Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

Mulungu Apitirize Kukukondani

Mulungu Apitirize Kukukondani

“Podzilimbitsa pamaziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana, . . . pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.”​-YUDA 20, 21.

1, 2. Kodi tingatani kuti Mulungu apitirize kutikonda?

TONSEFE timafuna kukhala amphamvu komanso athanzi. Choncho timayesetsa kudya chakudya chabwino, kuchita masewera olimbitsa thupi ndiponso kusamalira thupi lathu. Ngakhale kuti kuchita zimenezi si kophweka, timapitirizabe chifukwa choganizira ubwino wake. Koma tikufunikanso kukhala olimba ndiponso athanzi mwa njira ina.

2 Ngakhale kuti pofika pano tayamba kale kumudziwa Yehova, tikufunika kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. Pamene Yuda ankawalimbikitsa Akhristu kuti “pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani,” anafotokozanso mmene angachitire zimenezi. Anawauza kuti ‘adzilimbitse pamaziko a chikhulupiriro chawo choyera kopambana.’ (Yuda 20, 21) Ndiye kodi ifeyo tingatani kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu?

PITIRIZANI KULIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU

3-5. (a) Kodi Satana amafuna kuti muziona bwanji mfundo za Yehova? (b) Kodi inuyo mumaona bwanji malamulo a Yehova ndiponso mfundo zake?

3 N’zofunika kuti panokha musamakayikire zoti zimene Yehova amatiuza n’zothandiza. Satana amafuna kuti muziganiza kuti mfundo zimene Mulungu amatipatsa n’zovuta kuzitsatira ndiponso kuti muziganiza zoti mungamasangalale kwambiri ngati mutamasankha nokha zomwe zili zabwino kapena zoipa. Kungoyambira m’munda wa Edeni, Satana wakhala akuyesetsa kuti anthu azikhulupirira zimenezi. (Genesis 3:1-6) Ndipo mpaka pano akuyesetsabe kuti anthu aziyendera maganizo amenewa.

4 Kodi n’zoona kuti malamulo a Yehova ndi opondereza? Ayi. Mwachitsanzo, tayerekezani kuti mukuyenda pamalo poti panadzalidwa maluwa okongola. Kenako mukuona kuti chigawo china cha malowo chinatchingidwa ndi mpanda wautali. Mwina mumtima mwanu mungadzifunse kuti, ‘Kodi anatchingiranji pamenepa?’ Koma nthawi yomweyo, mukumva mkango ukubangula mkati mwa mpandawo. Kodi mungaonebe kuti mpandawo ukukutchingirani kumene mumafuna kupita? Ayi, mungaone kuti mpandawo ndi wothandiza chifukwa ukukutetezani kuti musadyedwe ndi mkangowo. Mfundo za Yehova zili ngati mpanda umenewu, ndipo Mdyerekezi ali ngati mkango. Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”​—1 Petulo 5:8.

5 Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. Iye safuna kuti Satana atipusitse. N’chifukwa chake anatipatsa malamulo ndiponso mfundo zoti zizititeteza ndiponso kutithandiza kukhala osangalala. (Aefeso 6:11) Yakobo analemba kuti: “Woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala.”​—Yakobo 1:25.

6. Kodi n’chiyani chingatithandize kutsimikizira kuti malangizo a Yehova ndi othandiza kwambiri?

6 Tikamatsatira malangizo a Yehova zinthu zimayamba kutiyendera bwino pa moyo wathu ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba. Mwachitsanzo, zinthu zimatiyendera bwino tikamachita zimene amatiuza zoti tizipemphera kwa iye mosalekeza. (Mateyu 6:5-8; 1 Atesalonika 5:17) Timasangalala tikamatsatira zimene amatiuza kuti tizisonkhana pamodzi kuti tizimulambira ndiponso kulimbikitsana komanso tikamagwira nawo ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20; Agalatiya 6:2; Aheberi 10:24, 25) Tikamaganizira mmene zinthu zimenezi zatithandizira kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba, timatsimikiza kuti malangizo a Yehova ndi othandiza kwambiri.

7, 8. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamadere nkhawa za mayesero amene tingadzakumane nawo m’tsogolo?

7 Mwina tingamachite mantha kuti m’tsogolo tingadzakumane ndi zinthu zovuta kwambiri zoyesa chikhulupiriro chathu. Ngati mumamva choncho, muzikumbukira mawu a Yehova akuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”​—Yesaya 48:17, 18.

8 Tikamamvera Yehova mtendere wathu umakhala ngati mtsinje umene sumauma ndipo chilungamo chathu chimakhala ngati mafunde a m’nyanja omwe nthawi zonse amakhala akuyenda. Tidzakhala okhulupirika kwa Yehova mpaka kalekale ngakhale titakumana ndi zotani pa moyo wathu. Baibulo limalonjeza kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.”​—Salimo 55:22.

‘YESETSANI MWAKHAMA KUTI MUKHALE OKHWIMA MWAUZIMU’

9, 10. Kodi kukhala wokhwima mwauzimu kumatanthauza chiyani?

9 Mukamayesetsa kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, mudzakhala “okhwima mwauzimu.” (Aheberi 6:1) Kodi kukhala okhwima mwauzimu kumatanthauza chiyani?

10 Sikuti timakhala Akhristu okhwima mwauzimu chifukwa chakuti tinabadwa kalekale. Kuti tikhale okhwima mwauzimu, tiziyesetsa kuti Yehova akhale mnzathu wapamtima komanso tiziona zinthu mmene iye amazionera. (Yohane 4:23) Paulo analemba kuti: “Otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.” (Aroma 8:5) Munthu wokhwima mwauzimu samaika mtima wake wonse pa zinthu zosangalatsa kapena pa chuma. M’malomwake amaika maganizo ake onse potumikira Yehova ndipo amapanga zosankha zanzeru pa moyo wake. (Miyambo 27:11; werengani Yakobo 1:2, 3.) Samalola kuti akopeke ndi zinthu zimene zingam’pangitse kuchita zoipa. Munthu wokhwima mwauzimu amadziwa zinthu zomwe ndi zoyenera ndipo amatsimikiza mumtima mwake kuzichita.

11, 12. (a) Kodi Paulo ananena zotani zokhudza ‘mphamvu za kuzindikira’ za Mkhristu? (b) Kodi kukhala Mkhristu wokhwima mwauzimu n’kofanana bwanji ndi kukhala katswiri wothamanga?

11 Pamafunika khama kuti munthu ukhale wokhwima mwauzimu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu, amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” (Aheberi 5:14) Mawu akuti “kuphunzitsa” angatipangitse kuganiza za munthu yemwe akuphunzira masewera othamanga.

12 Tikaona katswiri wothamanga, timadziwa kuti zinamutengera nthawi komanso khama kuti akhale katswiri. Munthu sabadwa ali kale katswiri wa masewera enaake. Mwana akabadwa, amakhala asakudziwa mmene angagwiritsire ntchito mikono ndi miyendo yake. Koma m’kupita kwa nthawi amaphunzira kugwira zinthu komanso kuyenda. Ataphunzitsidwa, akhoza kukhala katswiri wothamanga. Mofanana ndi zimenezi, pamafunika nthawi ndiponso kudziphunzitsa kuti tikhale Akhristu okhwima mwauzimu.

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziganiza ngati mmene Yehova amaganizira?

13 M’bukuli takambirana zimene zingatithandize kumaganiza ngati mmene Yehova amaganizira ndiponso kumaona zinthu ngati mmene iyeyo amazionera. Taphunzira kufunika kotsatira ndiponso kukonda mfundo za Yehova. Tikamasankha zochita, timadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi lamulo kapena mfundo iti ya m’Baibulo imene ikugwirizana ndi nkhaniyi? Kodi ndingatsatire bwanji lamulo kapena mfundoyo? Kodi Yehova angakonde nditasankha chiyani?’​—Werengani Miyambo 3:5, 6; Yakobo 1:5.

14. Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu?

14 Nkhani yolimbitsa chikhulupiriro chathu ilibe malire. Mofanana ndi mmene kudya chakudya chopatsa thanzi kumalimbitsira thupi lathu, kuphunzira za Yehova kumatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Titangoyamba kuphunzira Baibulo, tinaphunzira mfundo zoyambirira zokhudza Yehova komanso zimene amafuna. Koma m’kupita kwa nthawi, timafunika kuphunzira mfundo zozama. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu.” Tikamagwiritsa ntchito zinthu zimene taphunzira, timakhala ndi nzeru. Baibulo limatiuza kuti: “Nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.”​—Miyambo 4:5-7; 1 Petulo 2:2.

15. Kodi kukonda Yehova komanso abale ndi alongo athu n’kofunika bwanji?

15 Munthu akhoza kukhala wamphamvu komanso wathanzi, koma kuti akhalebe choncho ayenera kupitirizabe kudzisamalira. Mofanana ndi zimenezi, munthu wokhwima mwauzimu amadziwa kuti amafunika kuyesetsa kuti apitirizebe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Paulo amatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro.” (2 Akorinto 13:5) Koma pamafunika zambiri kuposa kungokhala ndi chikhulupiriro cholimba. Chikondi chathu pa Yehova komanso abale ndi alongo athu chiyenera kupitiriza kukula. Paulo ananena kuti: “Ngati ndili ndi chikhulupiriro chonse choti n’kusuntha nacho mapiri, koma ndilibe chikondi, sindili kanthu.”​—1 Akorinto 13:1-3.

MAGANIZO ANU ONSE AKHALE PA ZIMENE TIKUYEMBEKEZERA

16. Kodi Satana amafuna kuti tizikhala ndi maganizo otani?

16 Satana amafuna zoti tiziganiza kuti ngakhale titayesetsa bwanji Yehova sangasangalale nafe. Iye amafuna kutigwetsa ulesi ndiponso amafuna kuti tiziganiza kuti mavuto athu sangathe. Samafuna kuti tizidalira Akhristu anzathu komanso kuti tizikhala osangalala. (Aefeso 2:2) Satana amadziwa kuti maganizo oti zinthu sizidzayendanso mpaka kalekale akhoza kutisokoneza komanso kusokoneza ubwenzi wathu ndi Mulungu. Koma Yehova watipatsa chinthu chimene chingatithandize kulimbana ndi maganizo olakwika amenewa. Iye watipatsa chiyembekezo.

17. Kodi chiyembekezo n’chothandiza bwanji?

17 Palemba la 1 Atesalonika 5:8, Baibulo limayerekezera chiyembekezo ndi chipewa cha msilikali chimene chimateteza mutu wake pa nthawi ya nkhondo. Limanena kuti chiyembekezo chimabweretsa chipulumutso. Kuyembekezera zimene Yehova anatilonjeza kungateteze maganizo athu ndiponso kungatithandize kuti tisamataye mtima.

18, 19. Kodi chiyembekezo chinamuthandiza bwanji Yesu?

18 Yesu anapirira zinthu zambiri chifukwa cha chiyembekezo chimene anali nacho. Usiku wake womaliza padziko lapansi pano anakumana ndi mavuto motsatizana. Mnzake yemwe ankayenda naye anam’pereka kwa adani. Mnzake wina anakana kuti sakumudziwa. Anzake ena anamusiya yekha n’kuthawa. Anthu akwawo komwe anamuukira ndipo ankafunitsitsa kuti aphedwe mwankhanza. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire zinthu zonsezi? Baibulo limati: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo. Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”​—Aheberi 12:2.

19 Yesu ankadziwa kuti akakhala wokhulupirika, achititsa kuti Atate ake alemekezedwe ndiponso asonyeza kuti Satana ndi wabodza. Chiyembekezo chimenechi chinamuthandiza kukhala wosangalala kwambiri. Ankadziwanso kuti pasanapite nthawi yaitali, abwereranso kumwamba n’kumakakhala ndi Atate ake. Zimenezi zinamuthandiza kupirira mavuto amene anakumana nawo. Mofanana ndi Yesu, nafenso tiyenera kuika maganizo athu onse pa chiyembekezo chathu. Chiyembekezo chimenechi chidzatithandiza kupirira ngakhale titakumana ndi mavuto otani.

20. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musataye mtima?

20 Yehova amaona mukamapirira komanso mukamamukhulupirira. (Yesaya 30:18; werengani Malaki 3:10.) Iye analonjeza kuti ‘adzakupatsani zokhumba za mtima wanu.’ (Salimo 37:4) Choncho, maganizo anu onse azikhala pa zinthu zimene mukuyembekezera. Satana amafuna kuti musiye kukhala ndi chiyembekezo ndiponso kuti muziona kuti zimene Yehova anatilonjeza sizidzachitika. Koma simuyenera kulola maganizo amenewa kukusokonezani. Mukangoona kuti mwayamba kukayikira zinthu zimene Yehova watilonjeza, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Muzikumbukira mawu a pa Afilipi 4:6, 7, akuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”

21, 22. (a) Kodi Yehova akufuna kuti dzikoli lidzakhale lotani? (b) Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani?

21 Muzipeza nthawi pafupipafupi yosinkhasinkha zinthu zosangalatsa zimene tikuyembekezera. Posachedwapa, aliyense azidzalambira Yehova. (Chivumbulutso 7:9, 14) Taganizirani mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Lidzakhala losangalatsa kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Satana ndi ziwanda zake ndiponso zinthu zina zonse zoipa zidzachotsedwa. Pa nthawi imeneyo simuzidzadwala kapena kumwalira. M’malomwake, tsiku lililonse muzidzadzuka wamphamvu komanso wosangalala. Tizidzagwira ntchito limodzi pokonza dzikoli kuti likhale lokongola kwambiri. Aliyense adzakhala ndi chakudya chabwino komanso malo abwino okhala. Anthu sadzakhala oipa mtima kapena ankhanza koma adzakhala okomerana mtima. M’kupita kwa nthawi, anthu onse padzikoli adzasangalala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​​—Aroma 8:21.

22 Yehova amafuna kuti muzimutenga ngati mnzanu wapamtima. Choncho, muziyesetsa kumumvera komanso kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye tsiku ndi tsiku. Tiyeni tonse tipitirize kuchita zinthu zimene zingachititse kuti Mulungu azitikondabe mpaka kalekale.​​—Yuda 21.