Kodi Nkhani ya M’buku la Genesis Ikugwirizana ndi Sayansi?
Anthu ambiri amanena kuti zimene asayansi apeza zimatsutsana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani yolenga zinthu. Koma zimenezi si zoona. Kungoti zimene anthu ena achipembedzo amakhulupirira ndi zimene zimatsutsana ndi sayansi. Iwo amanena kuti Baibulo limaphunzitsa kuti zinthu zonse padzikoli zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24, pafupifupi zaka 10,000 zapitazo.
Koma Baibulo siliphunzitsa zimenezi. Zikanakhala choncho, ndiye kuti zimene asayansi atulukira pa zaka 100 zapitazi zikanasonyezadi kuti Baibulo si loona. Munthu akamaphunzira Baibulo bwinobwino amazindikira kuti zimene limaphunzitsa sizitsutsana ndi mfundo zasayansi. N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sagwirizana ndi zoti zinthu zapadzikoli zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24 ngati mmene anthu ena achipembedzo amanenera. Tiyeni tsopano tione zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni pa nkhaniyi.
Buku la Genesis silinena kuti zinthu zonse padzikoli zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24, pafupifupi zaka 10,000 zapitazo
Kodi Mawu Oti “pa Chiyambi” Amanena za Nthawi Iti?
Buku la Genesis limayamba ndi mawu akuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Akatswiri ambiri a Baibulo amavomereza kuti mawuwa akunena za nthawi yosiyana ndi ya masiku olenga zinthu amene amatchulidwa kuyambira pa vesi 3. Mfundoyi ndi yofunika kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti ikusonyeza kuti mawu oyamba a m’Baibulowa akutanthauza kuti zinthu zina za m’chilengedwe, kuphatikizapo dziko lapansili, zinalipo kale masiku olenga zinthu asanayambe.
Asayansi amanena kuti dzikoli lakhalapo kwa zaka 4 biliyoni ndipo zinthu zina za m’chilengedwe zakhalapo kwa zaka pafupifupi 15 biliyoni. Kodi zimene asayansi amanenazi zimatsutsana ndi mawu a pa Genesis 1:1? Ayi. Baibulo silinena kuti “kumwamba ndi dziko lapansi” zakhalapo kwa nthawi yaitali bwanji. Choncho Baibulo silimatsutsana ndi mfundo zasayansi.
Kodi Masiku Olenga Zinthu Anali Aatali Bwanji?
Kodi masiku olenga zinthu anali a maola 24 enieni? Anthu ena amanena kuti popeza Mose, yemwe analemba buku la Genesis, ananena kuti tsiku limene linatsatira masiku olenga zinthu linali ngati Sabata limene anthu amasunga mlungu uliwonse, ndiye kuti masiku olenga anali a maola 24. (Ekisodo 20:11) Koma kodi buku la Genesis limaphunzitsadi zimenezo?
Ayi, siliphunzitsa zimenezo. Mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti “tsiku” angatanthauze zambiri. Mwachitsanzo, pamene Mose anafotokoza mwachidule zinthu zonse zimene Mulungu analenga, anatchula masiku onse 6 ngati tsiku limodzi. (Genesis 2:4) Apa zikuonekeratu kuti palibe chifukwa chomveka chonenera kuti masiku olenga zinthu anali a maola 24.
Ndiye kodi masiku olenga zinthu anali aatali bwanji? Baibulo silinena koma mawu a m’chaputala 1 ndi 2 cha Genesis amasonyeza kuti masikuwa anali a nthawi yaitali ndithu.
Nyengo 6 Zolenga Zinthu
Mose analemba nkhani yokhudza kulenga zinthu m’Chiheberi. Komanso nkhaniyi anailemba ngati kuti wolembayo akuona zinthuzo ataima padziko lapansi. Mfundo ziwirizi komanso mfundo yakuti dziko lapansi linakhalapo masiku olenga zinthu asanayambe zimathandiza kuti anthu asamatsutse nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulenga zinthu. Kodi tikutero chifukwa chiyani?
Tikaphunzira bwinobwino buku la Genesis tingaone kuti zinthu zina zimene zinayamba kuchitika ‘m’tsiku’ lina zinapitiriza mpaka ‘m’masiku’ otsatira. Mwachitsanzo, “tsiku” loyamba la kulenga zinthu lisanayambe, kuwala kochokera kudzuwa, lomwe linali lilipo kale, sikunkafika padzikoli mwina chifukwa chakuti kunkaphimbidwa ndi mitambo. (Yobu 38:9) Koma pa “tsiku” loyamba, kuwalako kunayamba kuoneka pang’ono padziko lapansi. *
Pa tsiku lachiwiri analekanitsa thambo ndi nyanja ndipo pa “tsiku” la 4 anachititsa kuti dzuwa ndi mwezi ziyambe kuonekera kumwamba. (Genesis 1:14-16) M’mawu ena, tinganene kuti pa nthawi imeneyo ngati munthu akanaima padziko lapansi akanatha kuona dzuwa ndi mwezi. Zinthuzi zinkachitika mwapang’onopang’ono.
Buku la Genesis limanenanso kuti pa “tsiku” la 5 tizilombo touluka ndiponso nyama zokhala ndi mapiko zinayamba kupezeka.
Baibulo limasonyeza kuti mwina zinthu zina zimene zinachitika m’tsiku lina lolenga zinkachitika pang’onopang’ono ndipo n’kutheka kuti zinkapitiriza mpaka kufika m’masiku otsatira. *
“Monga mwa Mtundu Wake”
Kodi mfundo yoti mitundu yosiyanasiyana ya zomera ndiponso zinyama inayamba kukhalapo mwapang’onopang’ono ikusonyeza kuti polenga zinthu Mulungu anachititsa kuti zamoyo zizisintha kuchokera ku zinthu zina? Ayi. Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu analenga zomera komanso nyama “monga mwa mtundu wake.” (Genesis 1:11, 12, 20-25) Kodi mitundu imene analengayo inali yoti ikhoza kusintha pang’ono kuti igwirizane ndi kumene ili? Nanga kodi mitunduyo ikhoza kusintha kufika pati? Baibulo silifotokoza zimenezi. Chomwe limanena ndi chakuti zamoyozo zinachuluka mogwirizana ndi “mitundu yake.” (Genesis 1:21) Mfundo imeneyi ikusonyeza kuti zamoyo zikhoza kusintha pang’ono koma pali malire, moti sizingasinthiretu n’kukhala za mtundu wina. Zimene asayansi apeza zimatsimikizira kuti pa zaka zambirimbiri zimene zadutsazi, zomera komanso zinyama zamitundu yosiyanasiyana zangosintha pang’ono.
Mosiyana ndi zimene anthu ena achipembedzo amanena, buku la Genesis siliphunzitsa kuti zinthu zonse zapadzikoli zinalengedwa munthawi yochepa zaka pafupifupi 10,000 zapitazo. Koma zimene bukuli limanena pa nkhani yolenga zinthu zimagwirizana ndi zimene asayansi atulukira posachedwapa.
Zimene asayansi amakhulupirira zimawachititsa kutsutsa mfundo ya m’Baibulo yakuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. Koma chochititsa chidwi n’chakuti Mose analemba m’buku la Genesis kuti zinthu zonse zili ndi chiyambi ndipo zinkakhalapo mwapang’onopang’ono kwa nthawi yaitali. Kodi zinatheka bwanji kuti Mose azindikire mfundo yogwirizana ndi sayansiyi zaka zoposa 3,500 zapitazo? Yankho lake ndi losavuta. Amene ali ndi mphamvu komanso nzeru zotha kulenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi amenenso anathandiza Mose kuzindikira mfundo imeneyi. Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” *—2 Timoteyo 3:16.
Mwina mukudzifunsa kuti, Kodi zimene ndimakhulupirira pa nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulenga zinthu zimakhudzadi moyo wanga? Tiyeni tikambirane yankho la funso limeneli.
^ ndime 13 Pofotokoza zimene zinachitika pa “tsiku” loyamba, anagwiritsa ntchito mawu achiheberi akuti ‘ohr amene amanena za kuwala basi. Koma pofotokoza za “tsiku” la 4, anagwiritsa ntchito mawu oti ma·’ohrʹ omwe amatanthauza kumene kuwalako kumachokera.
^ ndime 16 Mwachitsanzo, pa tsiku la 6 lolenga zinthu, Mulungu analamula kuti anthu ‘achuluke ndipo adzaze dziko lapansi.’ (Genesis 1:28, 31) Koma zimenezi sizinayambe kuchitika mpaka “tsiku” lotsatira.—Genesis 2:2.
^ ndime 20 Kuti mudziwe zambiri, onani vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? yomwe ikupezeka pawebusaiti ya jw.org/ny.