Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 101

Yesu Akuphedwa

Yesu Akuphedwa

TAONANI chinthu choopsya chimene chikuchitika’cho! Yesu akuphedwa. Iwo am’khomera pa mtengo. Misomali yakhomeredwa m’manja ndi mapazi ake. Kodi ali yense akafuniranji kuchitira izi Yesu?

N’chifukwa chakuti anthu ena amada Yesu. Kodi mukuwadziwa? Mmodzi wa iwo ndiye mngelo woipa Satana Mdierekezi. Ndiye amene anachititsa Adamu ndi Hava kusamvera Yehova. Ndipo Satana ndiye amene anachititsa adani a Yesu kuchita upandu woopsya’wo.

Ngakhale Yesu asanakhomeredwe pa mtengo’wu, adani ake akum’chitira zinthu zankhanza. Mukukumbukira m’mene anadzera kumunda wa Getsemane nam’tenga kumka naye? Kodi adani’wo anali yani? Iwo anali atsogoleri achipembedzo. Eya, tiyeni tione chimene chikuchitika kenako.

Pamene Yesu akutengedwa ndi atsogoleri achipembedzo’wo, atumwi ake akuthawa. Akusiya Yesu yekha ndi adani ake, chifukwa chakuti akuopa. Koma mtumwi Petro ndi Yohane sakupita patali. Iwo akutsatira kuti aone zimene zikuchitikira Yesu.

Ansembe akumka naye kwa Anasi, amene anali mkulu wa ansembe. Khamu’lo silikukhalitsa pano. Kenako akumka ndi Yesu ku nyumba ya Kayafa, amene tsopano ali mkulu wa ansembe. Atsogoleri achipembedzo ambiri asonkhana pa nyumba yake.

Pano pa nyumba ya Kayafa akuweruza. Anthu akulowetsedwamo kudzanamizira Yesu. Atsogoleri achipembedzo’wo onse akunena kuti: ‘Yesu ayenera kuphedwa.’ Ndiyeno akum’labvulira, ndi kum’menya makofi.

Pamene zonse’zi zikuchitika, Petro ali pabwalo panjapo. Ndi usiku wozizira, ndipo chotero anthu’wo akoleza moto. Pamene akuotha pa motopo, mdzakazi wina akuyang’ana Petro, nati: ‘Munthu’yu anali’nso ndi Yesu.’

‘Ai, sindinali naye!’ akutero Petro.

Katatu anthu’wo akunena za Petro kuti anali ndi Yesu. Koma nthawi iri yonse iye akunena kuti si zoona. Kachitatu kamene Petro akunena izi, Yesu akutembenuka nam’yang’ana. Petro akumva chisoni kwambiri chifukwa cha kunena mabodza’wa, ndipo akuchoka nalira.

Pamene dzuwa likukwera Lachisanu m’mawa, ansembe akumka ndi Yesu ku malo ao osonkhanira, Sanhedrini. Munomo akukambitsirana zimene adzam’chitira. Iwo akumka naye kwa Pontiyo Pilato, wolamulira wa chigawo cha Yudeya.

‘Uyu ndi munthu woipa,’ ansembe’wo akuuza choncho Pilato. ‘Ayenera kuphedwa.’ Atafunsa Yesu mafunso, Pilato akunena kuti: ‘Sindikuona kuti iye wachita cholakwa.’ Ndiyeno Pilato akutumiza Yesu kwa Herode Antipa. Herode ndi wolamulira wa Galileya, koma iye amakhala m’Yerusalemu. Herode sakuona kuti Yesu wachita cholakwa chiri chonse, chotero akum’bwezera kwa Pilato.

Pilato akufuna kumasula Yesu. Koma adani a Yesu akufuna mkaidi wina kumasulidwa m’malo mwake. Munthu’yu ndi mbala. Tsopano ukufika usana pamene Pilato akutulutsira panja Yesu. Iye akuti kwa anthu’wo: ‘Onani! mfumu Yanu!’ Koma akulu ansembe akupfuula kuti: ‘M’chotseni! M’pheni! M’pheni!’ Chotero Pilato akumasula Baraba, ndipo akutenga Yesu kumka kukam’pha.

Kuchiyambi kwa Lachisanu masana Yesu akukhomeredwa pa mtengo. Simungawaone pa chithunzi’cho, koma pa mbali iri yonse ya Yesu mpandu akuphedwera’nso pa mtengo. Yesu atangotsala pang’ono kufa, mmodzi wa apandu’wo akuti kwa iye: ‘Mundikumbukire pamene mulowa mu ufumu wanu.’ Ndipo Yesu akuyankha kuti: ‘Ndikulonjeza kuti udzakhala ndi ine m’Paradaiso,’

Kodi izi si zodabwitsa? Kodi mukudziwa paradaiso amene Yesu anali kum’nena? Kodi Paradaiso woyamba amene Mulungu anapanga anali kuti? Inde, pa dziko lapansi. Ndipo pamene Yesu alamulira monga mfumu kumwamba, adzaukitsa munthu’yu kudzasangala ndi Paradaiso watsopano pa dziko lapansi. Kodi sitingakhale achimwemwe ndi izi?