PHUNZIRO 2
Kodi Mulungu Ndani?
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Mulungu?
Mulungu woona ndi amene analenga zinthu zonse. Iye alibe chiyambi komanso alibe mapeto. (Salimo 90:2) Uthenga wabwino umene uli m’Baibulo unachokera kwa iyeyo. (1 Timoteyo 1:11) Popeza kuti Mulungu ndi amene anatipatsa moyo, iye yekha ndi amene tiyenera kumulambira.—Werengani Chivumbulutso 4:11.
2. Kodi Mulungu ndi wotani kwenikweni?
Palibe munthu amene anaonapo Mulungu chifukwa chakuti Mulungu ndi Mzimu. Izi zikutanthauza kuti iye ndi wapamwamba kwambiri kuposa cholengedwa chilichonse cha padziko lapansi. (Yohane 1:18; 4:24) Komabe, tingathe kudziwa makhalidwe a Mulungu tikaona zinthu zimene iye analenga. Mwachitsanzo, Mulungu analenga maluwa komanso zipatso za mitundu yosiyanasiyana zimene zimasonyeza kuti iye ndi wachikondi komanso wanzeru. Ndipo zinthu zambiri zakuthambo zimene analenga zimasonyeza kuti iye ndi wamphamvu.—Werengani Aroma 1:20.
Tikamawerenga Baibulo tingaphunzire zambiri zokhudza makhalidwe a Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza zimene Mulungu amakonda komanso zimene amadana nazo, zimene amachita kwa anthu, ndiponso mmene amachitira zinthu pa nkhani zosiyanasiyana.—Werengani Salimo 103:7-10.
3. Kodi Mulungu ali ndi dzina?
Yesu ananena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ngakhale kuti Mulungu ali ndi mayina ambiri aulemu, koma dzina lake lenileni ndi limodzi lokha. Dzinali limalembedwa m’njira zosiyanasiyana, m’zinenero zosiyanasiyananso. Mwachitsanzo, m’Chichewa timati “Yehova,” koma anthu ena amangoti “Yahweh.”—Werengani Salimo 83:18.
M’Mabaibulo ambiri anachotsamo dzina la Mulungu ndipo m’malomwake anaikamo mayina audindo chabe akuti Ambuye kapena Mulungu. Koma Baibulo litangolembedwa kumene,dzina la Mulungu linkapezeka m’malo pafupifupi 7,000. Ndipotu pamene Yesu ankaphunzitsa anthu zokhudza Mulungu, anawathandiza kuti adziwenso dzina la Mulungu.—Werengani Yohane 17:26.
Onerani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?
4. Kodi Yehova amasamala za ife?
Kodi mmene mavuto achulukiramu, zikusonyeza kuti Yehova ndi Mulungu amene sasamala za ife? Anthu ena amanena kuti Mulungu amatibweretsera mavuto pofuna kutiyesa, koma zimenezi si zoona.—Werengani Yakobo 1:13.
Mulungu amatilemekeza ndipo anatipatsa ufulu wosankha zimene tikufuna. Kunena zoona, timayamikira kwambiri kuti tili ndi ufulu wosankha kulambira Mulungu. (Yoswa 24:15) Komabe anthu ambiri amasankha kuchitira ena zinthu zoipa, ndipo izi zachititsa kuti anthu ambiri azivutika. Yehova amakhumudwa akamaona kupanda chilungamo kotereku.—Werengani Genesis 6:5, 6.
Yehova ndi Mulungu amene amasamala za ife. Iye amafuna kuti tizisangalala ndi moyo. Choncho, posachedwapa athetsa mavuto onse komanso awononga anthu onse amene amayambitsa mavutowo. Koma padakali pano, Mulungu ali ndi chifukwa chomveka chololera kuti anthu avutike kwa kanthawi kochepa. Mu Phunziro 8, tidzakambirana za chifukwa chimenechi.—Werengani 2 Petulo 2:9; 3:7, 13.
5. Kodi tingatani kuti timuyandikire Mulungu?
Yehova akutipempha kuti timuyandikire polankhula naye m’pemphero. Iye amasamalira munthu aliyense payekha. (Salimo 65:2; 145:18) Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira. Ndipotu iye amaona tikamayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa, ngakhale kuti nthawi zina timalephera. Choncho, ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, n’zotheka ndithu kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.—Werengani Salimo 103:12-14; Yakobo 4:8.
Popeza kuti Yehova watipatsa moyo, tiyenera kumukonda kwambiri kuposa mmene timakondera wina aliyense. (Maliko 12:30) Mukamasonyeza kuti mumakonda Mulungu popitiriza kuphunzira za iyeyo, komanso pochita zimene akufuna, mudzamuyandikira kwambiri.—Werengani 1 Timoteyo 2:4; 1 Yohane 5:3.