Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 3

Mwamuna ndi Mkazi Oyamba

Mwamuna ndi Mkazi Oyamba

KODI chosiyana n’chiani m’chithunzi’chi? Ndicho anthu’wo. Ndiwo mwamuna ndi mkazo oyamba. Kodi anawapanga ndani? Ndiye Mulungu. Kodi mukudziwa dzina Lake? Ndiro Yehova. Ndipo iwo anachedwa Adamu ndi Hava.

Yehova anapanga Adamu motere. Anatenga dothi lapansi naumba nalo thupi langwiro, la munthu wamwamuna. Anauzira mpweya m’mphuno mwake, Adamu nakhala wamoyo.

Yehova anali ndi ntchito yoti Adamu achite. Anauza Adamu kucha maina zinyama zonse. Adamu angakhale atapenda zinyama’zo kwa nthawi yaitali kuti azisankhire maina abwino kwambiri. Pocha maina zinyama’zo iye anayamba kuona kanthu kena. Kotani?

Zinyama zonse zinali ziwiriziwiri. Panali njobvu zamphongo ndi zazikazi, mikango yamphongo ndi yaikazi. Koma Adamu analibe mnzake. Chotero Yehova anam’goneka tulo tatikulu, nachotsa nthiti yake imodzi. Nthiti’yo Yehova anaipanga mkazi wa Adamu.

Ha, ndi wokondwa chotani m’mene analiri Adamu tsopano! Ganizani m’mene Hava anakondwera kuikidwa m’munda wokongola’wo! Tsopano akanatha kubala ana ndi kukhala pamodzi mwachimwemwe.

Yehova anafuna kuti iwo akhale ndi moyo kosatha. Anafuna kuti iwo akongoletse dziko lonse ngati munda wa Edene’wo. Ha, ndi okondwera nawo chotani nanga m’mene analiri Adamu ndi Hava! Kodi mukanakonda kukongoletsa nawo dziko lapansi? Koma chimwemwe chao sichinakhalitse. Tiyeni tione chifukwa chake.