Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 4

Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?

Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?

“Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.”—1 PETULO 2:17.

1, 2. (a) Kodi timakhala ndi vuto lanji pa nkhani ya ulamuliro? (b) Kodi tikambirana mafunso otani?

KODI mumaona zimene mwana amachita ngati watumidwa kugwira ntchito inayake imene sakufuna? Amaipitsa nkhope yake. Iye amakhala atamva ndithu zimene makolo ake amuuza, ndipo amadziwa kuti amafunika kuwalemekeza. Koma amangofuna kusawamvera basi. Zimenezi n’zimenenso ambirife timachita.

2 Kulemekeza ulamuliro kumavuta nthawi zambiri. Kodi inuyo nthawi zina zimakuvutani kulemekeza anthu amene akukulamulirani? Ngati ndi choncho, sikuti ndinu nokha amene zimakuvutani. Masiku ano, zikuoneka kuti anthu ambiri salemekeza ulamuliro kuposa mmene zinalili m’mbuyomu. Komabe, Baibulo limanena kuti tiyenera kulemekeza anthu amene ali ndi ulamuliro. (Miyambo 24:21) Ndipotu kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri kuti Mulungu apitirizebe kutikonda. Komabe, m’pomveka kufunsa mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani anthufe zimativuta kwambiri kulemekeza ulamuliro? N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizilemekeza ulamuliro, nanga n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Komanso, kodi tingalemekeze bwanji ulamuliro?

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHUFE ZIMATIVUTA KULEMEKEZA ULAMULIRO?

3, 4. Kodi uchimo ndi kupanda ungwiro zinayamba bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani kupanda ungwiro kumatilepheretsa kulemekeza ulamuliro?

3 Tiyeni tikambirane mwachidule zifukwa ziwiri zimene zimachititsa kuti tizivutika kwambiri kulemekeza anthu amene ali ndi ulamuliro. Choyamba, ndife opanda ungwiro, ndipo chachiwiri, anthu amene ali ndi udindo nawonso ndi opanda ungwiro. Uchimo ndi kupanda ungwiro zinayamba kalekale m’munda wa Edene pamene Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mulungu. Choncho, uchimo unayamba chifukwa cha kusamvera. Kuyambira pamenepo anthufe timabadwa ndi mtima wosafuna kumvera.—Genesis 2:15-17; 3:1-7; Salimo 51:5; Aroma 5:12.

4 Chifukwa choti timabadwa tili ochimwa, n’zosavuta kuti ambirife tikhale onyada ndi odzikuza. Kukhala wodzichepetsa kumativuta ngakhale kuti ndi khalidwe lofunika kwambiri limene tiyenera kuyesetsa kukhala nalo. Ngakhale titatumikira Mulungu kwa nthawi yaitali mokhulupirika, n’zotheka kukhala wodzikweza ndi wonyada. Mwachitsanzo, taganizirani za Kora. Iye anali wokhulupirika ndipo anakumana ndi mavuto ambiri limodzi ndi anthu a Yehova. Komabe, iye ankafunitsitsa udindo ndipo mopanda manyazi anatsogolera anthu kuukira Mose, yemwe anali munthu wofatsa kwambiri kuposa wina aliyense pa nthawiyo. (Numeri 12:3; 16:1-3) Taganiziraninso za Mfumu Uziya. Chifukwa cha kunyada, iye anakalowa m’kachisi wa Yehova n’kukagwira ntchito yopatulika imene inali ya ansembe okha. (2 Mbiri 26:16-21) Anthu amenewa analangidwa koopsa chifukwa cha kusamvera kwawo ndipo sitiyenera kutengera zitsanzo zawo zoipazi. Tiyenera kupewa kunyada, chifukwa ngati tili onyada zingativute kulemekeza ulamuliro.

5. Kodi anthu opanda ungwiro agwiritsa ntchito bwanji mphamvu zawo molakwika?

5 Chinanso n’chakuti, anthu opanda ungwiro amene ali ndi ulamuliro akhala akuchita zinthu zimene zachititsa kuti anthu asamalemekeze ulamuliro. Olamulira ambiri akhala akuchita nkhanza. Ndipotu kuyambira kalekale anthu akhala akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. (Werengani Mlaliki 8:9.) Mwachitsanzo, Sauli anali munthu wabwino ndiponso wodzichepetsa pamene Yehova anamusankha kukhala mfumu. Koma kenako, iye anakhala wonyada ndi wansanje ndipo anazunza Davide yemwe anali munthu wokhulupirika. (1 Samueli 9:20, 21; 10:20-22; 18:7-11) Davide nayenso anadzakhala mfumu yabwino kwambiri mu Isiraeli. Komabe nayenso anagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika. Iye analanda mkazi wa Uriya Mhiti, ndipo kenako anatumiza mwamuna wosalakwayu kunkhondo n’kulamula kuti aikidwe kutsogolo kwa asilikali kuti aphedwe. (2 Samueli 11:1-17) Izi zikusonyeza kuti anthu zimawavuta kugwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo chifukwa cha kupanda ungwiro. Makamaka olamulira ake akakhala kuti saopa Yehova, amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. Katswiri wina wa ndale wa ku Britain, pofotokoza mmene apapa ena achikatolika anachititsira kuti anthu ambirimbiri azizunzidwa, ananena kuti: “Munthu akakhala pa udindo, amakula mphamvu, ndipo udindowo ukakhala waukulu, amakulanso mphamvu kwambiri.” Poganizira zimenezi, tiyeni tikambirane funso ili: Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza ulamuliro?

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KULEMEKEZA ULAMULIRO?

6, 7. (a) Kodi kukonda Yehova kumatilimbikitsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi kugonjera kumatanthauza chiyani, ndipo tingasonyeze bwanji kuti timagonjera?

6 Timalemekeza ulamuliro chifukwa cha chikondi. Timakonda Yehova, anthu anzathu ndiponso moyo wathu. Timafuna kukondweretsa mtima wa Yehova chifukwa chakuti timamukonda kwambiri kuposa wina aliyense. (Werengani Miyambo 27:11; Maliko 12:29, 30.) Timadziwa kuti kuchokera pamene anthu oyamba anakana kumvera Mulungu mu Edeni, Satana wakhala akutsutsa zoti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndiponso anthu ambiri akhala kumbali ya Satana ndipo amakana kulamuliridwa ndi Yehova. Koma ifeyo timanyadira kukhala ku mbali ya Yehova. Mawu a pa Chivumbulutso 4:11 amatikhudza mtima kwambiri. Ifeyo tikudziwa bwino kuti Yehova ndi amene ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Timagonjera ulamuliro wa Yehova ndipo timatsatira malamulo ake pa moyo wathu.

7 Kulemekeza ulamuliro kumatanthauza zambiri osati kumvera kokha. Timamvera Yehova mosanyinyirika chifukwa chakuti timamukonda. Komabe, pamakhala nthawi zina pamene zimativuta kwambiri kumvera. Pa nthawi ngati zimenezi, ifeyo mofanana ndi mwana tamufotokoza koyambirira uja, timafunika kuphunzira kukhala ogonjera. Kumbukirani kuti Yesu anachita chifuniro cha Atate wake ngakhale kuti zimenezi zinaoneka kuti zinali zovuta kwambiri. Iye anauza Atate wake kuti: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.”—Luka 22:42.

8. (a) Kodi kugonjera ulamuliro wa Yehova masiku ano kumafuna chiyani, ndipo ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza mmene Yehova amaonera nkhaniyi? (b) Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kumvera uphungu ndi kulandira chilango? (Onani bokosi  “Mvera Uphungu Ndipo Utsatire Malangizo.”)

8 Masiku ano, Yehova salankhula nafe mwachindunji, koma amagwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso anthu omuimira padziko lapansi. Choncho, timagonjera ulamuliro wa Yehova tikamalemekeza anthu amene wawaika, kapena kuwalola kuti azititsogolera. Tikapanda kumvera uphungu wa anthuwa ndi malangizo awo a m’Malemba, ndiye kuti tikuukira komanso tikulakwira Mulungu. Aisiraeli atayamba kung’ung’udza ndi kuukira Mose, Yehova anaona kuti iwo samalimbana ndi Mose koma iyeyo.—Numeri 14:26, 27.

9. Kodi n’chifukwa chiyani kukonda anzathu kungatilimbikitse kulemekeza ulamuliro? Perekani chitsanzo.

9 Timalemekezanso ulamuliro chifukwa chakuti timakonda anthu anzathu. N’chifukwa chiyani izi zili choncho? Tiyerekezere kuti inu ndinu msilikali m’gulu lankhondo linalake. Kuti gulu lankhondolo lipambane ngakhale kupulumuka kumene, zimadalira kuti msilikali aliyense azimvera, kulemekeza ndi kugwirizana ndi akuluakulu awo. Koma ngati inu simungatsatire zinthu zofunikirazi, inuyo ndi asilikali anzanu onsewo mungakhale pa ngozi. Masiku ano magulu a asilikali ankhondo amawononga zinthu ndi kupha anthu mwachisawawa. Mosiyana ndi zimenezi, magulu a asilikali ankhondo a Yehova amachita zabwino zokhazokha. M’Baibulo muli malo ambiri amene amatchula Mulungu kuti “Yehova wa makamu.” (1 Samueli 1:3) Iye ndi Mtsogoleri wa makamu ambirimbiri a zolengedwa zauzimu zamphamvu kwambiri. Nthawi zina Yehova amayerekezera atumiki ake apadziko lapansi ndi gulu la asilikali. (Salimo 68:11; Ezekieli 37:1-10) Ndiye ngati sitimvera anthu amene Yehova wawapatsa ulamuliro, tingakhale tikuika moyo wa asilikali auzimu anzathu pa ngozi. Ngati Mkhristu samvera akulu mumpingo, anthu enanso mu mpingowo amavutika. (1 Akorinto 12:14, 25, 26) N’chimodzimodzinso mwana akakhala wosamvera, banja lonse lingavutike. Choncho, timasonyeza kuti timakonda anzathu ngati timawalemekeza komanso kuwadalira.

10, 11. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kumvera anthu amene ali ndi ulamuliro?

10 Timalemekezanso ulamuliro chifukwa tikamachita zimenezi timapindula. Yehova akamatipempha kulemekeza ulamuliro, kawirikawiri amatchulanso madalitso omwe tingapeze tikamvera. Mwachitsanzo, amauza ana kuti azimvera makolo awo kuti anawo akhale ndi moyo wautali ndiponso wamtendere. (Deuteronomo 5:16; Aefeso 6:2, 3) Amatiuzanso kuti tonsefe tizilemekeza akulu mu mpingo chifukwa ngati sitingatero, tingavulale mwauzimu. (Aheberi 13:7, 17) Ndiponso amatiuza kuti tizimvera olamulira a boma kuti tikhale otetezeka.—Aroma 13:4.

11 Tsopano tadziwa chifukwa chake Yehova amafuna kuti tizikhala omvera. Kodi simukuvomereza kuti kudziwa zimenezi kungatithandize kulemekeza ulamuliro? Ndiyeno, tiyeni tikambirane mmene tingalemekezere ulamuliro pa mbali zitatu zofunika kwambiri.

KUSONYEZA ULEMU M’BANJA

12. Kodi ndi udindo wotani umene Yehova anapatsa mwamuna, ndipo mwamuna angakwaniritse bwanji udindo umenewu?

12 Yehova ndi amene anayambitsa banja. Iye ndi Mulungu wadongosolo, choncho anaperekanso njira zothandiza kuti banjalo liziyenda mwadongosolo. (1 Akorinto 14:40) Iye anapatsa mwamuna udindo wokhala mutu wa banja. Mwamuna amalemekeza Mutu wake, yemwe ndi Khristu Yesu, akamatsanzira mmene Yesu amachitira potsogolera mpingo. (Aefeso 5:23) Choncho, mwamuna sayenera kuthawa udindo wake koma ayenera kuukwaniritsa molimba mtima. Iye sayenera kukhala wopondereza ndi wankhanza. M’malomwake, ayenera kukhala wachikondi, wololera ndi wokoma mtima. Iye amakumbukira kuti ulamuliro wake uli ndi malire, ndipo sungapose ulamuliro wa Yehova.

Bambo wachikhristu amatsanzira mmene Khristu amachitira potsogolera mpingo

13. Kodi mkazi angakwaniritse bwanji udindo wake m’banja m’njira yokondweretsa Yehova?

13 Udindo wa mkazi ndi kuthandiza mwamuna wake. Mkazinso ali ndi ulamuliro m’banja, chifukwa Baibulo limanena kuti iye amaperekansomalangizo kapena kuti “malamulo.” (Miyambo 1:8) Koma ulamuliro wake si wofanana ndi wa mwamuna wake. Mkazi wachikhristu amalemekeza ulamuliro wa mwamuna wake pomuthandiza kukwaniritsa udindo wake monga mutu wa banja. Sanyoza mwamuna wake, kumunyengerera kuti azichita zofuna zake ndiponso salanda udindo wa mwamuna wakeyo. M’malomwake, iye amakhala wothandiza ndiponso wogwirizana ndi mwamuna wake. Ngati mkazi sakugwirizana ndi zimene mwamuna wake wasankha, angathe kunena maganizo ake mwaulemu, koma amakhalabe wogonjera kwa mwamuna wakeyo. Ngati mwamuna wakeyo ali wosakhulupirira, mkazi angakumane ndi mavuto ambiri. Koma akakhalabe wogonjera, mwamunayo angakopeke ndi khalidwe la mkazi wake ndipo angafune kuphunzira za Yehova.—Werengani 1 Petulo 3:1.

14. Kodi ana angasangalatse bwanji makolo awo komanso Yehova?

14 Ana amakondweretsa mtima wa Yehova akamamvera bambo ndi mayi awo. Komanso amalemekeza ndi kukondweretsa makolowo. (Miyambo 10:1) M’mabanja amene muli mayi kapena bambo okha, ana ayeneranso kukhala omvera, podziwa kuti kholo lawolo lili ndi udindo waukulu ndipo amafunikira kulithandiza kwambiri. M’mabanja amene aliyense amakwaniritsa udindo wake umene Mulungu anamupatsa, mumakhala mtendere ndi chimwemwe chachikulu. Zimenezi zimachititsa kuti Yehova Mulungu amene anayambitsa banja alemekezedwe.—Aefeso 3:14, 15.

KUSONYEZA ULEMU MUMPINGO

15. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza ulamuliro wa Yehova mumpingo? (b) Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kumvera amene akutitsogolera? (Onani bokosi  “Muzimvera Amene Amakutsogolerani.”)

15 Yehova wasankha Mwana wake kukhala wolamulira mpingo wachikhristu. (Akolose 1:13) Nayenso Yesu wasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azisamalira zosowa zauzimu za anthu a Mulungu padziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi lomwe lili “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Monga mmene zinalili ndi mpingo wachikhristu woyambirira, akulu masiku ano amalandira malangizo ndi uphungu kuchokera ku Bungwe Lolamulira. Amalandira malangizo amenewa kudzera m’makalata kapena mwa abale monga oyang’anira dera amene amaimira bungweli. Ifeyo tikamalemekeza ulamuliro wa akulu achikhristu, timamvera Yehova.—Werengani 1 Atesalonika 5:12; Aheberi 13:17.

16. Kodi akulu amaikidwa bwanji ndi mzimu woyera?

16 Akulu ndi atumiki othandiza ndi anthu opanda ungwiro. Mofanana ndi ife tonse, nawonso amalakwa. Ngakhale zili choncho, akulu ndi “mphatso za amuna,” zimene zaperekedwa kuti zithandize mpingo kukhalabe wolimba mwauzimu. (Aefeso 4:8) Akulu amaikidwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 20:28) Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Amuna amenewa choyamba afunika kuyesetsa kuchita zinthu zowathandiza kuti ayenerere udindo mumpingo, zomwe zili m’Mawu a Mulungu ouziridwa ndi mzimu. (1 Timoteyo 3:1-7, 12; Tito 1:5-9) Ndiponso, akulu akamakambirana za m’bale winawake amene angayenerere udindo mumpingo, amapemphera mochokera pansi pa mtima kuti mzimu woyera wa Yehova uwatsogolere.

17. Pa zochitika za mumpingo, n’chifukwa chiyani akazi achikhristu nthawi zina amavala chinachake kumutu?

17 Nthawi zina zimachitika mumpingo kuti palibe akulu ndi atumiki othandiza oti achite ntchito yofunikira iwowo, monga kuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda. Zikatero, abale ena obatizidwa angachite ntchitoyi. Ngati abalewo palibe, alongo oyenerera angachite ntchito imeneyo. Komabe, mkazi akamasamalira udindo umene uyenera kuchitidwa ndi mwamuna wobatizidwa, ayenera kuvala chinachake kumutu. * (1 Akorinto 11:3-10) Lamulo limeneli silinyozetsa akazi. M’malomwake, limawapatsa mpata wolemekeza zimene Yehova anakonza pa nkhani ya umutu, m’banja ndi mumpingo momwe.

KULEMEKEZA BOMA

18, 19. (a) Kodi mungafotokoze bwanji mfundo zimene zili pa Aroma 13:1-7? (b) Kodi timalemekeza bwanji boma?

18 Akhristu oona amayesetsa kutsatira mfundo zotchulidwa pa Aroma 13:1-7. (Werengani.) Mukamawerenga lemba limeneli, mutha kuona kuti “olamulira akuluakulu” amene atchulidwa pamenepo akutanthauza maboma a anthu. Pa nthawi yonse imene Yehova walola maboma a anthu amenewa kukhalapo, iwo amagwira ntchito zofunika kwambiri monga kukhazikitsa mtendere ndiponso kupereka zinthu zina zofunika pa moyo wa anthu. Timalemekeza olamulira amenewa tikamamvera malamulo a boma. Timaonetsetsa kuti tikupereka misonkho yonse, kulemba mafomu kapena zikalata zimene boma likufuna, ndiponso timatsatira malamulo alionse okhudza ifeyo, banja lathu, bizinezi yathu kapenanso katundu wathu. Komabe, sitigonjera a boma ngati iwo atilamula kusamvera Mulungu. M’malomwake, timayankha ngati mmene anayankhira atumwi kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:28, 29; onani bokosi lakuti: “ Kodi Ndiyenera Kumvera Ulamuliro wa Ndani?

19 Timalemekezanso boma tikamasonyeza makhalidwe abwino. Nthawi zina, tingafunike kuchita zinthu ndi akuluakulu a boma. Mwachitsanzo, pamene mtumwi Paulo anaonekera kwa olamulira monga Mfumu Herode Agiripa ndi Bwanamkubwa Fesito, iye anawalankhula mwaulemu ngakhale kuti olamulira amenewa anali ndi makhalidwe oipa. (Machitidwe 26:2, 25) Timatsanzira Paulo nthawi zonse tikamalankhula ndi anthu onse audindo, kaya ndi mkulu wa boma yemwe ndi wolamulira wamphamvu kapena wapolisi. Kusukulu, ana achikhristu nawonso amayesetsa kulemekeza aphunzitsi awo, akuluakulu a sukulu kapenanso ogwira ntchito pasukulu. Sikuti timangolemekeza anthu okhawo amene amavomereza zikhulupiriro zathu, koma timakhalanso aulemu ngakhale kwa anthu amene amatsutsa Mboni za Yehova. M’pofunika kuti anthu osakhulupirira aziona kuti ndife aulemu.—Werengani Aroma 12:17, 18; 1 Petulo 3:15.

20, 21. Kodi ena mwa madalitso amene amabwera tikamalemekeza ulamuliro ndi otani?

20 Tiyeni tipewe mtima wosafuna kulemekeza ulamuliro. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.” (1 Petulo 2:17) Anthu akamaona kuti timawalemekeza mochokera pansi pamtima, amasangalala nafe. Kumbukirani kuti masiku ano anthu ambiri alibe khalidwe limeneli. Choncho, kulemekeza ena ndi njira imodzi imene tingasonyezere kuti timatsatira lamulo la Yesu lakuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:16.

21 M’dziko la mdimali, anthu amitima yabwino akukopeka ndi kuwala kwauzimu. Choncho, tikamasonyeza ulemu m’banja, mumpingo ndi pochita zinthu ndi anthu a boma, anthu ena angakopeke, nawonso n’kuyamba kuyenda m’kuwala kwauzimu. Zimenezitu zingakhale zosangalatsa kwambiri. Ngakhale kuti nthawi zina zimenezi sizingachitike, ndife otsimikiza kuti kulemekeza anthu kumasangalatsa Yehova Mulungu ndipo kumachititsa kuti apitirize kutikonda. Palibenso mphoto yoposa imeneyi.

^ ndime 17 Onani Zakumapeto “Kodi Mlongo Ayenera Kuvala Chinachake Kumutu pa Zochitika Ziti, Ndipo N’chifukwa Chiyani?” Pamenepa pali njira zingapo zofotokoza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imeneyi.