GAWO 3
Mfundo Zimene Anthu Amene Ali mu Ufumuwu Amatsatira—Kufunafuna Chilungamo cha Mulungu
TAYEREKEZERANI kuti tsiku lina mukubayibitsa neba wanu yemwe wakhala akuona zimene banja lanu limachita ndipo naye akukubayibitsani kenako n’kukukodolani. Pamene mukuyamba kucheza naye, akukufunsani kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani anthu inu mumachita zinthu mosiyana ndi anthu ena?” Ndiyeno mukumufunsa kuti, “Mukutanthauza chiyani?” Iye akunena kuti, “Ndikudziwa kuti ndinu a Mboni chifukwa mumasiyana ndi anthu amatchalitchi ena. Simumachita nawo zikondwerero zina, simumalowerera nawo ndale, simumamenya nawo nkhondo, simusuta fodya komanso nonse muli ndi makhalidwe abwino kwambiri. N’chifukwa chiyani anthu inu mumachita zinthu mosiyana ndi anthu ena?”
Inuyo mukudziwa kuti yankho lake n’lakuti: Tikulamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu ndipo Yesu, yemwe ndi Mfumu, akupitirizabe kutiyenga. Akutithandiza kuti tizitsatira chitsanzo chake n’cholinga choti tikhale ndi makhalidwe osiyana kwambiri ndi anthu a m’dziko loipali. M’chigawo chimenechi, tiona mmene Ufumu, womwe Mfumu yake ndi Mesiya, wakhala ukuyengera anthu a Mulungu mwauzimu komanso kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Ukuwayenganso monga gulu n’cholinga choti anthu onse alemekeze Yehova.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 11
Anawayenga Kuti Akhale Ndi Makhalidwe Abwino Potsanzira Mulungu Woyera
Zipinda za alonda komanso zipata za pakachisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya zakhala ndi zothandiza kwambiri kwa anthu a Mulungu polambira kuyambira mu 1914.
MUTU 12
Gulu Limene Likutumikira “Mulungu Wamtendere”
Baibulo limasiyanitsa chisokonezo ndi mtendere osati ndi kuchita zinthu mwadongosolo mtendere. N’chifukwa chiyani? Kodi yankho la funso limeneli limathandiza bwanji Akhristu masiku ano?