Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 80

Anthu a Mulungu Atuluka m’Babulo

Anthu a Mulungu Atuluka m’Babulo

PAFUPI-FUPI zaka ziwiri zapitapo chigonjetsedwere Babulo ndi Amedi ndi Aperisi. Ndipo onani zimene zikuchitika tsopano! Aisrayeli akuchoka ku Babulo. Kodi anamasuka motani? Ndani akuwalola kupita?

Koresi, mfumu ya Perisiya ndiyo. Kale-kale Koresi asanabadwe, Yehova anachititsa mneneri wake Yesaya kulemba za iye kuti: ‘Udzachita zimene ndikufuna kuti uchite. Zipata zidzakhala chitsegukire kuti ulande mzinda’wo.’ Ndipo Koresi anatsogolera m’kulanda Babulo. Amedi ndi Aperisi analowa mu mzinda’wo usiku kulowera pa zipata zimene zinasiyidwa zosatseka.

Koma mneneri wa Yehova Yesaya ananena’nso kuti Koresi adzalamulira kuti Yerusalemu ndi kachisi wake zimangidwe’nso. Kodi Koresi anapereka lamulo limene’li? Inde. Nazi zimene iye akuuza Aisrayeli: ‘Pitani, tsopano, ku Yerusalemu ndi kukamanga kachisi wa Yehova, Mulungu wanu.’ Ndipo ndizo zimene Aisrayeli akumka kukachita.

Koma si Aisrayeli onse m’Babulo akatha kuyenda ulendo wautali wobwerera ku Yerusalemu’wo. Ndi ulendo wautali kwambiri wa mamailo pafupi-fupi 500 (makilomita 800) ndipo ambiri ngokalamba kapena odwala kwambiri kosati n’kuyenda kutali. Ndipo pali zifukwa zina zimene ena sakumkera. Koresi akuuza awo amene sakumka kuti: ‘Patsani siliva ndi golidi ndi mphatso zina awo amene akubwerera kukamanga Yerusalemu ndi kachisi wake.’

Chotero mphatso zambiri zikuperekedwa kwa iwo amene akubwerera ku Yerusalemu. Ndipo’nso, Koresi akuwapatsa mbale ndi zikho zimene Nebukadinezara anazitenga m’kachisi pamene anaononga Yerusalemu. Anthu’wo ali ndi zinthu zonyamula zochuluka pobwerera.

Atayenda kwa pafupi-fupi miyezi inai, iwo akufika ku Yerusalemu pa nthawi yake. Zangokwana zaka 70 chiyambire pamene mzinda’wo unaonongedwa, ndipo dziko’lo linasiyidwa labwinja kotheratu. Koma ngakhale Aisrayeli abwerera ku dziko lakwao adzakhala ndi nthawi zobvuta, monga momwe tidzaonera.