kuti iye ndi wotani? Perekani chitsanzo.

13 Malamulo ndiponso mfundo za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yehova ndi Wopereka Malamulo wanzeru ndiponso Atate wachikondi amene amafuna kuti ana ake zinthu ziziwayendera bwino. (Salimo 19:7-11) Ngakhale kuti lamulo la “kupewa . . . magazi” limene Mulungu anapereka silinali lokhudza nkhani zaumoyo, limatiteteza ku matenda ena obwera chifukwa chothiridwa magazi. (Machitidwe 15:20) Ndipotu madokotala ambiri amanena kuti opaleshoni yosagwiritsa ntchito magazi ndi njira yatsopano yabwino kwambiri yoperekera chithandizo. Zimenezi zimatsimikizira Akhristu oona kuti Yehova ndi wanzeru zopanda malire ndiponso ndi Atate wachikondi.—Werengani Yesaya 55:9; Yohane 14:21, 23.

14, 15. (a) Kodi ndi malamulo ati amene amasonyeza kuti Mulungu amakonda anthu ake? (b) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo za m’malamulo opewera ngozi amenewa?

14 Malamulo ambiri a Mulungu amasonyezanso kuti iye ankadera nkhawa kwambiri moyo wa anthu ake, Aisiraeli. Mwachitsanzo, iye analamula kuti Aisiraeli azimanga kampanda kuzungulira denga la nyumba zawo kuti apewe ngozi, popeza kuti padengapo ankachitirapo zinthu zambiri. (Deuteronomo 22:8; 1 Samueli 9:25, 26; Nehemiya 8:16; Machitidwe 10:9) Mulungu analamulanso kuti ng’ombe zolusa ziziyang’aniridwa bwino. (Ekisodo 21:28, 29) Munthu akapanda kumvera malamulo amenewa, ankasonyeza kuti sakulemekeza moyo wa ena ndipo zikanachititsa kuti akhale ndi mlandu wa magazi.

15 Kodi mungatsatire bwanji mfundo za m’malamulo amenewa? Mungachite bwino kuganizira za galimoto yanu, mmene mumayendetsera galimotoyo, ziweto zanu, nyumba yanu, malo anu a ntchito ndiponso zosangalatsa zimene mumakonda. M’mayiko ena, achinyamata ambiri amafa pa ngozi zosiyanasiyana. Kawirikawiri zimenezi zimachitika chifukwa chakuti achinyamatawo amachita zinthu mosasamala. Koma achinyamata amene akufuna kuti Mulungu apitirize kuwakonda, amalemekeza moyo ndipo sachita zosangalatsa zimene zingaike moyo wawo pa chiswe. Iwo saganiza mopanda nzeru kuti achinyamata savulala chisawawa. M’malomwake, akamasangalala ndi unyamata, amapewa kuchita zinthu zomwe zingawabweretsere tsoka.—Mlaliki 11:9, 10.

16. Kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti imene imakhudza kuchotsa mimba? (Onaninso mawu a m’munsi.)

16 Ngakhalenso moyo wa mwana amene sanabadwe ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu. Kale ku Isiraeli, munthu akavulaza mayi woyembekezera ndipo ngati mayiyo kapena mwana wosabadwayo wamwalira, Mulungu ankaona kuti wolakwayo ndi wakupha munthu, ndipo ankafunika kuphedwa kuti ‘alipire moyo.’ * (Werengani Ekisodo 21:22, 23.) Ndiye kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji akamaona ana ambirimbiri osabadwa akuphedwa chaka chilichonse pochotsa mimba? Ndipotu ana ambiri amaphedwa mwanjira imeneyi chifukwa makolo awo ndi odzikonda ndipo amakonda chiwerewere.

17. Kodi mungamulimbikitse bwanji munthu amene anachotsapo mimba asanaphunzire malamulo a Mulungu?

17 Nanga bwanji ngati mayi anachotsapo mimba asanaphunzire Baibulo? Kodi ndiye kuti Mulungu sangamuchitire chifundo? Ayi, angamuchitire chifundo. Ndipotu munthu amene walapa moona mtima asakayikire zoti Yehova angamukhululukire pa maziko a magazi amene Yesu anakhetsa. (Salimo 103:8-14; Aefeso 1:7) Ndiponso Khristu ananena kuti: “Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.”—Luka 5:32.

PEWANI KUDANA NDI ANTHU ENA

18. Kodi Baibulo limasonyeza kuti n’chiyani chimene chimapangitsa anthu kuphana?

18 Kuwonjezera pa kupewa kuvulaza anthu ena, Yehova amafuna kuti tizichotsa chidani mumtima mwathu chifukwa chidani ndi chimene chimapangitsa anthu kuphana. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu.” (1 Yohane 3:15) Munthu wotereyu sikuti amangoda m’bale wakeyo koma amalakalaka m’bale wakeyo atafa. Iye angasonyeze kuti amada m’bale wakeyo pomunena miseche kapena kumunamizira kuti wachita zolakwa, zimene zitakhaladi kuti ndi zoona, munthu wonamiziridwayo angalangidwe ndi Mulungu. (Levitiko 19:16; Deuteronomo 19:18-21; Mateyu 5:22) Choncho, n’kofunika kuyesetsa kuchotsa mumtima mwathu maganizo alionse ofunira ena zoipa amene tingakhale nawo.—Yakobo 1:14, 15; 4:1-3.

19. Kodi munthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amaona bwanji malemba ngati Salimo 11:5 ndi Afilipi 4:8, 9?

19 Anthu amene amalemekeza moyo monga mmene Yehova amachitira ndiponso amene amafuna kuti Mulungu apitirize kuwakonda, ayeneranso kupewa chiwawa cha mtundu uliwonse. Lemba la Salimo 11:5 limati: “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” Mawu amenewa sikuti akungonena za khalidwe la Mulungu ayi, koma ndi mfundo imene nafenso tiyenera kutsatira pa moyo wathu. Mawuwa amapangitsa anthu amene amakonda Mulungu kudana ndi zosangalatsa zonse zimene zimalimbikitsa kukonda chiwawa. Popeza Yehova ndi “Mulungu wa mtendere,” amalimbikitsa atumiki ake kuti aziganizira zinthu zachikondi, zabwino, ndiponso zotamandika zimene zimalimbikitsa mtendere.—Werengani Afilipi 4:8, 9.

PEWANI MAGULU AMENE ALI NDI MLANDU WA MAGAZI

20-22. Kodi Akhristu amaziona bwanji zochitika zam’dzikoli, ndipo n’chifukwa chiyani?

20 Mulungu amaona kuti dziko lonse la Satanali lili ndi mlandu wa magazi. Maboma amene m’Malemba amaimiridwa ndi zilombo zolusa, apha anthu mamiliyoni ambiri kuphatikizapo atumiki a Yehova ambirimbiri. (Danieli 8:3, 4, 20-22; Chivumbulutso 13:1, 2, 7, 8) Amalonda ndiponso akatswiri osiyanasiyana a zopangapanga amagwira ntchito mogwirizana ndi maboma okhala ngati zilombo amenewa popanga zida zankhondo zamphamvu kwambiri ndipo amapeza nazo ndalama zambiri. N’zoonadi kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

21 Chifukwa chakuti otsatira a Yesu ‘sali mbali ya dzikoli,’ salowerera ndale kapena nkhondo, amapewa kukhala ndi mlandu wa magazi ndiponso amapewa magulu amene ali ndi mlandu umenewu. * (Yohane 15:19; 17:16) Potsanzira Khristu, iwo sabwezera anthu ena akamawazunza. Koma amakonda adani awo, ngakhalenso kuwapempherera kumene.—Mateyu 5:44; Aroma 12:17-21.

22 Koposa zonse, Akhristu oona amapewa kugwirizana ndi “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga ndipo ndi amene ali ndi mlandu waukulu wa magazi. Mawu a Mulungu amati: “Mwa iye munapezeka magazi a aneneri, a oyera, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” N’chifukwa chake tikuchenjezedwa kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga.”—Chivumbulutso 17:6; 18:2, 4, 24.

23. Kodi kutuluka m’Babulo Wamkulu kumatanthauza chiyani?

23 Kutuluka m’Babulo Wamkulu kumatanthauza zambiri, osati kungofufutitsa dzina lathu ku chipembedzo chonyenga. Kumatanthauzanso kudana ndi zoipa zimene chipembedzo chonyenga chimalekerera kapena chimalimbikitsa monga chiwerewere, kulowa ndale ndiponso kukonda kwambiri chuma. (Werengani Salimo 97:10; Chivumbulutso 18:7, 9, 11-17) Nthawi zambiri zinthu zimenezi n’zimene zimachititsa anthu kuphana.

24, 25. (a) Kodi Mulungu amagwiritsa ntchito chiyani kuti achitire chifundo munthu wokhala ndi mlandu wa magazi amene walapa? (b) Kodi m’Baibulo, zimenezi zinachitiridwa chithunzi ndi chiyani?

24 Tisanayambe kulambira koona, tonsefe tinachita nawo zinthu zina za m’dziko la Satanali, choncho tingati tinali ndi mlandu wa magazi. Komabe, Mulungu anatichitira chifundo ndipo amatiteteza mwauzimu chifukwa chakuti tinasintha khalidwe lathu, timakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu ndiponso tinadzipereka kwa Mulungu. (Machitidwe 3:19) Midzi yopulumukirako yakale imene imatchulidwa m’Baibulo inkachitira chithunzi chitetezo chimenechi.—Numeri 35:11-15; Deuteronomo 21:1-9.

25 Kodi dongosolo limeneli linkayenda bwanji? Kale ku Isiraeli munthu akapha mnzake mwangozi, ankathawira ku umodzi wa midzi yopulumukirako imeneyi. Kumeneko, woweruza woyenera akagamula nkhaniyo, wopha mnzake mwangoziyo ankayenera kukhala kumudzi wopulumukirakowo mpaka mkulu wa ansembe atafa. Kenako anali waufulu kukhala kulikonse kumene ankafuna. Zimenezitu zinasonyeza bwino kwambiri kuti Mulungu ndi wachifundo ndiponso amalemekeza kwambiri moyo wa anthu. Midzi yopulumukirako imeneyi ndi yofanana ndi zimene Mulungu anakonza zotiteteza ku chilango cha imfa chimene chingabwere chifukwa chophwanya mwangozi malamulo a Mulungu okhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi. Iye anachita zimenezi pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Khristu. Kodi mumayamikira zimene Mulungu anachitazi? Nanga mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira? Njira imodzi imene mungachitire zimenezi ndi kuitana ena kuti adzakhale nanu mumzinda wopulumukira wophiphiritsa, makamaka panopa pamene “chisautso chachikulu” chikuyandikira.—Mateyu 24:21; 2 Akorinto 6:1, 2.

MUZILEMEKEZA MOYO POLALIKIRA UTHENGA WA UFUMU

26-28. (a) Kodi zochitika za masiku ano zikufanana bwanji ndi mmene zinalili m’nthawi ya mneneri Ezekieli? (b) Kodi tingatani kuti Mulungu apitirizebe kutikonda?

26 Mmene zinthu zilili ndi anthu a Mulungu masiku ano, zikutikumbutsa mmene zinthu zinalili ndi mneneri Ezekieli. Iye anapatsidwa ntchito ndi Yehova yoti akhale mlonda wopereka machenjezo a Mulungu kwa Aisiraeli. Mulungu anamuuza kuti: “Umve mawu ochokera pakamwa panga ndi kundichenjezera anthuwo.” Ezekieli akananyalanyaza ntchito yakeyi, akanakhala ndi mlandu wa magazi wa anthu amene anaphedwa pamene Yerusalemu ankawonongedwa. (Ezekieli 33:7-9) Koma Ezekieli anamvera Mulungu ndipo analibe mlandu wa magazi.

27 Panopo, mapeto a dziko la Satanali ayandikira kwambiri. Choncho, Mboni za Yehova zimaona kuti kulalikira Uthenga wa Ufumu ndi udindo komanso mwayi wawo wolengeza za “tsiku lobwezera” la Mulungu. (Yesaya 61:2; Mateyu 24:14) Kodi inuyo mumagwira nawo ntchito yofunika imeneyi mokwanira? Mtumwi Paulo ankaona ntchito yake yolalikira kukhala yofunika kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, iye anati: “Ine ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro chonse cha Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri choti titsatire.

28 Komabe, kuti Yehova yemwe ndi Atate wathu apitirizebe kutikonda, pali zinanso zimene tiyenera kuchita kuwonjezera pa kulemekeza moyo ndi magazi monga mmene iyeyo amachitira. Tifunikiranso kukhala oyera pamaso pa Yehova monga tionere m’mutu wotsatira.

^ ndime 5 Pochitira umboni mawu a Mulungu akuti, “moyo wa nyama uli m’magazi,” magazini ina inati: “Mfundo yoti moyo wa nyama uli m’magazi ndi yoona chifukwa selo lililonse la magazi ndi lofunika kuti munthu kapena nyama ikhale ndi moyo.”—Scientific American.

^ ndime 12 Onani Galamukani! ya August 2006, patsamba 3 mpaka 12, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Mabaibulo ena amamasulira lembali m’njira yosonyeza kuti munthu angalandire chilango ngati amene wafa ndi mayi yekha. Komabe, olemba mabuku otanthauzira mawu a m’Baibulo amanena kuti mmene mawuwa analembedwera m’Chiheberi, “zikusonyezeratu kuti sankanena za imfa ya mayi yokha.” Onaninso kuti Baibulo silinena kuti chilango cha Yehova chimenechi chinkaperekedwa potengera kukula kwa mwana wosabadwayo.

^ ndime 70 Kuti mumve zambiri, onani Zakumapeto “Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni.”