MUTU 19
“Kulikonse Kumene Mtsinjewo Ukupita, Chilichonse Chidzakhala ndi Moyo”
MFUNDO YAIKULU: Mmene masomphenya a mtsinje umene ukuchokera m’kachisi anakwaniritsidwira m’mbuyomo, mmene akukwaniritsidwira masiku ano komanso mmene adzakwaniritsidwire m’tsogolo
1, 2. Mogwirizana ndi Ezekieli 47:1-12, kodi Ezekieli anaona komanso kuphunzira chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)
EZEKIELI anaonanso chinthu china chodabwitsa m’masomphenyawo. Anaona mtsinje ukuyenda kuchokera m’nyumba yopatulika. Tayerekezerani kuti mukumuona akuyenda kutsatira madzi oyerawo. (Werengani Ezekieli 47:1-12.) Mtsinjewo ukutuluka pakhomo la nyumba yopatulika, kenako ukudutsa pageti lakum’mawa la malo a pakachisipo. Mngelo amene akutsogolera Ezekieli akuchoka naye kukachisiko ndipo akutsatira mtsinjewo n’kumayeza kuzama kwake. Mobwerezabwereza mngeloyo akuuza Ezekieli kuti awoloke mtsinjewo ndipo mneneriyu akuona kuti ukuzama mofulumira. Pasanapite nthawi ukukhala mtsinje woti sangathe kuuwoloka pokhapokha atachita kusambira.
2 Ezekieli anamva kuti mtsinjewo ukukathira m’Nyanja Yakufa. M’nyanja imeneyi munali madzi amchere komanso munalibe chamoyo chilichonse. Koma mtsinjewo utakathira m’nyanjayi, munayamba kukhala nsomba zambiri. Komanso anaona kuti m’mbali mwa mtsinjewo mwamera mitengo yosiyanasiyana. Mwezi uliwonse mitengoyo imabala zipatso zabwino ndipo imaphuka masamba ochiritsa. Ezekieli ataona zonsezi ayenera kuti anapeza mtendere mumtima ndipo zinam’patsa chiyembekezo. Koma kodi mbali imeneyi ya masomphenya a pakachisi inkatanthauza chiyani kwa iyeyo ndi Ayuda ena omwe anali nawo ku ukapolo? Nanga kodi akutanthauza chiyani kwa ife masiku ano?
Kodi Mtsinje Umene Ezekieli Anaona M’masomphenya Unkatanthauza Chiyani kwa Ayuda Omwe Anali ku Ukapolo?
3. N’chifukwa chiyani Ayuda akale sankaona kuti masomphenya a mtsinje amene Ezekieli anaona akunena za zochitika zenizeni?
3 N’zodziwikiratu kuti Ayuda a m’nthawi yakale sankaona kuti zimene Ezekieli anaona m’masomphenyawo zinali zenizeni. N’kutheka kuti lemba limeneli linawakumbutsa ulosi wina wouziridwa wokhudza kubwezeretsa kulambira koyera umene unalembedwa ndi mneneri Yoweli mwina zaka zoposa 200 m’mbuyomo. (Werengani Yoweli 3:18.) Pamene Ayuda amene anali ku ukapolowo ankawerenga mawu a Yoweli, sankayembekezera kuti m’mapiri ‘mungatuluke vinyo wotsekemera’ weniweni kapena m’mapiri ang’onoang’ono ‘mungayende mkaka.’ Komanso sankayembekezera kuti “m’nyumba ya Yehova” mungatuluke kasupe. Mofanana ndi zimenezi, Ayuda anzake a mneneri Ezekieli sankaona kuti uthenga wakewu ukunena za mtsinje weniweni. a Ndiye kodi Yehova ankapereka uthenga wotani? Malemba amatithandiza kumvetsa mbali imeneyi ya masomphenyawa. Koma panopa tikambirana mbali zitatu zomveka bwino kuchokera mu ulosi umenewu zimene zikutipatsa chiyembekezo.
4. (a) Kodi mtsinje wa m’masomphenya a Ezekieli ukanachititsa kuti Ayuda aziyembekezera madalitso otani kuchokera kwa Yehova? (b) Kodi mmene Baibulo lagwiritsira ntchito mawu akuti “mtsinje” komanso “madzi” zikutitsimikizira bwanji kuti Yehova adzadalitsa anthu ake? (Onani bokosi lakuti “Mitsinje ya Madalitso Ochokera kwa Yehova.”)
4 Mtsinje wa madalitso. M’Baibulo mitsinje komanso madzi amagwiritsidwa ntchito kuimira madalitso opatsa moyo ochokera kwa Yehova. Ezekieli anaona mtsinje ngati umenewu ukuchokera pakachisi. Choncho masomphenyawa akanachititsa kuti anthu a Mulungu aziyembekezera kuti madalitso opatsa moyo ochokera kwa Yehova adzafika kwa iwo ngati angapitirizebe kulambira Yehova m’njira yovomerezeka. Kodi akanalandira madalitso otani? Iwo akanayambiranso kulandira malangizo kuchokera kwa ansembe. Popeza kuti akanayambiranso kupereka nsembe pakachisi, sakanakayikiranso kuti machimo awo aphimbidwa. (Ezek. 44:15, 23; 45:17) Zimenezi zikanapangitsa kuti akhalenso oyera ngati kuti asamba madzi oyera ochokera m’kachisi.
5. Kodi mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya ukuthetsa bwanji nkhawa yakuti mwina m’Paradaiso simudzakhala madalitso okwanira kwa wina aliyense?
5 Kodi zikanakhala zotheka kuti aliyense azilandira madalitso okwanira nthawi zonse? Masomphenyawo akuyankha funso limeneli chifukwa akusonyeza kuti madziwo akuchuluka modabwitsa moti mtsinjewo, womwe unali waung’ono unakula n’kukhala chimtsinje chachikulu pakamtunda kochepa chabe. (Ezek. 47:3-5) N’zoona kuti chiwerengero cha Ayuda amene anabwerera kwawo chikanatha kuwonjezereka, komabe madalitso a Yehova akanapitiriza kuwonjezeka moti aliyense akanapeza zimene akufunikira. Mtsinjewo unkaimira kuti m’dzikomo mudzakhala zinthu zochuluka kwambiri.
6. (a) Kodi masomphenyawa akupereka lonjezo liti lotsimikizika? (b) Kodi masomphenyawa akuperekanso chenjezo lotani? (Onani mawu am’munsi.)
6 Madzi opatsa moyo. M’masomphenya a Ezekieli, mtsinjewo ukukathira m’Nyanja Yakufa n’kuipangitsa kuti ikhale yamoyo. Onani kuti madziwo anapereka moyo kwa nsomba zambiri komanso zosiyanasiyana zofanana ndi zimene zikupezeka m’Nyanja Yaikulu kapena kuti nyanja ya Mediterranean. M’mbali mwa Nyanja Yakufa munkachitika bizinesi yaikulu yogulitsa nsomba pakati pa matauni awiri amene anali motalikirana. Mngeloyo ananena kuti: “Kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.” Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti madzi ochokera m’nyumba ya Yehovayo anafika mbali iliyonse ya Nyanja Yakufayo? Ayi. Mngeloyo ananena kuti m’madambo ena simunafike madzi opatsa moyowa. Malo amenewa ‘anakhalabe amchere.’ b (Ezek. 47:8-11) Choncho ulosiwu unapereka lonjezo lolimbikitsa lakuti kulambira koyera kudzathandiza kuti anthu akhalebe amphamvu komanso kuti zinthu ziziwayendera bwino. Koma anaperekanso chenjezo lakuti: Si aliyense amene adzalandire madalitso a Yehova kapena kuchiritsidwa.
7. Kodi kupezeka kwa mitengo m’mbali mwa mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya kunalimbikitsa bwanji Ayuda omwe anali ku ukapolo?
7 Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa. Kodi mitengo imene inali m’mbali mwa mtsinjewo inali ya ntchito yanji? Inkathandiza kuti malowo azioneka okongola, si choncho? Komanso mitengoyi inali ndi ntchito ina yofunika. Mosakayikira, Ezekieli ndi Ayuda anzake ayenera kuti ankasangalala akaganizira kuti mitengo imeneyi izidzawapatsa zipatso zokoma mwezi uliwonse. Zimenezi zinawatsimikizira kuti Yehova azidzawadyetsanso mwauzimu. Kodi mitengoyi ikanawathandizanso m’njira ina iti? Onaninso kuti Baibulo likunena kuti masamba a mitengoyo “adzakhala mankhwala.” (Ezek. 47:12) Yehova ankadziwa kuti koposa zonse, Ayuda amene adzabwerere kwawo adzafunika kuchiritsidwa mwauzimu ndipo analonjeza kuti adzawachiritsa. Maulosi ena okhudza kubwezeretsa anafotokoza mmene Mulungu anachitira zimenezi monga mmene Mutu 9 wa buku lino unafotokozera.
8. Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti masomphenya a Ezekieli anali oti adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu?
8 Koma mogwirizananso ndi zimene tinaona m’Mutu 9, Ayuda omwe anabwerera kwawo anaona mbali yochepa ya kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa. Zochita za anthuwo ndi zimene zinachititsa kuti asaone ulosiwu ukukwaniritsidwa m’mbali zonse. Kodi Yehova akanawadalitsa bwanji mokwanira pamene mobwerezabwereza ankachita zinthu zoipa, kusamvera komanso kunyalanyaza kulambira koyera? Ayuda okhulupirika zinkawapweteka komanso ankakhumudwa ndi zochita zoipa za Ayuda anzawo. Koma anthu amene ankalambira Yehova mokhulupirika ankadziwa kuti malonjezo ake amakwaniritsidwa nthawi zonse. (Werengani Yoswa 23:14.) Choncho masomphenya a Ezekieli anali oti tsiku lina adzakwaniritsidwa m’njira yaikulu. Koma kodi akanakwaniritsidwa liti?
Mtsinje Ukuyenda Masiku ano
9. Kodi masomphenya a kachisi amene Ezekieli anaona adzakwaniritsidwa liti m’njira yaikulu?
9 Monga mmene tinaonera m’Mutu 14 wa bukuli, masomphenya a Ezekieli a kachisi akukwaniritsidwa kwambiri “m’masiku otsiriza” ano, nthawi imene kulambira koyera kwakwezedwa kwambiri kuposa kale. (Yes. 2:2) Kodi mbali imeneyi ya ulosi wa Ezekieli ikukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
10, 11. (a) Kodi ndi madalitso ati amene akubwera kwa ife ngati mtsinje masiku ano? (b) Kodi madalitso ochokera kwa Yehova awonjezereka bwanji masiku ano kuti afikire anthu ambiri?
10 Mtsinje wa madalitso. Kodi madzi amene akuchokera m’nyumba ya Yehova akutikumbutsa za madalitso ati masiku ano? Akutikumbutsa za zinthu zambiri zimene Yehova amatipatsa zimene zimatithandiza mwauzimu. Chinthu chofunika kwambiri chimene watipatsa ndi nsembe ya dipo ya Khristu imene imatiyeretsa mwauzimu. Nsembe imeneyi imachititsa kuti zikhale zotheka kuti machimo athu akhululukidwe. Choonadi cha m’Mawu a Mulungu amachiyerekezeranso ndi madzi opatsa moyo omwe amayeretsa. (Aef. 5:25-27) Kodi madalitso amenewa tikuwalandira bwanji masiku ano?
11 Mu 1919, panali atumiki a Yehova ochepa kwambiri ndipo ankasangalala kulandira chakudya chauzimu chimene ankafunikira. Pamene zaka zinkapita, chiwerengero chawo chinkawonjezereka. Masiku ano chiwerengero cha anthu a Mulungu chikuposa 8 miliyoni. Kodi onsewa akulandira madzi oyera a choonadi pa nthawi yake? Inde. Pali mfundo zambiri za choonadi zimene panopa tikuzimvetsa bwino. Mwachitsanzo, zaka 100 zapitazi, anthu a Yehova atulutsa Mabaibulo mabiliyoni ambiri, mabuku, magazini, timabuku ndi timapepala. Mofanana ndi mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenyawo, choonadi chafalikira mofulumira kwambiri ndipo chathandiza anthu amene anali ndi ludzu la choonadi padziko lonse. Mabuku osindikizidwa, othandiza pophunzira Baibulo, akhala akupezeka kuyambira kalekale. Koma panopa, mabuku amenewa akupezeka pa webusaiti ya jw.org m’zilankhulo zoposa 900. Kodi madzi a choonadi amenewa amakhudza bwanji anthu amitima yabwino?
12. (a) Kodi taona zotani zosonyeza kuti uthenga wa choonadi wapereka moyo komanso thanzi lauzimu kwa anthu? (b) Kodi masomphenyawa akutipatsa chenjezo lotani la pa nthawi yake masiku ano? (Onaninso mawu am’munsi.)
12 Madzi opatsa moyo. Ezekieli anauzidwa kuti: “Kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.” Taganizirani mmene anthu omwe ali m’paradaiso wauzimu wobwezeretsedwa akupezera uthenga wa choonadi. Choonadi cha uthenga wa m’Baibulo chathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Komabe ulosiwu ukuperekanso chenjezo la pa nthawi yake lakuti: Si onse amene adzapitirize kumvetsera uthenga wa choonadi. Mofanana ndi madambo a madzi a m’mbali mwa Nyanja Yakufa, amene Ezekieli anaona m’masomphenya, pali anthu ena amene amakana kumvetsera uthenga wabwino kapena kugwiritsa ntchito mfundo za choonadi pa moyo wawo. c Tisalole kuti zimenezi zitichitikire.—Werengani Deuteronomo 10:16-18.
13. Kodi masiku ano tingaphunzire chiyani pa mitengo imene Ezekieli anaona m’masomphenya?
13 Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa. Kodi mitengo imene inali m’mbali mwa mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya ikutiphunzitsa chiyani masiku ano? Musaiwale kuti mitengoyi ikumabereka zipatso zokoma mwezi uliwonse ndipo masamba ake ndi mankhwala. (Ezekieli 47:12) Zimenezi zikutikumbutsa kuti tikutumikira Mulungu amene amatidyetsa mokwanira komanso kutichiritsa m’njira yofunika kwambiri yomwe ndi yauzimu. Masiku ano dzikoli likudwala mwauzimu ndipo anthu samvetsa mfundo za choonadi. Ndiye yerekezerani zimenezi ndi zimene Yehova akutipatsa. Mutawerenga nkhani m’magazini yathu, kuimba nyimbo yomaliza pamsonkhano wadera kapena wachigawo, kapena mutamaliza kuonera vidiyo, kodi munamva kuti Yehova wakudalitsani pokupatsani chakudya chauzimu chimenecho? Kunena zoona tili ndi chakudya chauzimu chochuluka. (Yes. 65:13, 14) Kodi chakudya chauzimuchi chimatithandiza kukhala olimba mwauzimu? Malangizo amene timalandira omwe amachokera m’Mawu a Mulungu, amatithandiza kulimbana ndi adani amene angasokoneze moyo wathu wauzimu monga chiwerewere, dyera komanso kupanda chikhulupiriro. Yehova wakhazikitsanso njira yothandizira Akhristu kuti azilimbana ndi matenda auzimu amene amabwera chifukwa cha tchimo lalikulu. (Werengani Yakobo 5:14.) Yehova watidalitsadi mogwirizana ndi mmene masomphenya a mitengo amene Ezekieli anaona akusonyezera.
14, 15. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa madambo osachiritsika amene Ezekieli anaona m’masomphenya? (b) Kodi masomphenya a mtsinje amene Ezekieli anaona akutithandiza bwanji masiku ano?
14 Koma pali zinanso zimene tikuphunzira kuchokera pa madambo amene sanachiritsidwe ndi madzi aja. Sitingayese n’komwe kukana kulandira madalitso ochokera kwa Yehova. Zingakhale zomvetsa chisoni ngati titakhala osachiritsika ngati mmene zilili ndi anthu ambiri m’dziko losachiritsikali. (Mat. 13:15) M’malomwake, timasangalala ndi mtsinje wa madalitso amene tikulandira. Tikamamwa madzi oyera a choonadi ochokera m’Mawu a Mulungu, tikamauza ena choonadi pogwira ntchito yolalikira, tikamalandira malangizo achikondi, tikamalimbikitsidwa komanso kuthandizidwa ndi akulu amene aphunzitsidwa ndi kapolo wokhulupirika, timaganizira za mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya. Kulikonse kumene mtsinjewo ukupita umathandiza kuti anthu akhale ndi moyo komanso kuwachiritsa.
15 Koma kodi chidzachitike n’chiyani masomphenya a mtsinjewa akadzakwaniritsidwa m’tsogolo? M’ndime zakutsogoloku, tiona kuti madzi amtsinjewo adzayenda kwambiri m’Paradaiso amene akubwerayo.
Mmene Masomphenyawa Adzakwaniritsidwire M’Paradaiso
16, 17. (a) Kodi madzi a moyo adzachuluka bwanji m’Paradaiso? (b) Kodi tidzapindula bwanji ndi mtsinje wa madalitsowu m’Paradaiso?
16 Kodi mumayerekezera muli m’Paradaiso limodzi ndi achibale komanso anzanu mukusangalala ndi moyo mokwanira? Kuphunzira masomphenya a mtsinje umene Ezekieli anaona kungakuthandizeni kuona kuti zimenezi ndi zenizeni. Kodi zingakuthandizeni bwanji? Ganiziraninso zinthu zitatu zimene tikuzipeza m’masomphenyawa zosonyeza kuti Mulungu amatikonda.
17 Mtsinje wa madalitso. Tinganene kuti mtsinje wophiphiritsawu udzakhala waukulu m’Paradaiso chifukwa choti madalitso ake sadzakhala auzimu okha koma adzakhalanso akuthupi. Mu ulamuliro wa Yesu wa Zaka 1,000, Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu okhulupirika kuti apindule ndi nsembe ya dipo m’njira yaikulu kwambiri. Iwo adzasintha pang’onopang’ono n’kukhala angwiro. Sipadzakhalanso matenda, madokotala, manesi, zipatala kapena kusunga ndalama kuti zidzatithandize tikadzadwala mwadzidzidzi. Anthu mabiliyoni ambiri amene adzapulumuke pa Aramagedo, adzalandira madzi amoyo. Anthu amenewa ndi “khamu lalikulu” limene lidzatuluke mu “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:9, 14) Komabe, mtsinje wa madalitso umenewu ngakhale kuti udzakhala wochititsa chidwi, udzakhala wochepa tikayerekezera ndi zimene zidzabwere pambuyo pake. Monga taonera m’masomphenya a Ezekieli, mtsinjewo udzakula kuti madalitso afikire anthu ambiri.
18. Kodi “mtsinje wa madzi a moyo” udzakhala bwanji mtsinje wa madzi ambiri mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu?
18 Madzi opatsa moyo. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, “mtsinje wa madzi amoyo” udzakula kwambiri. (Chiv. 22:1) Anthu mamiliyoni osawerengeka kapenanso mabiliyoni adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala m’Paradaiso mpaka kalekale. Madalitso amene Yehova adzatipatse kudzera mu Ufumu wake adzaphatikizapo kuukitsa anthu ambirimbiri amene anamwalira, anthu amene akhala akugona mufumbi kwa nthawi yaitali. (Yes. 26:19) Komabe kodi aliyense amene adzaukitsidwe adzakhala ndi moyo mpaka kalekale?
19. (a) N’chiyani chimene chikusonyeza kuti m’Paradaiso tidzapeza madzi atsopano a choonadi chochokera kwa Mulungu? (b) Kodi anthu ena “adzakhalabe amchere” m’tsogolo m’njira yotani?
19 Aliyense adzayenera kusankha yekha. Pa nthawi imeneyo, mipukutu yatsopano idzatsegulidwa. Choncho madzi otsitsimula ochokera kwa Yehova, adzaphatikizapo mfundo zatsopano za choonadi komanso malangizo atsopano auzimu. Kodi zimenezi si zochititsa chidwi? Komabe anthu ena adzakana kutsatira malangizo atsopanowa ndipo m’malomwake adzasankha kusamvera Yehova. N’kutheka kuti anthu ena adzakhala osamvera m’kati mwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, koma sadzaloledwa kuti azichita zosokoneza m’Paradaiso. (Yes. 65:20) Zimenezi zikutikumbutsa masomphenya a Ezekieli komanso kutichititsa kuganizira za madambo opanda chonde amene “adzakhalabe amchere.” Anthu amene amakana mouma mtima kumwa madzi amtengo wapatali opatsa moyo, ndi opusa kwambiri. Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, gulu la anthu oukira adzakhala kumbali ya Satana. Onse amene adzakane ulamuliro wolungama wa Yehova adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso mpaka kalekale.—Chiv. 20:7-12.
20. Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, kodi padzakonzedwa dongosolo lotani limene likutikumbutsa mitengo imene Ezekieli anaona m’masomphenya?
20 Mitengo ya zipatso komanso yochiritsa. Yehova sakufuna kuti wina aliyense aphonye mwayi wokapeza moyo wosatha. Pofuna kutithandiza kuti tisaphonye mwayi wamtengo wapatali umene akutipatsawu, adzaonetsetsanso kuti pali dongosolo lofanana ndi mitengo imene Ezekieli anaona. Koma m’Paradaiso madalitso ochokera kwa Yehova adzakhala akuthupi komanso auzimu. Ali kumwamba, Yesu Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000 adzalamulira monga mafumu kwa zaka 1,000. Monga ansembe, a 144,000 adzapereka madalitso obwera chifukwa cha nsembe ya dipo ya Khristu ndipo adzathandiza anthu okhulupirika kuti akhale angwiro. (Chiv. 20:6) Dongosolo limeneli, loti anthu achiritsidwe mwauzimu komanso mwakuthupi, likutikumbutsa za mitengo imene Ezekieli anaona m’mbali mwa mtsinje, imene inkabereka zipatso zokoma ndipo masamba ake anali ochiritsa. Masomphenya a Ezekieli akufanana ndi ulosi wina wochititsa chidwi umene unalembedwa ndi mtumwi Yohane. (Werengani Chivumbulutso 22:1, 2.) Masamba a mitengo imene Yohane anaona, “anali ochiritsira mitundu ya anthu.” Anthu mamiliyoni ambirimbiri okhulupirika adzapindula ndi ntchito imene a 144,000 adzagwire monga ansembe.
21. Kodi kuganizira masomphenya a mtsinje umene Ezekieli anaona, kukukukhudzani bwanji, nanga m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani? (Onani bokosi lakuti, “Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu.”)
21 Mukamaganizira za masomphenya a mtsinje umene Ezekieli anaona, kodi mumtima mwanu simukudzaza mtendere komanso chiyembekezo? Tikuyembekezeratu zinthu zosangalatsa kwambiri kutsogoloku. Tangoganizani, zaka masauzande ambiri zapitazo Yehova anatithandiza kuona chithunzi cha mmene zinthu zidzakhalire ndipo moleza mtima, akutipempha kuti tidzakhalepo pa nthawiyo kuti tidzaone kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi umenewu. Kodi mudzakhalapo? Mwina mungamakayikire kuti kodi malo anga adzakhalapo m’Paradaiso? Tsopano tiyeni tione mmene mavesi omalizira a ulosi wa Ezekieli akutithandizira kuti tisamakayikire lonjezo limeneli.
a Kuwonjezera pamenepo, Ayuda omwe anali ku ukapolo omwe ankakumbukira mmene dziko lawo linalili, ankadziwa kuti mtsinje umenewu sungakhale weniweni. Tikutero chifukwa chakuti mtsinjewu ukuyambira m’kachisi amene ali pamwamba pa phiri lalitali lomwe pamalo amene akufotokozedwawa panalibe. Komanso masomphenyawa angatanthauze kuti mtsinjewu unkalowera ku Nyanja Yakufa ndipo panalibe cholepheretsa chilichonse. Koma malinga ndi mmene dzikolo linalili zimenezinso zinali zosatheka.
b Akatswiri ena oikira ndemanga pa mawu a m’Baibulo, amaona kuti imeneyi ndi nkhani yabwino. Amanena kuti kwa nthawi yaitali kukumba mchere n’kumaugwiritsa ntchito poteteza zinthu kuti zisawonongeke inali bizinesi yaikulu ku Nyanja Yakufa. Koma mungaone kuti nkhaniyi ikunena mosapita m’mbali kuti madambo amenewo “sadzasintha nʼkukhala abwino.” Iwo adzakhala opanda moyo komanso sadzachiritsidwa chifukwa chakuti madzi opatsa moyo ochokera kunyumba ya Yehova sadzafika kumeneko. Choncho zikuoneka kuti pamene lembali likunena kuti madambowo adzakhala amchere, zikutanthauza kuti sadzakhala malo abwino.—Sal. 107:33, 34; Yer. 17:6.
c Mofanana ndi zimenezi, ganizirani fanizo la Yesu la khoka. Khoka limagwira nsomba zambiri koma si zonse zimene zimakhala “zabwino.” Nsomba zoipazo amangozitaya. Choncho Yesu anachenjeza kuti anthu ena amene alowa m’gulu la Yehova, pakapita nthawi, akhoza kusonyeza kuti ndi osakhulupirika.—Mat. 13:47-50; 2 Tim. 2:20, 21.