CHIGAWO 6
Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?
1. Malinga ndi Mawu a Mulungu, kodi mitundu iŵiri yokha ya zipembedzo ndi iti?
“LOŴANI pa chipata chopapatiza,” anatero Yesu, “chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Malinga ndi Mawu a Mulungu, pali mitundu iŵiri yokha ya zipembedzo basi: china choona, china chonyenga; china cholondola, china cholakwika; china chopita kumoyo, china chopita kuchiwonongeko.
2. Kodi Malemba akusonyeza bwanji kuti si zipembedzo zonse zimene zimasangalatsa Mulungu?
2 Anthu ena amaganiza kuti zipembedzo zonse zimasangalatsa Mulungu. Koma mavesi a m’Baibulo otsatiraŵa akusonyeza kuti zimenezi si zoona:
-
“Ana a Israyeli anawonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aastaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sihoni, ndi milungu ya Moabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anam’leka Yehova osam’tumikira. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli.” (Oweruza 10:6, 7) Ngati tilambira mafano kapena milungu ina m’malo mwa Mulungu woona, Yehova sadzatiyanja.
-
“Anthu aŵa andilemekeza Ine [Mulungu] ndi milomo yawo, koma mtima wawo ukhala kutali ndi ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Marko 7:6, 7) Ngati anthu amene amati amalambira Mulungu aphunzitsa maganizo awoawo m’malo mwa zimene Baibulo limaphunzitsa, kulambira kwawo kuli kwachabe ndipo Mulungu savomereza kulambira kumeneko.
-
“Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Kulambira kwathu kufunika kugwirizana ndi choonadi cha Mawu a Mulungu.
Zipatso za Chipembedzo Chonyenga
3. Kodi njira imodzi yosiyanitsa chipembedzo choona ndi chonyenga ndi iti?
3 Tingadziŵe bwanji kuti chipembedzo ichi chikusangalatsa Mulungu kapena sichikum’sangalatsa? Yesu anati: “Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa . . . Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.” Kunena kwina, ngati chipembedzo chichokera kwa Mulungu, chimabala zipatso zokoma; koma ngati chichokera kwa Satana, chimabala zoipa.—Mateyu 7:15-20.
4. Kodi ndi khalidwe liti limene olambira Yehova amasonyeza?
4 Chipembedzo choona chimakhala ndi anthu amene amakondana ndiponso amakonda ena. Zili choncho chifukwa Yehovayo ndi Mulungu wachikondi. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Kodi zipembedzo zikutsatira muyezo umenewu wa kulambira koona?—Yohane 13:35; Luka 10:27; 1 Yohane 4:8.
5. Kodi buku lina limafotokoza zotani pa malonda a akapolo mu Africa muno?
5 Taganizani za malonda a akapolo mu Africa muno. Buku lakuti The New Encyclopædia Britannica limati: “Aafirika pafupifupi 18,000,000 anagwidwa pamalonda a akapolo omwe Asilamu ankachita kudutsa chipululu cha Sahara ndi Indian Ocean kuyambira chaka cha 650 mpaka 1905. Chakumapeto kwa zaka za ma 1400 Azungu anayamba kuchita malondawo kugombe la kumadzulo
kwa Africa, ndipo mmene chaka cha 1867 chimafika n’kuti Aafirika kuyambira 7,000,000 mpaka 10,000,000 atatengedwa ukapolo kupita ku Dziko Latsopano.”6. Kodi chipembedzo chinachita zotani pa malonda a akapolo?
6 Kodi zipembedzo zinati chiyani nthaŵi ya chipwirikiti imeneyi mu Africa muno pamene amuna, akazi, ndi ana anawakhwatula kuwachotsa kwawo ndi kwa achibale, atawamanga maunyolo, kuwasindikiza ndi zitsulo zamoto, ndi kuwagula ndi kuwagulitsa ngati ng’ombe? Bethwell Ogot analemba mu Daily Nation ya ku Nairobi, ku Kenya kuti: “M’Chikristu ndi m’Chisilamunso amakhulupirira kuti anthu afunika kugwirizana, koma [m’zipembedzo] ziŵirizi ndi mmenenso munachokera anthu ogwira akapolo omwe analimbikitsa kusankhana mafuko. . . . Tivomereze kuti onse Asilamu ndi Akristu, mayiko a Kumadzulo ndi a ku Middle East ali ndi mlandu, ndipo ananyalanyaza khalidwe loipa limene linachititsa Aafirika kuzunzika koopsa zaka mazana ambiri.”
Chipembedzo pa Nkhondo
7. Kodi atsogoleri a zipembedzo achita zotani pa nkhondo?
7 Chipembedzo chonyenga chaonetsa zipatso zake zoipa m’njira zinanso. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Baibulo limati “uzikonda mnzako,” atsogoleri a zipembedzo kuzungulira dziko lonse lapansi athandiza ndi kulimbikitsa nkhondo.—Mateyu 22:39.
8. (a) Kodi atsogoleri a zipembedzo analimbikitsa bwanji kuphana pankhondo za mu Africa muno? (b) Kodi pasitala wina anati chiyani za atsogoleri a zipembedzo ku Nigeria nthaŵi ya nkhondo yachiŵeniŵeni?
8 Zikudziŵika bwino kuti chaka cha 1994, avirigo ena ndi ansembe anathandiza kupha anthu ku Rwanda. Zipembedzo zatenganso mbali m’nkhondo zina mu Africa muno. Mwachitsanzo, pankhondo yachiŵeniŵeni imene inapha anthu miyandamiyanda ku Nigeria, zipembedzo
kumbali zonse zinalimbikitsa anthu kumenya nkhondo. Pamene nkhondoyo inali kupitiriza, pasitala wina anati atsogoleri a matchalitchi anali “ataiŵala ntchito imene Mulungu anawapatsa.” Anawonjeza kuti: “Ife amene tikuti ndife atumiki a Mulungu tasanduka atumiki a Satana.”9. Kodi Baibulo limati chiyani za atumiki a Satana?
9 Zimene Baibulo limanena zikufanana kwambiri ndi zimenezi. Limati: “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo.” (2 Akorinto 11:14, 15) Mofanana ndi mmene anthu ambiri oipa amadzionetsera ngati anthu abwino, Satana amanyenga anthu mwa kugwiritsa ntchito atsogoleri a zipembedzo amene amaoneka ngati olungama koma ntchito zawo n’zoipa ndipo zipatso zawo n’zoola.
10. Kodi atsogoleri a zipembedzo am’kana bwanji Mulungu?
10 Kuzungulira dziko lonse lapansi, atsogoleri a zipembedzo alalikira za chikondi, mtendere, ndi ubwino, koma achita chidani, nkhondo, ndi zoipa. Baibulo limafotokoza bwino za iwo. Limati: “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo am’kana Iye.”—Tito 1:16.
Tulukani mu ‘Babulo Wamkulu’
11. Kodi Baibulo limati chiyani pofotokoza chipembedzo chonyenga?
11 Titha kuona mmene Yehova amaganizira za chipembedzo chonyenga mwa kuŵerenga buku la Chivumbulutso m’Baibulo. Mmenemo akufotokoza chipembedzo chonyenga monga mkazi wophiphiritsa, ‘Babulo Wamkulu.’ (Chivumbulutso 17:5) Taonani mmene Mulungu akufotokozera mkaziyo:
-
“Mkazi wachigololo wamkulu . . . amene mafumu a dziko anachita chigololo naye.” (Chivumbulutso 17:1, 2) M’malo mokhulupirika kwa Mulungu, chipembedzo chonyenga chaloŵerera m’ndale, ndipo chimauza maboma zoti achite.
-
“Momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.” (Chivumbulutso 18:24) Chipembedzo chonyenga chazunza ndi kupha atumiki okhulupirika a Mulungu ndipo chaphetsa anthu mamiliyoni m’nkhondo.
-
‘Anadzichitira ulemu, nadyerera.’ (Chivumbulutso 18:7) Chipembedzo chonyenga chili ndi chuma chambiri chimene atsogoleri ake amadyerera.
-
“Ndi nyanga [yake] mitundu yonse inasokeretsedwa.” (Chivumbulutso 18:23) Chifukwa cha chiphunzitso chake chonama chakuti mzimu umapulumuka imfa, chipembedzo chonyenga chatsegulira mpata mtundu uliwonse wa zokhulupirira mizimu ndi matsenga ndipo chalimbikitsa kuopa akufa ndi kulambira makolo.
12. Kodi Baibulo limapereka chenjezo lotani pa chipembedzo chonyenga?
12 Pochenjeza anthu zolimba kuti achoke m’chipembedzo chonyenga, Baibulo limati: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”—Chivumbulutso 18:4, 5.
13. Kodi chimene chidzachitikira chipembedzo chonyenga ndi anthu ake n’chiyani?
13 M’tsogolo muno, Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, adzawonongedwa psiti. Baibulo limati: “Miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu woweruza ndiye wolimba.” (Chivumbulutso 18:8) Kuti tisalandireko miliri yake, tifunika kulekeratu kugwirizana ndi chipembedzo chonyenga. Tilekeretu kuchita miyambo yake, zikondwerero zake, ndi kusiyiratu zikhulupiriro zake chifukwa zonsezi Mulungu sakondwera nazo. Zimenezi n’zofunika kuchita mwamsanga. Moyo wathu uli pachiswe!—2 Akorinto 6:14-18.