Mutu 3
Amene Anapanga Zinthu Zonse
PALI kanthu kena kochititsa chidwi kamene ndimakadziŵa. Kodi ufuna ukamve?— Tayang’ana dzanja lako. Pinda zala zako. Tsopano tola china chake. Dzanja lako lingachite zinthu zambiri, ndipo limachita bwino. Kodi ndani amene anapanga manja athu?—
Inde, ndi Munthu yemweyo amene anapanga pakamwa pathu, mphuno zathu, ndi maso athu. Mulungu, Atate ake a Mphunzitsi Waluso, ndiye anapanga zimenezi. Kodi sitisangalala kuti Mulungu anatipatsa maso?— Timatha kuona zinthu zambirimbiri chifukwa choti tili ndi maso. Timaona maluŵa. Timaona udzu wobiriŵira ndi kumwamba kowala. Timathanso kuona timbalame tikudya, monga ngati iti tili pachithunzichi. Ndithu, ndi zodabwitsa kuti timatha kuona zinthu moteremu. Kodi iwenso ukuganiza choncho?—
Koma ndani amene anapanga zinthu zimenezi? Kodi ndi anthu anazipanga? Ayi. Anthu amapanga nyumba. Koma palibe munthu amene angapange udzu womera. Anthu sangapange mwana wa mbalame, maluŵa, kapenanso chinthu chilichonse chamoyo. Kodi umadziŵa zimenezi?—
Mulungu ndiye anapanga zinthu zonsezi. Mulungu anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. Anapanganso anthu. Analenga munthu wamwamuna woyambirira ndiponso munthu wamkazi woyambirira. Mphunzitsi Waluso, Yesu, anaphunzitsa zimenezi.—Mateyu 19:4-6.
Kodi Yesu anadziŵa bwanji kuti Mulungu anapanga munthu wamwamuna ndi wamkazi? Kodi Yesu anamuona Mulungu akuwapanga?— Inde anamuona. Yesu anali ndi Mulungu pamene Mulungu anali kupanga anthuwo. Yesu ndiye anali woyambirira weniweni kupangidwa ndi Mulungu. Yesu anali mngelo, ndipo anali kukhala kumwamba ndi Atate ake.
Baibulo limatiuza kuti Mulungu ananena kuti: “Tipange munthu.” (Genesis 1:26) Kodi ukuganiza kuti Mulungu anali kulankhula ndi ndani?— Anali kulankhula ndi Mwana wake uja amene anabwera padziko lapansi natchedwa kuti Yesu.
Zimenezitu ndi zosangalatsa, kodi si choncho? Tangoganiza, tikamamvera zimene Yesu anena, timakhala tikuphunzitsidwa ndi munthu amene anali ndi Mulungu pamene Mulungu anali kupanga dziko lapansi ndi zinthu zonse zili m’dzikoli! Yesu anaphunzira zambiri pogwira ntchito limodzi ndi Atate ake kumwamba. Ndi zosadabwitsa kuti Yesu ndi Mphunzitsi Waluso!
Kodi ukuganiza kuti Mulungu sanali kusangalala chifukwa chakuti anali yekhayekha asanapange Mwana wake?— Ayi, anali kusangalala. Ndiye ngati iye anali kusangalala, n’chifukwa chiyani anapanga zinthu zamoyo zina?— Anachita zimenezi chifukwa chakuti iye ndi Mulungu wachikondi. Anafuna kuti enanso azisangalala ndi moyo. Tiyenera kuyamikira Mulungu potipatsa moyo.
Chilichonse chimene Mulungu anachita chimaonetsa chikondi chake. Mulungu anapanga dzuŵa. Dzuŵa limatipatsa kuwala komanso kukazizira timamva kufunda. Pakanakhala palibe dzuŵa, chilichonse chikanakhala chozizira komanso padziko lapansi sipakanakhala chinthu chamoyo. Kodi iwe susangalala kuti Mulungu anapanga dzuŵa?—
Mulungu amachititsanso mvula kugwa. Nthaŵi zina mvula sungaikonde chifukwa ikamagwa umalephera kukaseŵera. Komatu mvula imathandiza kuti maluŵa azikula. Ndiye tikaona maluŵa okongola, kodi tiyenera kuyamika ndani?— Mulungu. Nanga ndani amene tiyenera kumuyamika tikamadya zipatso ndiponso ndiwo zamasamba zokoma?— Tiyenera kuyamika Mulungu popeza kuti zinthu zimakula chifukwa cha dzuŵa lake ndi mvula imene iye amagwetsa.
Tiyerekeze kuti munthu wina wakufunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anapanga anthu ndi nyama zomwe?’ Iwe ungayankhe bwanji?— Ee ungalondole kunena kuti: “Inde, Mulungu anapanga anthu ndi nyama zomwe.” Koma bwanji ngati wina sakhulupirira kuti Mulungu anapangadi anthu? Bwanji ngati iye anena kuti anthu anachokera ku nyama? Baibulo siliphunzitsa zimenezo. Limati Mulungu analenga zinthu zonse zamoyo.—Genesis 1:26-31.
Koma munthu wina angakuuze kuti sakhulupirira Mulungu. Ndiyeno iwe ungati chiyani?— Bwanji osamulozera nyumba? Ndiye umufunse kuti: “Kodi ndani anapanga nyumba iyo?” Aliyense amadziŵa kuti inapangidwa ndi winawake. Ndithudi nyumbayo sinadzipange yokha!—Ahebri 3:4.
Kenako pita naye kumene kuli maluŵa.
Mufunse kuti: “Ndani anapanga maluŵa aŵa?” Sanapangidwe ndi munthu aliyense. Tsono monga mmene nyumba ija sinadzipange yokha, maluŵa aŵanso sanadzipange okha. Anapangidwa ndi winawake. Mulungu ndiye anawapanga.Uza munthuyo kuti akhale kaye chete ndipo amve kulira kwa mbalame. Ndiyeno mufunse kuti: “Ndani anapanga mbalame ndi kuziphunzitsa kulira?” Mulungu. Mulungu ndiye anapanga kumwamba ndi dziko lapansi ndiponso zinthu zonse zamoyo! Iye ndiye amene amapereka moyo.
Komatu munthu wina anganene kuti amakhulupirira zinthu zimene amaziona zokha. Iye anganene kuti: ‘Ngati chinthucho sindichiona, sindingachikhulupirire.’ Motero anthu ena amati sakhulupirira Mulungu chifukwa chakuti samuona.
Ndi zoona kuti Mulungu sitingamuone. Baibulo limati: ‘Palibe Munthu angaone Mulungu.’ Palibe munthu wamwamuna, wamkazi, kapena mwana aliyense padziko lapansi amene angaone Mulungu. Choncho anthu sayenera kujambula chithunzi kapena kupanga chinthu chofanizira Mulungu. Mulungu mwini wakeyo amatiuza kuti tisapange zinthu zomufanizira. Motero Mulungu sangasangalale ngati tili ndi zinthu zimenezi m’nyumba mwathu.—Eksodo 20:4, 5; 33:20; Yohane 1:18.
Koma ngati Mulungu sitingamuone, kodi timadziŵa bwanji kuti alikodi? Taganizira izi. Kodi mphepo ukhoza kuiona?— Ayi. Palibe amene angaone mphepo. Koma ukhoza kuona zinthu zimene mphepo imachita, monga kugwedezeka kwa masamba mphepo ikafika pamtengo. Ndipotu umakhulupirira kuti mphepo iliko.
Zinthu zimene Mulungu anapanga ukhozanso kuziona. Ukaona maluŵa omera kapena mbalame yamoyo, umaona zinthu zimene Mulungu anapanga. Choncho umakhulupirira kuti Mulungu alikodi.
Munthu wina angakufunse kuti, ‘Kodi ndani anapanga dzuŵa ndi dziko lapansi?’ Baibulo limati: “Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko Genesis 1:1) Inde, Mulungu anapanga zinthu zodabwitsa zonsezi! Kodi iwe ukuganizapo bwanji pamenepa?—
lapansi.” (Kukhala ndi moyo ndi kokondweretsa kwambiri, kodi si choncho? Timamva mbalame zikuimba mosangalatsa. Timaona maluŵa ndi zinthu zina zimene Mulungu anapanga. Ndipo timadya chakudya chimene Mulungu watipatsa.
Tiyenera kuyamikira Mulungu chifukwa cha zinthu zonsezi. Mwa zonse, tiyenera kumuyamikira kwambiri chifukwa chotipatsa moyo. Ngati Mulungu timamuyamikiradi, tiyenera kuchitapo kanthu. Ukuganiza tidzachita chiyani?— Tidzamumvera, ndipo tidzachita zimene amatiuza m’Baibulo. Tikachita zimenezi tidzasonyeza kuti timamukonda Amene anapanga zinthu zonse.
Tiyenera kuyamikira Mulungu pa zonse zimene wachita. Tingatero motani? Ŵerengani zimene zalembedwa pa Salmo 139:14; Yohane 4: