Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni

Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zopangira Opaleshoni

Tizigawo ta magazi. Tizigawo timeneti timatengedwa m’zigawo zikuluzikulu 4 za magazi. Zigawo zikuluzikulu zimenezi ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana, ndi madzi a m’magazi. Mwachitsanzo, maselo ofiira amakhala ndi pulotini inayake yotchedwa himogulobini. Ndipo pulotini ya mtundu umenewu yotengedwa m’magazi a anthu kapena a nyama amaigwiritsa ntchito popanga mankhwala amene amaperekedwa kwa anthu amene akudwala matenda osowa magazi kapena amene ataya magazi ambiri.

M’madzi a m’magazi, omwe pafupifupi onse ndi madzi wamba, muli zinthu zambirimbiri zothandiza m’thupi monga mchere, shuga ndi zina zotero. Madzi a m’magaziwo amakhalanso ndi mapulotini ena osiyanasiyana, tinthu tina tothandiza magazi kuundana ndiponso maselo olimbana ndi matenda. Ngati munthu wadwala matenda enaake, madokotala angapereke jakisoni wa madzi otengedwa m’madzi a m’magazi a anthu amene magazi awo amatha kulimbana ndi matendawo. Ndipo m’maselo oyera amatha kuchotsamo tinthu tina timene amapangira mankhwala othandizira anthu odwala matenda a khansa kapena matenda ena oyambitsidwa ndi mavailasi.

Kodi Mkhristu ayenera kulandira mankhwala opangidwa kuchokera ku tizigawo ta magazi? M’Baibulo mulibe malamulo onena kuti alandire kapena ayi. Choncho aliyense ayenera kusankha yekha zochita mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Akhristu ena amakana tizigawo tonse ta magazi, chifukwa amaona kuti lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli limanena kuti magazi akachoka m’thupi la cholengedwa chilichonse ‘azithiridwa pansi.’ (Deuteronomo 12:​22-24) Ena amakana kuikidwa magazi kapena zigawo zikuluzikulu za magazi koma amatha kulandira mankhwala ochokera ku tizigawo ta magazi. Iwo amaona kuti tizigawo ta magazi tikachotsedwa m’magazimo sitimaimiranso moyo wa cholengedwa chimene mwachotsedwa magaziwo.

Posankha zochita pa nkhani ya tizigawo ta magazi, ganizirani mafunso awa: Kodi ndikudziwa kuti kukana tizigawo tonse ta magazi kukutanthauza kuti sindingalandire mankhwala ena amene ali ndi tinthu tina ta m’magazi tolimbana ndi matenda kapena amene amathandiza magazi kuundana kuti asiye kutuluka? Kodi ndingathe kufotokozera dokotala chifukwa chimene ndikukanira kapena kuvomerera tizigawo tina ta magazi?

Njira zopangira opaleshoni. Zina mwa njira zimenezi ndi kusungunula magazi ndiponso kupulumutsa magazi. Potsatira njira yosungunula magazi, magazi a wodwala amawapatutsa kuchoka m’thupi ndipo amamuika wodwalayo madzi owonjezera magazi. Kenako magazi opatutsidwa aja, amawaikanso m’thupi la wodwalayo. Potsatira njira yopulumutsa magazi, magazi amene amatayika popanga opaleshoni amapopedwa n’kubwezeretsedwa m’thupi la wodwalayo. Magaziwa amapopedwa pabala kapena pamalo ena amene ang’ambidwa, kenako amasefedwa n’kuwabwezeretsa m’thupi la wodwalayo. Madokotala amatsatira njirazi mosiyanasiyana, choncho Mkhristu aliyense ayenera kufunsa zimene madokotala akufuna kuchita.

Mukafuna kusankha chochita pa njira zopangira opaleshoni zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Ngati ena mwa magazi anga angatulutsidwe m’thupi langa ndipo mwina n’kusiya kuyenda kwakanthawi, kodi chikumbumtima changa chidzandilola kuona kuti magazi amenewa adakali mbali ya thupi langa, moti si ofunika kuti “[athiridwe] pansi”? (Deuteronomo 12:​23, 24) Kodi chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo chingandivutitse ngati pondipanga opaleshoni apatutsa magazi anga, n’kuwasakaniza ndi mankhwala ena, kenako n’kuwabwezeranso m’thupi mwanga? Kodi ndikudziwa kuti kukana njira zonse zachipatala zogwiritsa ntchito magazi anga omwe kukutanthauza kuti sindingalole kuyezedwa magazi, kuthandizidwa pogwiritsa ntchito makina osefa magazi kapena makina ogwira ntchito ya mtima ndi mapapo?’

Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zimene akufuna kuti madokotala achite ndi magazi ake pamene akumuchita opaleshoni. N’chimodzimodzinso ndi magazi ake amene atengedwa kuti ayezedwe kapenanso njira zina zochiritsira zimene zayamba posachedwapa zomwe amachotsa magazi ochepa m’thupi, n’kuwasakaniza ndi mankhwala ena kenako n’kuwabwezeretsanso.