Mutu 34
Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?
PAJA ukudziŵa kuti anthu masiku ano amakalamba, kudwala, ndi kufa. Ngakhale ana ena amafa. Kodi uyenera kuopa imfa kapena aliyense amene wamwalira?— Kodi ukudziŵa chimene chimachitika anthufe tikamwalira?—
Palibe munthu wamoyo masiku ano amene anafapo kenako ndi kuuka kuti atiuze za akufa. Koma pamene Yesu, Mphunzitsi Waluso, anali padziko lapansi pano, munthu wotero analipo. Tingadziŵe zimene zimachitika kwa omwalira mwa kuŵerenga za munthuyo. Iye anali bwenzi la Yesu ndipo anali kukhala ku Betaniya, mudzi waung’ono pafupi ndi Yerusalemu. Dzina lake linali Lazaro, ndipo anali ndi alongo ake aŵiri, omwe mayina awo anali Marita ndi Mariya. Tiye tione kuti Baibulo limati chiyani pofotokoza zimene zinachitika.
Tsiku lina Lazaro anadwala kwambiri. Panthaŵiyo, Yesu anali kutali. Chotero Marita ndi Mariya anatuma munthu wina kuti akauze Yesu kuti mlongo wawo, Lazaro, akudwala. Anachita zimenezi podziŵa kuti Yesu akafika, angachiritse mlongo wawoyo. Yesu sanali dokotala, koma anali ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu ndipo anali kuchiritsa nthenda ya mtundu uliwonse.—Mateyu 15:30, 31.
Yesu asanapite kwa Lazaro kukamuona, Lazaro uja anadwala kwambiri mpaka kumwalira. Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti Lazaro wagona ndipo Iye akupita kukamuutsa. Ophunzira aja sanadziŵe zimene Yesu anali kutanthauza. Choncho Yesu anawauza mosabisa kuti: “Lazaro wamwalira.” Kodi zimenezi zikutiuza chiyani za imfa?— Eya, zikutiuza kuti imfa ili ngati kugona tulo tatikulu. Tulo
take timakhala tatikulu kwambiri moti munthu salota ngakhale pang’ono.Ndiye Yesuyo ananyamuka kupita kwa Marita ndi Mariya. Mabwenzi awo ambiri anali atafika kale. Iwo anabwera kukatonthoza azimayi ameneŵa chifukwa cha imfa ya mlongo wawo. Marita atamva kuti Yesu akubwera, anatuluka kuti akakumane naye. Sipanatenge nthaŵi ndipo Mariya nayenso anatuluka kuti akaone Yesu. Anali ndi chisoni chachikulu ndipo anali kulira. Atafika kwa Yesu, anagwada pamaso pake. Mabwenzi ena amene anali kutsatira Mariya analinso kulira.
Mphunzitsi Waluso anawafunsa kumene anaika Lazaro. Atamva zimenezo, anthu aja anaperekeza Yesu kumanda kumene anaika Lazaro. Yesu ataona anthu onse akulira, iyenso anayamba kulira. Anali kudziŵa mmene zimapwetekera ngati munthu amene umamukonda wamwalira.
Pamandapo panali mwala, choncho Yesu anati: ‘Chotsani mwalawo.’ Kodi anayenera kuuchotsadi?— Marita sanaganize kuti ndi nzeru yabwino imeneyo. Choncho anati: “Ambuye, adayamba kununkha; pakuti wagona masiku anayi.”
Koma Yesu anati kwa iye: “Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?” Yesu anatanthauza kuti zimene Marita adzaona zidzalemekeza Mulungu. Kodi Yesu anachita chiyani? Iwo atachotsapo mwala uja, Yesu anapemphera mokweza mawu kwa Yehova. Kenako Yesu anafuula kuti: “Lazaro, tuluka”! Kodi iye anatuluka? Ukuganiza bwanji?—
Kodi iwe ungamuutse munthu amene akugona?— Inde, ukamuitana mokweza, angauke. Koma kodi ungamuutse munthu amene wagona mu imfa?— Iyayi. Kaya ufuule bwanji pomuitana, wakufayo sadzamva. Sikutheka ineyo kapena iweyo kapenanso munthu wina
aliyense padziko lapansi pano kuukitsa munthu wakufa masiku ano.Koma Yesu amasiyana ndi ife. Iye ali ndi mphamvu zapadera zochokera kwa Mulungu. Chotero pamene Yesu anaitana Lazaro, panachitika zodabwitsa. Munthu uja amene anali wakufa masiku anayi anatuluka m’manda! Anakhalanso wamoyo! Anayambanso kupuma, kuyenda, ndi kulankhula! Inde, Yesu anaukitsa Lazaro kwa akufa.—Yohane 11:1-44.
Ndiye ukaganiza, ungati ndi chiyani chinachitikira Lazaro atamwalira? Kodi mbali yake ina—kapena kuti mzimu wake—unatuluka m’thupi lake kukakhala kwinakwake? Kodi mzimu wa Lazaro unapita kumwamba? Kodi masiku anayiwo iye anali wamoyo kumwambako limodzi ndi Mulungu ndi angelo oyera?—
Iyayi. Ukukumbukira kuti Yesu ananena kuti Lazaro anali m’tulo. Kodi chimachitika ndi chiyani ngati uli m’tulo? Ukagona tulo tatikulu, sudziŵa zimene zikuchitika, kodi umadziŵa ngati?— Ndipo
ukadzuka, sudziŵa kuti wagona nthaŵi yaitali bwanji mpaka utayang’ana wotchi.Ndi mmenenso akufa alili. Iwo sadziŵa kalikonse. Samva chilichonse. Ndipo sangachite chilichonse. Ndi mmenenso Lazaro analili pamene anali wakufa. Imfa ili ngati tulo tatikulu pamene munthu sakumbukira kalikonse. Baibulo limanena kuti: “Akufa sadziŵa kanthu bi.”—Mlaliki 9:5, 10.
Taganizanso izi: Ngati Lazaro anali kumwamba masiku anayi amenewo, kodi sakananenapo za kumwambako?— Ndipo akanakhala kumwamba, kodi Yesu akanamuchotsa ku malo abwino ngati amenewo kubwerera padziko lapansi pano?— Sakanatero ayi!
Komabe, anthu ambiri amanena kuti tili ndi mzimu umene umakhalabe ndi moyo thupi likafa. Iwo amanena kuti mzimu wa Lazaro unali ndi moyo kwinakwake. Koma Baibulo silinena zimenezo. Limanena kuti Mulungu anapanga munthu woyamba Adamu kukhala munthu “wamoyo.” Baibulo limanenanso kuti Adamu atachimwa, anafa. Iye anakhala wakufa ndipo sanadziŵe kanthu kalikonse. Anabwerera ku dothi limene anapangidwako. Baibulo limanenanso kuti ana a Adamu onse analandira uchimo ndi imfa.—Genesis 2:7; 3:17-19; Aroma 5:12.
Choncho, ndi zoonekeratu kuti tilibe mzimu umene umachoka m’thupi ndi kupitiriza kukhalabe ndi moyo. Ife tonse ndife anthu amoyo. Ndipo popeza kuti anthu analandira uchimo kwa munthu woyamba, Adamu, Baibulo limanena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.”—Anthu ena amaopa akufa. Iwo sangapite pafupi ndi manda chifukwa chakuti amaganiza kuti mizimu ya akufa imachoka m’matupi awo ndipo ingapweteke amoyo. Koma kodi munthu wakufa angapweteke wamoyo?— Ayi, sangatero.
Anthu ena amakhulupirira kuti akufa angabwerenso ngati mizimu kudzaona amoyo. Choncho amasungira akufawo chakudya. Koma anthu amene amachita zimenezo sakhulupiriradi zimene Mulungu amanena za akufa. Ngati ife timakhulupirira zimene Mulungu amanena, sitidzaopa akufa. Ndipo ngati tili ndi mtima woyamika Mulungu chifukwa chotipatsa moyo, tidzasonyeza zimenezo mwa kuchita zimene Mulunguyo amafuna.
Koma mwina ungafunse kuti: ‘Kodi Mulungu adzaukitsa ana amene anamwalira ndi kuwapatsanso moyo? Kodi iye amafuna kuchitadi zimenezo?’ Tiye tikambiranenso nkhani imeneyi.
Tiye tiŵerengenso malemba ena m’Baibulo ofotokoza za mmene akufa alili, pa Salmo 115:17 ndi Salmo146:3, 4.