Mutu 45
Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Chiyani? Zimene Tingachite Posonyeza Kuti Tikuufuna
KODI pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake ukulidziŵa?— Ngati sukulidziŵa, tiye tiŵerengere limodzi m’Baibulo pa Mateyu 6:9-13. Mu pempheroli, lomwe anthu ambiri amalitcha Pemphero la Ambuye, muli mawu aŵa akuti: “Ufumu wanu udze.” Kodi ukudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ndi chiyani?—
Chabwino, mfumu ndi munthu amene amalamulira dziko kapena dera linalake. Ndipo ulamuliro wa mfumuyo, kapena kuti boma lake, umatchedwa ufumu. Mu mayiko ena munthu wamkulu kwambiri mu boma amamutcha pulezidenti. Nanga Wolamulira wa boma la Mulungu amatchedwa ndani?— Amatchedwa kuti Mfumu. Ndi chifukwa chake boma la Mulungu limatchedwa kuti Ufumu.
Kodi ukumudziŵa amene Yehova Mulungu anasankha kukhala Mfumu
ya boma Lake?— Anasankha Mwana wake, Yesu Kristu. Kodi ndi chifukwa chiyani iye ali wolamulira wabwino kuposa wina aliyense amene anthu angasankhe?— Ndi chifukwa chakuti Yesu amakonda kwambiri Atate ake, Yehova. Choncho iye nthaŵi zonse amachita zinthu zabwino.Kalekale Yesu asanabadwe ku Betelehemu, Baibulo linanena za kubadwa kwake ndipo linati adzakhala Wolamulira amene Mulungu adzasankha. Tiye tiŵerenge nkhaniyi pa Yesaya 9:6, 7. Pamati: ‘Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wa mtendere. Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.’
Palembali, Yesu monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu akutchedwa “Kalonga.” Iye alinso Mwana wa Mfumu Yaikulu, Yehova. Ndiye Yehova waikanso Yesu kukhala Mfumu ya boma Lake, lomwe lidzalamulira dziko lapansi kwa zaka wanisauzande. (Chivumbulutso 20:6) Yesu atabatizidwa, anayamba “kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.”—Mateyu 4:17.
Kodi ukuganiza kuti ndi chifukwa chiyani Yesu ananena kuti Ufumu unali utayandikira?— Chinali chifukwa chakuti Mfumu yake, imene pambuyo pake idzalamulira ili kumwamba, inali nawo pomwepo! Ndi chifukwa chaketu Yesu anauza anthu kuti: ‘Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.’ (Luka 17:21) Kodi ungasangalale kuyandikana kwambiri ndi Mfumu ya Yehova mpaka iwe kumatha kuigwira?—
Tsono tandiuza, kodi Yesu anabwera padziko lapansi kudzagwira ntchito yofunika iti?— Yesu anayankha funso limeneli kuti: ‘Ndiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.’ (Luka 4:43) Yesu anadziŵa kuti sangalalikire madera onse yekha. Ndiye ukuganiza kuti anachita chiyani?—
Mateyu 10:5, 7) Kodi Yesu anangophunzitsa ntchitoyi atumwi ake okha? Ayi, Baibulo limanena kuti Yesu anaphunzitsanso anthu ena ambiri kuti adziŵe kulalikira. M’kupita kwa nthaŵi, anatumiza ophunzira ena 70 ali aŵiriaŵiri kuti atsogole kumene iye anali kudzafikako. Kodi iwo anaphunzitsa anthu chiyani?— Yesu anawauza kuti: ‘Muziwauza kuti, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.’ (Luka 10:9) Mwa njira imeneyi anthu anaphunzira za boma la Mulungu.
Yesu anali kuyenda ndi anthu ena ndipo anawasonyeza mmene angachitire ntchito yolalikirayo. Oyamba amene anawaphunzitsa anali anthu 12 aja omwe anawasankha kukhala atumwi ake. (Kalekalelo mu Israyeli, mafumu atsopano anali kuloŵa m’mudzi atakwera pa mwana wa bulu kuti anthu awaone. Izi ndi zimene anachita Yesu pamene anafika ku Yerusalemu kwa nthaŵi yomaliza. Waonatu, Yesu anali kudzakhala Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. Koma kodi anthu anafuna kuti iye akhale Mfumu yawo?—
Eya, pamene anali kupita, anthu ambiri anayamba kuyala zovala zawo mu njira kutsogolo kwake. Ena anali kudula nthambi za mitengo ndi kumaika panjirapo. Mwa kuchita zimenezi anasonyeza kuti anali kufuna Yesu kukhala Mfumu yawo. Anali kufuula kuti: ‘Yolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye’! Koma si onse amene anakondwera. Moti atsogoleri ena achipembedzo mpaka anauza Yesu kuti: ‘Auzeni ophunzira anu akhale chete.’—Luka 19:28-40.
Patapita masiku faifi, Yesu anamangidwa ndipo anapita naye kunyumba yachifumu kuti akaonekere kwa nduna ija Pontiyo Pilato. Adani ake a Yesu ananena kuti Yesuyo akuti ndi mfumu ndipo akutsutsana ndi boma la Roma. Ndiye Pilato anafunsa Yesu za nkhaniyi. Yesu anakana kuti sakufuna kulanda bomalo. Anauza Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.”—Yohane 18:36.
Kenako Pilato anapita panja ndi kuuza anthu kuti wapeza kuti Yesu alibe mlandu. Koma apa anthuwo sanafune Yesu kukhala Mfumu yawo. Sanafune kuti iye amasulidwe. (Yohane 18:37-40) Pilato atalankhulanso ndi Yesu, anatsimikiza kuti Yesu sanalakwe ngakhale pang’ono. Motero pomalizira pake, atatulutsa Yesu panja komaliza, Pilato ananena kuti: “Taonani, Mfumu yanu!” Koma anthuwo anakuwa kuti: ‘Muchotseni, muchotseni, mupachikeni Iye!’
Ndiyeno Pilato anawafunsa kuti: “Ndipachike Mfumu yanu kodi?” Ansembe aakulu anayankha kuti: “Tilibe Mfumu koma Kaisara.” Koma mpaka pamenepo? Ansembe oipawo ananyengerera anthu kuti akane Yesu!—Yohane 19:1-16.
Mmene zinthu zilili masiku ano sizikusiyana ndi mmene zinalili nthaŵiyo. Anthu ambiri safuna kuti
Yesu akhale Mfumu yawo. Amanena kuti amakhulupirira Mulungu, komatu safuna kuti Mulungu kapena Kristu aziwauza zochita. Amafuna maboma awoawo padziko lapansi pompano.Nanga bwanji ifeyo? Pamene taphunzira za Ufumu wa Mulungu ndi zinthu zonse zabwino zimene Ufumuwo udzachita, kodi timamva bwanji mumtimamu tikaganiza za Mulungu?— Timamukonda, si choncho?— Ndiyeno, kodi Mulungu tingamusonyeze bwanji kuti timamukonda ndiponso kuti tikufuna kuti Ufumu wake uzitilamulira?—
Mulungu tingamusonyeze zimene zili mumtima mwathu mwa kutengera chitsanzo cha Yesu. Kodi paja Yesu anachita chiyani posonyeza kuti anali kukonda Yehova?— ‘Ndimachita zinthu zomukondweretsa nthaŵi zonse,’ anafotokoza tero Yesu. (Yohane 8:29) Inde, Yesu anabwera padziko lapansi ‘kudzachita zimene Mulungu amafuna’ ndi “kutsiriza ntchito yake.” (Ahebri 10:7; Yohane 4:34) Tatiye tione zimene Yesu anachita asanayambe ntchito yake yolalikira.
Yesu anapita kwa Yohane Mbatizi kumtsinje wa Yordano. Ataloŵa m’madzimo, Yohane anamiza Yesu yense m’madziwo kenako ndi kumutulutsa. Kodi ukudziŵa chifukwa chake Yohane anabatiza Yesu?—
Ndi chifukwa chakuti Yesu anauza Yohane kuti amubatize. Koma kodi tikudziŵa bwanji kuti Mulungu anafuna kuti Marko 1:9-11.
Yesu abatizidwe?— Tikudziŵa chifukwa chakuti Yesu atatuluka m’madzi muja anamva mawu a Mulungu kuchokera kumwamba akuti: “Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.” Mulungu anatumizanso mzimu wake woyera womwe unaoneka monga nkhunda kuti ufike pa Yesu. Choncho mwa kubatizidwa Yesu anasonyeza kuti anafuna kutumikira Yehova moyo wake wonse, inde, mpaka kalekale.—Tsonotu iwe udakali kukula. Koma kodi ukadzakula udzachita chiyani?— Kodi udzakhala ngati Yesu ndi kubatizidwa?— Uyenera kuchita zimene iye anachita, chifukwa Baibulo limanena kuti anakusiyira ‘chitsanzo kuti ukalondole mapazi ake.’ (1 Petro 2:21) Ukadzabatizidwa, udzasonyeza kuti ukufunadi kulamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Komabe kubatizidwa kokha si kokwanira.
Tifunika kumvera zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa. Yesu ananena kuti sitifunika kukhala ‘mbali ya dziko.’ Ngati tichita nawo zinthu za dzikoli, kodi tinganene kuti tikumumveradi? Yesu ndi atumwi ake sanachite nawo zinthu za dzikoli. (Yohane 17:14) Koma kodi anali kuchita chiyani?— Anali kuuza anthu ena za Ufumu wa Mulungu. Imeneyi ndiyo inali ntchito yaikulu pamoyo wawo. Kodi ifenso tikhoza kuchita zimenezi?— Inde, ndipo tidzachitadi zimenezi ngati zomwe timanena popemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndizo zimene timafunadi.
Onaninso malemba ena aŵa amene amatiuza zimene tingachite kuti tisonyeze kuti tikufuna Ufumu wa Mulungu ubwere: Mateyu 6: