Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 8

Siyani Chipembedzo Chonyenga; Tsatani Chipembedzo Choona

Siyani Chipembedzo Chonyenga; Tsatani Chipembedzo Choona

1. Pankhani ya kulambira, kodi anthu afunika kusankha chiyani masiku ano?

YESU anati: “Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine.” (Mateyu 12:30) Tili kumbali ya Yehova kapena ya Satana. Anthu ambiri amaganiza kuti akutumikira Mulungu movomerezeka, koma Baibulo limati Satana ali “wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Anthu mamiliyoni amakhulupirira kuti akulambira Mulungu, koma kwenikweni akutumikira Satana Mdyerekezi! Anthu masiku ano afunika kusankhapo chimodzi: Kutumikira Yehova, “Mulungu wa choonadi,” kapena Satana, “atate wake wa bodza.”​—Salmo 31:5; Yohane 8:44.

Masukani ku Chipembedzo Chonyenga

2. Kodi ina mwa njira zimene Satana amayesera kuletsa anthu kulambira Yehova ndi iti?

2 Mukasankha kutumikira Yehova, ndiye kuti mwasankha bwino chifukwa Mulungu adzakuyanjani. Koma Satana sasangalala ena akamatumikira Mulungu; amawadzetsera mavuto. Ina mwa njira zimene iye amachitira zimenezi ndi kusonkhezera ena, ngakhale mabwenzi athu ndi achibale, kutinyodola kapena kutikaniza. Yesu anachenjeza kuti: “Apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.”​—Mateyu 10:36.

3. Ngati achibale anu kapena mabwenzi akuletsani kulambira Mulungu, kodi inu mudzatani?

3 Kodi zimenezi zikakuchitikirani mudzatani? Anthu ambiri akudziŵa kuti kalambiridwe kawo n’kolakwa, koma akuzengereza kusiya. Amaganiza kuti akatero ndiye kuti ali osakhulupirika kwa achibale awo. Kodi zimenezo ndi nzeru? Inuyo mukanadziŵa kuti achibale anu anali kumwa mankhwala osokoneza bongo, kodi simukanawachenjeza kuti mankhwalawo adzawapweteka? Simukanagwirizana nawo n’kumamwera limodzi mankhwalawo, mukanatero ngati?

4. Nthaŵi imene Yoswa anali moyo anawauza chiyani Aisrayeli pankhani ya kulambira?

4 Yoswa analimbikitsa Aisrayeli kusiya kapembedzedwe kolakwika ndi miyambo ya makolo awo. Anati: “Tsopano, opani Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m’Aigupto; nimutumikire Yehova.” (Yoswa 24:14) Yoswa anali wokhulupirika kwa Mulungu, ndipo Yehova anam’dalitsa. Tikakhala okhulupirika kwa Yehova, adzatidalitsa ifenso.​—2 Samueli 22:26.

Onongani Zonse Zogwiritsidwa Ntchito pa Kulambira Konyenga

5. N’chifukwa chiyani tifunika kuwononga zinthu zonse zamatsenga?

5 Kumasuka ku chipembedzo chonyenga kumafunanso kuti tiwononge zinthu zonse zamatsenga zimene tingakhale nazo, monga zithumwa, mphinjiri, mphete zamatsenga ndi makoza, ndi zinthu zina ngati zimenezi. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri chifukwa kumasonyeza kuti tikudalira Yehova ndi mtima wathu wonse.

6. Kodi Akristu oyambirira anatani nawo mabuku awo a zamatsenga?

6 Nazi zimene Akristu ena oyambirira anachita atasankha kutsata chipembedzo choona. Baibulo limati: “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse.”​—Machitidwe 19:19.

7. Tingachite chiyani ngati ziŵanda zikutivutitsa?

7 Ena amene amayamba kutumikira Yehova ndipo m’mbuyomu akhala akuchita ufiti kapena zamatsenga, ziŵanda zingawavutitse. Zikakuchitikirani zimenezo, itanani Yehova mofuula popemphera, kutchula dzina lakelo ndipo iye adzakuthandizani.​—Miyambo 18:10; Yakobo 4:7.

8. Kodi Akristu amaona motani mafano ndi zithunzithunzi zogwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga?

8 Amene akufuna kutumikira Yehova asasunge kapena kugwiritsa ntchito fano kapena chithunzithunzi chilichonse chogwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga. Akristu oona ‘amayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe.’ (2 Akorinto 5:7) Amalemekeza lamulo la Mulungu loletsa kugwiritsa ntchito fano lamtundu uliwonse polambira.​—Eksodo 20:4, 5.

Gwirizanani ndi Anthu a Yehova

9. Kodi Baibulo limapereka langizo lotani ngati munthu akufuna kukhala wanzeru?

9 Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.” (Miyambo 13:20) Ngati tikufuna kukhala anzeru, tifunika kuyenda, kapena kugwirizana, ndi Mboni za Yehova. Anthu ameneŵa ndiwo akuyenda panjira ya kumoyo.​—Mateyu 7:14.

10. Kodi Mboni za Yehova zingakuthandizeni bwanji kutumikira Mulungu?

10 Mboni zimasamaladi anthu. Cholinga cha ntchito yawo ndi kuthandiza anthu oona mtima kumvetsa mfundo za choonadi cha m’Baibulo chopatsa moyo wosatha. Mboni zingakuthandizeni mwa kuphunzira nanu Baibulo kwaulere. Zidzakuthandizani kuyankha mafunso anu ndi kukusonyezani mmene mungagwiritsire ntchito nzeru ya m’Baibulo pamoyo wanu.​—Yohane 17:3.

11. Kodi misonkhano yachikristu idzakuthandizani bwanji?

11 Kumisonkhano yawo, imene nthaŵi zambiri imachitikira ku Nyumba ya Ufumu, mudzaphunzira zambiri ponena za njira za Yehova. Chikhumbo chanu chotsata chipembedzo choona chidzalimba. Ndipo mudzaphunziranso mmene mungathandizire ena kudziŵa mfundo za choonadi cha m’Baibulo.​—Ahebri 10:24, 25.

12. Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji kutumikira Mulungu?

12 Popitiriza kuphunzira zambiri za chifuniro ndi cholinga cha Yehova, mosakayika mudzamvetsa ndi kuyamikira kwambiri njira zake zachikondi. Ndiponso, chikhumbo chanu chochita zokondweretsa Mulungu ndi kupeŵa zosam’kondweretsa chidzakula. Kumbukirani kuti mutha kulankhula ndi Yehova m’pemphero kum’pempha kuti akuthandizeni kuchita chabwino ndi kupeŵa choipa.​—1 Akorinto 6:9, 10; Afilipi 4:6.

Kodi mufunika kuchita chiyani kuti mutsate kulambira koona?

13. Kodi mufunika kuchita chiyani kuti mukondweretse mtima wa Yehova?

13 M’kupita kwa nthaŵi, pamene mukukula mwauzimu, simudzalephera kuona kuti mufunika kukhala Mboni yodzipatulira ndi yobatizidwa ya Yehova. Mwa kugwirizana ndi anthu ake, mudzakondweretsa mtima wa Yehovayo. (Miyambo 27:11) Mudzakhala pakati pa anthu osangalala amene Mulungu amati za iwo: “Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga.”​—2 Akorinto 6:16.