CHIGAWO 7
Kodi Amene Ali ndi Chipembedzo Choona Ndani?
1. Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tisangalatse Mulungu?
NGATI tikufuna kuti Mulungu akhale bwenzi lathu lapamtima, tifunika kupeŵeratu chipembedzo chonyenga. Tifunika kutsata chipembedzo choona. Lerolino anthu mamiliyoni kuzungulira dziko lonse lapansi akuchita zimenezi.
2. Kodi Mboni za Yehova zingapezeke kuti, ndipo zimachita ntchito yotani?
2 Malinga ndi zimene Baibulo linalosera, olambira oona amapanga “khamu lalikulu” lomwe lachokera “mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) M’mayiko okwana 235, Mboni za Yehova mamiliyoni zikukangalika kuthandiza anthu kudziŵa njira zachikondi za Yehova ndi zofuna zake.
Kudziŵa Olambira Oona
3. Kodi Mboni zimalambira ndani, ndipo zimapeŵa kulambira kotani?
3 Mboni zimakhulupirira kuti Yehova yekha ndiye amene tiyenera kum’lambira. Zimakana kugwadira mafano kapena zithunzithunzi zachipembedzo. (1 Yohane 5:21) Sizichitira akufa ulemu mwa kuchezera pamaliro kapena kuchita miyambo ina imene imalimbikitsa zikhulupiriro zonama za chipembedzo ndi “maphunziro a ziŵanda.” (1 Timoteo 4:1) Komabe, zimatonthoza mtima ofedwa mwa kuwafotokozera zimene Mulungu walonjeza kuti kudzakhala kuuka kwa akufa m’paradaiso padziko lapansi.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
4. Kodi anthu a Mulungu amawaona bwanji matsenga?
4 Mboni zimapeŵeratu matsenga kapena ufiti chifukwa zimadziŵa kuti zinthu zimenezi zimachokera kwa Mdyerekezi. Sizidalira matsenga pofuna chitetezo koma zimadalira Yehova.—Miyambo 18:10.
5. Kodi Mboni za Yehova sizili ‘za dziko lapansi’ m’njira yotani?
5 Yesu anati ophunzira ake sadzakhala “a dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Ngakhale Yesu anakana kuloŵa m’ndale zimene zinaliko masiku akewo. (Yohane 6:15) Mboninso siziloŵa m’ndale, zilibe mzimu wokonda dziko la munthuwe, ndipo siziloŵerera pa mikangano ya mafuko a dzikoli. Komabe, zimakhoma misonkho ndipo zimamvera malamulo a dziko limene zikukhala.—Yohane 15:19; Aroma 13:1, 7.
6. Kodi atumiki a Mulungu amatsata malangizo otani a ukwati ndi chisudzulo?
6 Chifukwa chakuti Mboni zimatsata malangizo a boma, zimaonetsetsa kuti zalembetsa maukwati awo. (Tito 3:1) Zimamvera malangizo a Mulungu, ndipo zimapeŵa mitala. (1 Timoteo 3:2) Ndiponso, popeza atumiki a Mulungu amatsata mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino, si kaŵirikaŵiri kuti maukwati awo amatha n’kusudzulana.
7. Kodi Mboni zimasonyezana bwanji chikondi wina ndi mnzake?
7 Mboni zimakondana. Chifukwa cha chikondi chimenechi, kuphatikizapo kukonda kwawo Mulungu, zimagwirizana pamodzi kupanga ubale weniweni, ngakhale kuti zachokera m’mafuko ndi mayiko ambiri. Pakachitika tsoka kapena ngati pakufunika thandizo, Mboni sizizengereza kuthandizana. Zimasonyeza chikondi ndi mmene zimakhalira.—Yohane 13:35.
8. Kodi anthu a Mulungu amapeŵa ntchito zoipa ziti?
8 Anthu a Yehova amayesetsa kukhala oona mtima ndi olungama pamoyo wawo. Sakuba, sanama, sachita chiwerewere, saledzera, ndipo amapeŵa chinyengo pantchito kapena pamalonda. Amuna samenya akazi awo. Ena asanakhale Mboni anali kuchita zimenezi koma anasiya pothandizidwa ndi Yehova. ‘Anayeretsedwa’ malinga ndi kuona kwa Mulungu.—1 Akorinto 6:9-11.
Ochita Chifuniro cha Mulungu
9. Kodi buku lina linati chiyani za matchalitchi auzimu mu Africa muno?
9 Inde, zipembedzo zambiri zimati zili ndi choonadi. Zimachita ntchito zozizwitsa pofuna kutsimikiza zonena zawo. Mwachitsanzo, buku lina linafotokoza za amene amati matchalitchi auzimu mu Africa muno kuti: “Makamaka [magulu atsopano achikristu] atenga ntchito ya amatsenga kapena asing’anga. . . . Amati atha kunenera ndi kuchita zozizwitsa. Aneneri awo amafotokoza masomphenya ndi kumasulira maloto. Amagwiritsa ntchito madzi oyera, mafuta opatulika, phulusa, makandulo ndi zonunkhira pochiritsa ndi poteteza matenda.”
10, 11. Kodi n’chifukwa chiyani zimene amati zozizwitsa masiku ano si umboni wakuti chipembedzocho chachokera kwa Mulungu?
10 Anthu m’zipembedzo zimenezi amati zozizwitsa zimatsimikiza kuti chipembedzo chawo n’chodalitsidwa ndi Mulungu. Koma zimene amati zozizwitsazo si umboni wakuti chipembedzo chawo Yehova amachiyanja. Satana amapatsa olambira ena onyenga mphamvu yochita ‘zamphamvu.’ (2 Atesalonika 2:9, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Ndiponso, Baibulo linalosera kuti mphatso yochita zozizwitsa yochokera kwa Mulungu, monga kulosera, kulankhula m’malilime, ndi nzeru zapadera, “idzakhala chabe.”—1 Akorinto 13:8.
11 Yesu anachenjeza kuti: “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.”—Mateyu 7:21-23.
12. Adzaloŵa Ufumu wakumwamba ndani?
12 Nanga adzaloŵa Ufumu wakumwamba ndani? Ndi aja amene amachita chifuniro cha Yehova.
Olalikira Ufumu wa Mulungu
13. Kodi ntchito imene Mulungu akulamula anthu ake kuchita masiku ano ndi iti, ndipo akuchita ntchito imeneyi ndani?
13 Kodi chifuniro cha Mulungu kwa anthu ake masiku ano n’chiyani? Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Iyi ndi ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita mwachangu.
14. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndipo adzalamulira mu Ufumuwo ndani?
14 Kuzungulira “padziko lonse lapansi,” Mboni za Yehova zikulengeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba limene lidzalamulira dziko lonse lapansi m’chilungamo. Zimaphunzitsa kuti Yehova wasankha Kristu Yesu kukhala Mfumu ya Ufumuwo, limodzi ndi olamulira anzake okwanira 144,000 osankhidwa mwa anthu.—Danieli 7:14, 18; Chivumbulutso 14:1, 4.
15. Kodi Ufumuwo udzawononga chiyani?
15 Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito Baibulo kusonyeza anthu kuti Ufumu wa Mulungu udzawononga dziko lonse la Satana. Udzawononganso chipembedzo chonyenga limodzi ndi ziphunzitso zake zimene, m’malo molemekeza Mulungu, zimalemekeza Mdyerekezi! (Chivumbulutso 18:8) Maboma onse aumunthu otsutsa Mulungu adzawonongedwanso!—Danieli 2:44.
16. Kodi Kristu Yesu adzalamulira ndani, ndipo iwo adzakhala kuti?
16 Ndiponso, Mboni za Yehova zimadziŵitsa anthu kuti Kristu Yesu adzapereka madalitso kwa onse ochita zimene Mulungu amafuna. Yesuyo adzawalamulira padziko lapansi. Baibulo limalonjeza kuti: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”—Salmo 72:12, 13.
17. Kodi ndani okha amene akulengeza Ufumu wa Mulungu?
17 Kulibe gulu linanso la anthu limene limachita chifuniro cha Mulungu mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Ndi Mboni za Yehova zokha zimene zikudziŵitsa Ufumu wa Mulungu kuzungulira dziko lonse lapansi.