Kuchitiridwa Zoipa
Kodi tingamve bwanji ngati anthu ena akutichitira zinthu zoipa?
Sl 69:20; Miy 18:14; Mla 4:1-3; Mki 2:13-16; Akl 3:21
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Sa 10:1-5—Mfumu Davide anachita zinthu mokoma mtima kwambiri ndi asilikali ake ena omwe anachititsidwa manyazi ndi adani awo
2Sa 13:6-19—Tamara analira kwambiri mpaka kung’amba mkanjo wake chifukwa choti anachititsidwa manyazi Aminoni atamugwiririra
N’chiyani chimene chikusonyeza kuti Yehova amadziwa munthu wina akachitiridwa zinthu zoipa? Nanga adzachita zotani?
Yob 34:21, 22; Sl 37:8, 9; Yes 29:15, 19-21; Aro 12:17-21
Onaninso Sl 63:6, 7
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 25:3, 14-17, 21, 32-38—Nabala anachitira mwano Mfumu Davide ndipo zimenezi zinaika moyo wa anthu am’banja lake pangozi, kenako Yehova anamupha
Yer 20:1-6, 9, 11-13—Yeremiya anafooka wansembe wina dzina lake Pasuri atamumenya n’kumuika m’matangadza, koma kenako Yehova anamulimbikitsa n’kumupulumutsa