Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 32

Mmene Yesu Anatetezedwera

Mmene Yesu Anatetezedwera

NTHAŴI zina Yehova amachita zinthu modabwitsa pofuna kuteteza ana ndiponso anthu ena amene sangathe kudziteteza. Ngati utati ukuyenda mu tchire ukhoza kuona njira imodzi imene Yehova amachitira zimenezi. Koma poyamba sungazindikire chimene chikuchitika.

Ungaone mbalame ikutera pansi pafupi nawe. Ingaoneke ngati yapweteka. Phiko limodzi lingakhale ngati ndi lothyoka, koma uona kuti ukati ufike pafupi iyo ikuthaŵira patali. Ukamailondola, iyo ingamangokuthaŵabe. Kenako ungoona kuti yauluka. Phiko lake lija linali labwinobwino! Kodi ukudziŵa chimene mbalameyo inali kuchita?—

Eya, cha paja mbalameyo inatera pafupi nawe panali ana ake mu udzu atabisala. Iyo inaopa kuti anawo uwaona ndi kuwapweteka. Ndi chifukwa chake imayerekezera kuti yapweteka ndi kukupititsa kutali ndi anawo. Kodi ukudziŵa amene angatiteteze mofanana ndi mmene mbalame imatetezera ana ake?— Baibulo limanena kuti Yehova ali ngati mbalame yotchedwa mphungu, yomwe imathandiza ana ake.—Deuteronomo 32:11, 12.

Kodi mbalame iyi ikuteteza ana ake motani?

Mwana wofunika kwambiri wa Yehova ndi Yesu, yemwe amamukonda kwambiri. Yesu ali kumwamba anali munthu wauzimu wamphamvu monga Atate ake. Anali kudzisamalira yekha. Koma pamene Yesu anabadwa kukhala mwana wakhanda padziko lapansi, sakanatha kudzithandiza. Anafunika kutetezedwa.

Kuti akwaniritse zimene Mulungu anafuna kuti iye achite padziko lapansi, Yesu anafunika kukula ndi kukhala munthu wamkulu wangwiro. Komabe Satana anayesa kupha Yesu adakali wamng’ono. Nkhani yosimba za kufuna kupha Yesu ali mwana ndiponso mmene Yehova anamutetezera ndi yochititsa chidwi kwambiri. Kodi ukufuna kuimva?—

Patapita nthaŵi yochepa Yesu atabadwa, Satana anachititsa chomwe chinaoneka monga nyenyezi kuwala kumwamba m’madera a Kum’maŵa. Okhulupirira nyenyezi, omwe ndi anthu amene amafufuza za nyenyezi, analondola nyenyeziyo mtunda wa makilomita mahandiredi ambiri kukafika ku Yerusalemu. Ku Yerusalemuko anafunsa malo amene anabadwira yemwe adzakhale mfumu ya Ayuda. Atafunsa amuna odziŵa zimene Baibulo limanena pankhaniyi, anawayankha kuti: “Mu Betelehemu.”—Mateyu 2:1-6.

Okhulupirira nyenyezi atafika kwa Yesu, kodi Mulungu anawachenjeza chiyani chomwe chinapulumutsa Yesu?

Herode, amene anali mfumu yoipa ya ku Yerusalemu, anamva za mfumu yatsopanoyi yomwe inali itabadwa kumene mu mudzi woyandikana nawo wa Betelehemu. Atamva zimenezi, Herode anauza okhulupirira nyenyezi aja kuti: ‘Pitani mukamufunefune mwanayo mumupeze, kenako mubwere mudzandiuze.’ Kodi ukudziŵa chifukwa chake Herode anafuna kudziŵa kumene angapeze Yesu?— Ndi chifukwa chakuti Herode anachita nsanje ndipo anafuna kumupha!

Kodi Mulungu anamuteteza bwanji Mwana wake?— Eya, okhulupirira nyenyezi aja atamupeza Yesu, anamupatsa mphatso. Pambuyo pake Mulungu anachenjeza okhulupirira nyenyeziwo kudzera m’maloto kuti asapitenso kwa Herode. Choncho iwo anadzera njira ina pobwerera kwawo osadutsanso ku Yerusalemu. Herode atazindikira kuti okhulupirira nyenyezi anabwerera kwawo, anakwiya kwambiri. Pofuna kupha Yesu ndithu, Herode ananena kuti ana onse aamuna ku Betelehemu a zaka zosapitirira ziŵiri aphedwe! Koma panthaŵiyo ndi kuti Yesu atachokako.

Kodi ukudziŵa kuti Yesu anathaŵa bwanji?— Okhulupirira nyenyezi aja atanyamuka kupita kwawo, Yehova anachenjeza Yosefe, mwamuna wake wa Mariya, kuti anyamuke athaŵire kutali ku Igupto. Kumeneko Yesu sakanaphedwa ndi Herode woipayo. Patapita zaka, Mariya ndi Yosefe anabwerako ndi Yesu ku Igupto, ndipo Mulungu anachenjezanso Yosefe. Kudzera m’maloto anamuuza kuti akakhale ku Nazarete, kumene Yesu akakhale bwinobwino.—Mateyu 2:7-23.

Kodi Yesu ali wamng’ono anapulumutsidwanso motani?

Kodi ukuona mmene Yehova anatetezera Mwana wake?— Kodi unganene kuti ndani amene akufanana ndi ana a mbalame aja anali mu udzu kapena Yesu pamene anali wamng’ono? Ndi iweyo, kodi si choncho?— Nawenso pali ena amene amafuna kukupweteka. Kodi ukuwadziŵa?—

Baibulo limanena kuti Satana ali ngati mkango wobangula amene akufuna kutidya. Ndipo mofanana ndi mikango yomwe imakonda kugwira nyama zing’onozing’ono, Satana ndi ziwanda zake nawo amakonda ana. (1 Petro 5:8) Koma Yehova ndi wamphamvu kuposa Satana. Yehova angateteze ana ake kapena angachotse choipa chilichonse chimene Satana angawachitire.

Kodi ukukumbukira zimene tinaphunzira mu Mutu 10 wa buku lino, zomwe Mdyerekezi ndi ziwanda zake amafuna kuti ife tizichita?— Inde, amafuna kuti tizichita zimene Mulungu amaletsa pankhani ya kugonana. Kodi paja ndani okha amene ayenera kugonana?— Eya, amene ayenera kugonana ndi munthu wamwamuna wamkulu ndi munthu wamkazi wamkulu okwatirana.

Komabe, ndi zomvetsa chisoni kuti anthu akuluakulu ena amakonda kugonana ndi ana. Iwo akamachita zimenezi, anyamata ndi atsikana mwina amayamba kuchita zinthu zoipa zimene aphunzira kwa anthu akuluakuluwo. Nawonso amayamba kugwiritsa ntchito molakwika ziwalo zawo zoberekera. Zoterezi zinachitika kalekalelo mu mudzi wa Sodomu. Baibulo limanena kuti anthu akumeneko, ‘anyamata ndi okalamba,’ anafuna kugonana ndi anthu aamuna amene anabwera kudzacheza kwa Loti.—Genesis 19:4, 5.

Choncho mofanana ndi Yesu amene anafunika kutetezedwa, iwenso ufunika kutetezedwa kwa anthu akuluakulu, ndiponso ngakhale ana ena, amene angafune kugonana nawe. Nthaŵi zambiri anthu ameneŵa amayerekeza kukhala anzako. Nthaŵi zina angakuuze kuti akupatsa chinachake ngati iwe utalonjeza kuti suuza munthu wina zimene akufuna muchite. Komatu anthuŵa ndi odzikonda, ali ngati Satana ndi ziwanda zake, ndipo amangofuna kudzisangalatsa. Tsono amafuna kusangalalako pogonana ndi ana. Izitu ndi zoipa kwambiri!

Nanga ukudziŵa zimene angachite pofuna kuti adzisangalatse?— Iwo angayese kukugwiragwira ziwalo zako zoberekera. Mwinanso angafike mpaka pokhudzitsa chiwalo chawo choberekera ku chiwalo chako choberekera. Koma nthaŵi zonse osalola munthu wina kuseŵeretsa mpheto yako. Osalola ngakhale mkulu wako kapena mng’ono wako kapena mlongo wako kapena ngakhale amayi ako kaya atate ako kuti achite zimenezi. Pathupi lako, ziwalo zimenezi ndi zoti uziziona kapena kuzigwira iweyo wekha basi.

Kodi uyenera kunena chiyani ndiponso kuchita chiyani ngati munthu wina akufuna kukugwira molakwika?

Kodi thupi lako ungaliteteze motani kwa anthu amene amachita zinthu zoipa ngati zimenezi?— Choyamba, osalola munthu wina aliyense kuseŵeretsa ziwalo zako zoberekera. Ngati wina akufuna kuchita zimenezi, nena mosaopa komanso mofuula kuti: “Osandigwira! Ndikakunenerani!” Ndipo ngati munthuyo anena kuti iweyo ndiwe unalakwa ndi chifukwa chake zinachitika zimenezo, usakhulupirire zimenezo. Si zoona. Iweyo ungochoka ukamunenere, mosasamala kanthu kuti iye ndi ndani! Uyenera kukanenabe ngakhale iye anene kuti zimene mukuchitazo ndi za aŵirinu basi osauzako ena. Ngakhale munthuyo akulonjeze kuti akupatsa mphatso yabwino kwambiri kapena ngakhale akuopseze, iwe mulimonsemo umuthaŵe ndi kukamunenera.

Suyenera kuchita mantha, koma ufunika kukhalabe wosamala. Makolo ako atakuchenjeza za anthu enaake kapena malo enaake amene angakhale oopsa kwa iweyo, uyenera kumvera. Ukamvera, munthu woipa sumupatsa mpata woti akupweteke.

Tiŵerenge za mmene ungadzitetezere ku kugonana kolakwika, pa Genesis 39:7-12; Miyambo 4:14-16; 14:15, 16; 1 Akorinto 6:18; ndi 2 Petro 2:14.