GAWO 24
Paulo Analemba Makalata Opita Kumipingo
Makalata amene Paulo analemba analimbikitsa mipingo yachikhristu
MPINGO wachikhristu umene unali utangokhazikitsidwa kumene, unali ndi udindo waukulu kwambiri wokwaniritsa cholinga cha Yehova. Koma pasanapite nthawi, Akhristu a m’nthawi ya atumwi anayamba kuzunzidwa. Kodi iwo akanapitirizabe kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika ngakhale kuti ankazunzidwa ndi adani awo komanso ankakumana ndi mavuto ena mumpingo momwemo? M’Malemba Achigiriki muli makalata 21 omwe ali ndi malangizo othandiza komanso mfundo zolimbikitsa.
Mtumwi Paulo ndi amene analemba makalata 14 mwa makalata onse 21, kuyambira pa Aroma mpaka pa Aheberi. Makalata amenewa ali ndi mayina a anthu kapena mipingo imene ankailembera. Tiyeni tione nkhani zina zimene zili m’makalata a Paulo amenewa.
Malangizo othandiza kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino. Anthu amene amachita dama, chigololo ndiponso machimo ena akuluakulu “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:19-21; 1 Akorinto 6:9-11) Anthu amene amalambira Mulungu ayenera kukhala ogwirizana ngakhale atakhala osiyana dziko limene akuchokera. (Aroma 2:11; Aefeso 4:1-6) Akhristu ayenera kudzipereka pothandiza Akhristu anzawo amene akufunikira thandizo. (2 Akorinto 9:7) Paulo anati: “Muzipemphera mosalekeza.” N’zoonadi, anthu amene amalambira Mulungu akulimbikitsidwa kuti azipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. (1 Atesalonika 5:17; 2 Atesalonika 3:1; Afilipi 4:6, 7) Kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro.—Aheberi 11:6.
Kodi n’chiyani chingathandize kuti mabanja aziyenda bwino? Amuna ayenera kukonda akazi awo ngati mmene amakondera thupi lawo. Akazinso ayenera kulemekeza kwambiri amuna awo. Ana nawonso ayenera kumvera makolo awo, chifukwa zimenezi zimasangalatsa Mulungu. Makolo ayenera kulangiza ndi kuphunzitsa ana awo mwachikondi, pogwiritsa ntchito mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu.—Aefeso 5:22–6:4; Akolose 3:18-21.
Akhristu anathandizidwa kuti amvetse cholinga cha Mulungu. Mbali zambiri za Chilamulo cha Mose zinkateteza Aisiraeli ndiponso kuwapatsa malangizo kufikira nthawi imene Khristu anabwera. (Agalatiya 3:24) Komabe, Akhristu sachita kufunikira kuti azitsatira Chilamulo polambira Mulungu. M’kalata imene analembera Aheberi kapena kuti Akhristu achiyuda, Paulo anawathandiza kumvetsa cholinga cha Chilamulo ndiponso mmene Khristu anakwaniritsira cholinga cha Mulungu. Paulo anafotokoza kuti zinthu zosiyanasiyana zimene zinkachitika potsatira Chilamulo zinali zaulosi. Mwachitsanzo, nyama zimene ankapereka nsembe zinkaimira Yesu amene anapereka moyo wake monga nsembe, imene inathandiza kuti machimo athu azikhululukidwa. (Aheberi 10:1-4) Pogwiritsa ntchito imfa ya Yesu, Mulungu anafafaniza pangano la Chilamulo chifukwa silinalinso lofunika.—Akolose 2:13-17; Aheberi 8:13.
Malangizo othandiza kuti mpingo uziyenda bwino. Amuna amene amafuna kukhala ndi udindo mumpingo ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kukwaniritsa zowayenereza za m’Malemba. (1 Timoteyo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Anthu amene amalambira Yehova Mulungu amafunika kusonkhana pamodzi ndi Akhristu anzawo nthawi zonse kuti azilimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Misonkhano yolambira Mulungu iyenera kukhala yolimbikitsa ndiponso yophunzitsa.—1 Akorinto 14:26, 31.
Pa nthawi imene Paulo analembera Timoteyo kalata yachiwiri, mtumwiyu anali atabwerera ku Roma. Pa nthawiyi iye anali m’ndende, kudikirira kuti aweruzidwe. Anthu ochepa chabe ndi amene analimba mtima kukamuona. Paulo anadziwa kuti watsala pang’ono kufa. Iye anati: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro.” (2 Timoteyo 4:7) Zikuoneka kuti patangopita nthawi yochepa atalemba kalatayi, Paulo anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Koma makalata amene mtumwiyu analemba, amathandizabe anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera mpaka pano.
—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Aroma; 1 Akorinto; 2 Akorinto; Agalatiya; Aefeso; Afilipi; Akolose; 1 Atesalonika; 2 Atesalonika; 1 Timoteyo; 2 Timoteyo; Tito; Filimoni; Aheberi.