Mutu 17
Mmene Tingakhalire Osangalala
TONSE timafuna kukhala osangalala, ndi choncho eti?— Koma si anthu onse amene akusangalala. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Ndi chifukwa chakuti sakudziŵa chinsinsi cha mmene angakhalire osangalala. Amaganiza kuti angasangalale ngati ali ndi zinthu zambiri. Komabe ngakhale apeze zinthuzo, sasangalala nthaŵi yaitali.
Nachi chinsinsi chofunikiracho. Mphunzitsi Waluso anati: ‘Kupatsa kumasangalatsa kuposa kulandira.’ (Machitidwe 20:35) Ndiye ukuganiza kuti chofunika ndi chiyani kuti tikhale osangalala?— Inde, chofunika ndi kupatsa ena ndiponso kuchitira ena zinthu. Kodi iwe unali kudziŵa zimenezi?—
Tiye tiganizire zimenezi kwambiri. Kodi Yesu anati munthu amene amalandira mphatso sangasangalale?— Ayi, iye sanatero. Iwe umafuna kulandira mphatso, eti?— Aliyensetu amafuna. Timasangalala tikalandira chinthu chabwino kwa ena.
Koma Yesu ananena kuti munthu amasangalala kwambiri akamapatsa anthu ena zinthu. Ndiye ukuganiza kuti ndi munthu uti amene wakhala akupatsa ena zinthu zambiri kuposa wina aliyense?— Eya, ndi Yehova Mulungu.
Baibulo limanena kuti Mulungu ‘amapatsa anthu onse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.’ Amatipatsa mvula kuchokera kumwamba ndi kuŵala kwa dzuŵa kuti mbewu zikule bwino ndi cholinga choti tikhale ndi chakudya. (Machitidwe 14:17; 17:25) Ndicho chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wosangalala’! (1 Timoteo 1:11, NW) Mulungu amasangalala chifukwa chakuti amapatsa ena zinthu. Ndipo pamene ife tipatsa ena zinthu, tingakhalenso osangalala.
Tsopano, kodi ifeyo tingapatse anthu ena chiyani? Kodi iwe unganene kuti tingawapatse chiyani?— Nthaŵi zina pamafunika kuti ukhale ndi ndalama kuti uthe kupereka mphatso. Ngati ili mphatso yokagula kusitolo, ungafunike kulipira ndalama. Chotero ngati ukufuna kupereka mphatso ya mtundu wotere, mwina udzafunika kusunga ndalama zambiri kuti ugule mphatsoyo.
Komatu si mphatso zonse zimene zimagulidwa kusitolo. Mwachitsanzo, pamene kwatentha kwambiri madzi ozizira angakhaletu abwino zedi kwa munthu amene ali ndi ludzu. Ndiyeno pamene ukupereka mphatso yotere kwa munthu waludzuyo, ungakhale wosangalala chifukwa cha kupatsa kwakoko.
Mwina iweyo ndi amayi ako tsiku lina mungaphike mandasi. Zimenezo zingakhaletu zabwino kwambiri. Koma kodi ungachite chiyani ndi ena mwa mandasiwo kuti usangalale kwambiri kusiyana ndi kudya wekha onsewo?— Eya, ungapatuleko ena kuti upatse anzako. Kodi ungakonde kuchita zimenezo nthaŵi ina?—
Mphunzitsi Waluso ndi atumwi ake anadziŵa kuti kupatsa kumasangalatsa. Kodi ukudziŵa chimene iwo anapatsa anthu ena?— Chinali chinthu chapamwamba kwambiri kuposa chilichonse padziko lapansi! Iwo anadziŵa choonadi chonena za Mulungu, ndipo anasangalala kwambiri kuuza ena uthenga wabwinowo. Iwo sanafune kuti wina aliyense awapatse ndalama chifukwa chomuuza uthenga wabwino.
Tsiku lina mtumwi Paulo ndi mnzake wapamtima Luka, yemwenso anali wophunzira wa Yesu, anakumana ndi mayi wina amenenso anafuna kukhala wosangalala popatsa ena zinthu. Iwo anakumana ndi mayi ameneyu kumtsinje. Paulo ndi Luka anapita kumeneko chifukwa anamva kuti anali malo opempherera. Ndipo atafika pamalowo, anapezadi akazi akupemphera.
Paulo anayamba kuuza akazi ameneŵa uthenga wabwino wa Yehova Mulungu ndi Ufumu wake. Mmodzi wa akaziwo dzina lake linali Lidiya, ndipo anamvetsera mwachidwi kwambiri. Kenako, Lidiya anafuna kuchita kanthu kenakake kosonyeza kuti anasangalala kwambiri ndi uthenga wabwino umene anamvawo. Ndiyeno mkaziyo anakakamiza Paulo ndi Luka nati: ‘Ngati mwandiona kuti ine ndine wokhulupirika kwa Ambuye, tiyeni ku nyumba yanga, mukagone kumeneko.’ Ndipo mkaziyo anawaumiriza mpaka anapita naye kunyumba kwake.—Machitidwe 16:13-15.
Lidiya anasangalala kwambiri kukhala ndi atumiki a Mulungu ameneŵa m’nyumba mwake. Iye anawakonda chifukwa anamuthandiza kuphunzira za Yehova ndi Yesu ndiponso mmene anthu angakhalire kosatha. Lidiya anasangalala kwambiri chifukwa chakuti anapatsa chakudya Paulo ndi Luka ndiponso anawapatsa malo ogona. Motero, iye anasangalala chifukwa chakuti anali kufunadi kuwachitira zimenezo. Imeneyi ndi mfundo yofunikatu kumaikumbukira nthaŵi zonse. Munthu wina angatiuze kuti tipereke mphatso. Koma ngati ife sitikufuna, kupatsa koteroko sikungatisangalatse.
Mwachitsanzo, bwanji ngati iweyo uli ndi masuwiti amene ukufuna kudya, ndiyeno ine ndikukuuza kuti upatseko mnzako masuwitiwo, kodi ukanapereka mosangalala?— Nanga bwanji utakhala kuti uli ndi masuwiti
ndiyeno wakumana ndi mnzako amene umamukonda kwambiri? Iweyo utati waganiza wekha zomupatsako mnzakoyo, kodi sungasangalale?—Nthaŵi zina munthu wina timamukonda kwambiri moti timafuna kumupatsa chilichonse chimene tili nacho, ife eni osadzisiyirako kalikonse. Ndi mmene tiyenera kuonera Mulungu pamene tikupitiriza kumukonda kwambiri.
Mphunzitsi Waluso anali kudziŵa mkazi wina wosauka amene anali ndi maganizo oterowo. Iye anaona mkaziyo mu kachisi ku Yerusalemu. Mkaziyo anali ndi tindalama tiŵiri tokha basi. Koma iye anaika tindalama tiŵiri tonseto mu bokosi la zopereka monga mphatso ya pa kachisi. Panalibe munthu amene anamuuza kuti achite zimenezo. Ndiponso anthu ena omwe analipo panthaŵiyo sanadziŵe zimene mkaziyo anachita. Iye anachita zimenezo chifukwa chakuti anali wofunitsitsa kupereka mphatsoyo ndiponso anakondadi Yehova. Ndipo iye anasangalala.—Luka 21:1-4.
Palitu zinthu zambiri zimene ife tingapatse ena. Kodi ungaganize zina mwa izo?— Ngati tipatsa ena zinthu chifukwa chakuti tikufunadi kuwapatsa, tidzasangalala. Ndi chifukwa chake Mphunzitsi Waluso amatiuza kuti: ‘Khalani opatsa.’ (Luka 6:38) Ngati ife tichita zimenezi, tidzasangalatsa anthu ena. Ndipotu ife tidzasangalala kuposa onse!
Tiye tiŵerengenso za mmene kupatsa kumasangalatsira. Zimenezi zili pa Mateyu 6: