Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 15

Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

1, 2. Kodi ndi nthawi iti pamene Yesu anakwiya, nanga n’chifukwa chiyani?

 YESU ankaoneka kuti wakwiya ndipo zinali zomveka kutero. Mwina zimenezi zingakuvuteni kumvetsa chifukwa Yesu anali munthu wofatsa kwambiri. (Mateyu 21:5) Iye sanali munthu wosachedwa kukwiya ndipo akakwiya zinkakhala kuti waona kuti sipanachitike zachilungamo. a Ndiye kodi pa nthawiyi n’chiyani chinakwiyitsa munthu wokonda mtendereyu? Panali zinthu zinazake zoipa kwambiri zimene zinkachitika.

2 Yesu ankakonda kwambiri kachisi wa ku Yerusalemu. Padziko lonse lapansi, malo okhawa ndi amene anali opatulika omwe anaperekedwa kuti azilambirirapo Atate ake akumwamba. Ayuda ochokera m’madera akutali ankapita kumeneko kukalambira. Nawonso anthu amitundu ina oopa Mulungu ankabwera kukachisiyu ndipo ankalowa m’bwalo limene analikonza kuti anthu oterewa azilambiriramo. Koma chakumayambiriro kwa utumiki wake, Yesu anafika pakachisi n’kupeza kuti pakuchitika zinthu zoipa kwambiri. Malowa ankangokhala ngati msika osati kachisi. Panali anthu ambiri ogulitsa malonda komanso osintha ndalama. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kunali kupanda chilungamo? Chifukwa choti anthuwa ankagwiritsa ntchito kachisi wa Mulungu kuti azichita zachinyengo ngakhalenso kubera anthu. Kodi ankachita bwanji zimenezi?​—Yohane 2:14.

3, 4. Kodi ndi zinthu zolakwika ziti zomwe zinkachitika panyumba ya Yehova, ndipo Yesu anachita chiyani kuti akonze zolakwikazo?

3 Atsogoleri achipembedzo analamula kuti mtundu umodzi wokha wa ndalama ndi umene uzigwiritsidwa ntchito pokhoma msonkho wapakachisi. Anthu omwe abwera pakachisipo ankafunika kusinthitsa ndalama zawo kuti apeze ndalama za mtundu umenewo. Choncho osinthitsa ndalama ankaika matebulo awo m’kati mwa kachisimo, ndipo kuti munthu asinthe ndalama zake ankamulipiritsa. Anthu ankagulitsanso ziweto ndipo ankapeza phindu lalikulu. Anthu omwe ankafuna kupereka nsembe akanatha kugula nyama yoti apereke nsembeyo kwa wogulitsa wina aliyense mumzindawo. Koma akuluakulu apakachisi ankatha kukana nyama zoterozo kuti n’zosayenera. Nyama zogulidwa pakachisi pomwepo ndi zimene sankazikana. Ndiye poti anthuwo sakanachitira mwina koma kugula pakachisipo, nthawi zina amalondawo ankawadulitsira kwambiri. b Komatu kumeneku sikunali kungodulitsa malonda chabe. Kunali kuba.

4 Yesu sakanalekerera zinthu zopanda chilungamozi. Imeneyi inali nyumba ya Bambo ake. Choncho anapanga chikwapu cha zingwe n’kutulutsa ng’ombe ndi nkhosa m’kachisimo. Kenako anapita pomwe panali osinthitsa ndalama n’kugubuduza matebulo awo. Ndalama zambirimbiri zinangoti mbwee pansi pomwe anapakonza ndi miyala ya mabo. Ndiyeno Yesu analamula mokalipa anthu amene ankagulitsa nkhundawo kuti: “Chotsani izi muno!” (Yohane 2:15, 16) Zikuoneka kuti panalibe aliyense amene anayerekeza kutsutsa munthu wolimba mtimayu.

“Chotsani izi muno!”

Ankachita Zinthu Ngati Atate Ake

5-7. (a) Asanabwere padzikoli, kodi Yesu anaphunzira bwanji mmene Yehova amaonera nkhani ya chilungamo, ndipo tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake? (b) Kodi Yesu anatani pa zinthu zopanda chilungamo zimene Satana ananena, nanga adzachita chiyani m’tsogolomu?

5 Patapita nthawi amalondawo anabweranso. Moti patatha zaka pafupifupi zitatu, Yesu anawathamangitsanso m’kachisi ndipo pa nthawiyi ananena mawu omwenso Yehova ananena potsutsa anthu omwe anasandutsa nyumba yake kukhala “phanga la achifwamba.” (Yeremiya 7:11; Mateyu 21:13) Yesu ataona kuti anthu akuberedwa ndiponso kachisi wa Mulungu akudetsedwa, anakhumudwa ngati mmene Atate ake anachitira ndipo n’zosadabwitsa. Yesu anaphunzitsidwa ndi Atate ake akumwamba kwa zaka mamiliyoni osawerengeka. Chifukwa cha zimenezi, iye ankakonda chilungamo ngati Yehova. Yesu ndi chitsanzo chenicheni cha mawu akuti, “Make mbuu, mwana mbuu.” Choncho ngati tikufuna kudziwa bwino mmene Yehova alili wachilungamo, njira yabwino n’kuganizira chitsanzo cha Yesu Khristu.​—Yohane 14:9, 10.

6 Mwana wobadwa yekha wa Yehovayu analipo pamene Satana mopanda chilungamo ananena kuti Yehova Mulungu ndi wabodza ndiponso salamulira mwachilungamo. Limenelitu linali bodza lalikulu kwambiri. Kenako Mwanayu anamvanso Satana akunena kuti palibe munthu angatumikire Yehova chifukwa chomukonda. Mabodza amenewa anakhumudwitsa kwambiri Mwanayu chifukwa amakonda chilungamo. Choncho ayenera kuti anasangalala kwambiri atamva kuti adzathandiza nawo m’njira yapadera posonyeza kuti Satana ndi wabodza. (2 Akorinto 1:20) Kodi akanachita bwanji zimenezi?

7 Monga taphunzirira m’Mutu 14, Yesu Khristu anapereka yankho losatsutsika pa zimene Satana ananena zokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Yehova. Pochita zimenezi, Yesu anachita zinthu zomwe zidzathandize aliyense kudziwa kuti ulamuliro wa Yehova ndi wolungama ndiponso kuti dzina la Yehovayo lidzayeretsedwe. Monga Mtumiki Wamkulu wa Mulungu, Yesu adzaonetsetsa kuti aliyense akuchita zimene Yehova amaona kuti n’zolungama. (Machitidwe 5:31) Zimene ankachita komanso kuphunzitsa ali padzikoli, zinkasonyezanso kuti amatsanzira Mulungu pa nkhani ya chilungamo. Ponena za iye, Yehova anati: “Ndidzaika mzimu wanga pa iye ndipo anthu a mitundu ina adzawasonyeza bwinobwino chilungamo chenicheni.” (Mateyu 12:18) Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji mawu amenewa?

Yesu Anathandiza Anthu Kudziwa “Chilungamo Chenicheni”

8-10. (a) Kodi malamulo amene atsogoleri achipembedzo a Chiyuda anapanga ankalimbikitsa bwanji anthu kuti azinyansidwa ndi anthu a mitundu ina ndiponso kunyoza akazi? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti malamulo amene anthu anapanga anachititsa kuti kutsatira lamulo la Yehova lokhudza Sabata kukhale kovuta?

8 Yesu ankakonda Chilamulo cha Yehova ndipo ankachita zimene chimanena. Koma atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake ankapotoza Chilamulocho. Yesu anawauza kuti: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! . . . Mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, zomwe ndi chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.” (Mateyu 23:23) Mwadala, aphunzitsi a Chilamulo cha Mulungu amenewo sankathandiza anthu kudziwa “chilungamo chenicheni,” kapena kuti zimene Mulungu amafuna pa nkhani ya chilungamo. Kodi ankachita bwanji zimenezi? Taonani zitsanzo izi.

9 Yehova anauza anthu ake kuti asamagwirizane ndi anthu a mitundu ina omwe ankalambira mafano. (1 Mafumu 11:1, 2) Komabe, atsogoleri ena achipembedzo ankakokomeza n’kumalimbikitsa anthu kuti azinyansidwa ndi aliyense yemwe sanali Myuda. Moti m’buku la Mishnah munali lamulo lakuti: “Osasiya ng’ombe kunyumba kwa munthu yemwe si Myuda chifukwa akhoza kugona nayo.” Maganizo amenewa anali olakwika komanso osagwirizana ndi mfundo za m’Chilamulo cha Mose. (Levitiko 19:34) Panalinso malamulo ena amene anthu anapanga omwe ankanyoza akazi. Mwachitsanzo, lamulo lina linkati mkazi aziyenda kumbuyo kwa mwamuna wake, osati pambali pake. Mwamuna ankachenjezedwa kuti asamacheze ndi mkazi pagulu, ngakhale mkazi wake. Mofanana ndi akapolo, akazi sankaloledwa kupereka umboni m’khoti. Panalinso pemphero limene amuna ankanena n’kumathokoza Mulungu chifukwa chakuti anabadwa amuna osati akazi.

10 Atsogoleri achipembedzo anapanga malamulo ambirimbiri omwe ankachititsa kuti zikhale zovuta kumvetsa Chilamulo cha Mulungu. Mwachitsanzo, lamulo lonena za Sabata linkangoletsa kugwira ntchito tsiku la Sabata kuti anthu pa tsikulo azichita zinthu zokhudza kulambira, azilimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova ndiponso azipuma. Koma Afarisi anachititsa kuti lamuloli likhale lovuta kulitsatira. Anangodzisankhira okha tanthauzo la mawu akuti “ntchito.” Anatchula zinthu 39 kuti ngati munthu atazichita, ndiye kuti wagwira ntchito. Zina mwa zinthuzi zinali kukolola ndiponso kusaka nyama. Koma zimenezi zinangobweretsa mafunso ambirimbiri. Munthu akapha nthata pa Sabata, kodi ndiye kuti wasaka? Ngati akudutsa m’munda wa tirigu n’kupulula tirigu wokwana m’manja mwake kuti adye, kodi akukolola? Ngati wachiritsa munthu wodwala, kodi ndiye kuti wagwira ntchito? Pofuna kuyankha mafunso ngati amenewa, atsogoleri achipembedzo anapanga malamulo okhwima kwambiri komanso ovuta kuwamvetsa.

11, 12. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankatsutsa miyambo ya Afarisi yosagwirizana ndi Malemba?

11 Popeza zinthu zinali choncho, kodi Yesu akanathandiza bwanji anthu kudziwa chilungamo chenicheni? Zimene Yesu ankaphunzitsa komanso kuchita pa moyo wake, zinasonyeza kuti ankatsutsa molimba mtima zochita za atsogoleri achipembedzowo. Mwachitsanzo, taonani zina mwa zimene anaphunzitsa. Anatsutsa mosapita m’mbali malamulo ambirimbiri amene atsogoleri achipembedzo anapanga ndipo anati: “Mumapangitsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu imene munaipereka kwa anthu.”​—Maliko 7:13.

12 Molimba mtima Yesu anaphunzitsa kuti zimene Afarisi ankanena zokhudza lamulo la Sabata zinali zolakwika ndipo iwo sanamvetse cholinga cha lamuloli. Anafotokoza kuti Mesiya ndi “Mbuye wa Sabata” choncho anali ndi ufulu wochiritsa anthu pa tsikuli. (Mateyu 12:8) Pofuna kutsindika mfundoyi, iye ankachiritsa anthu pa Sabata onse akuona. (Luka 6:7-10) Zimenezi zinkasonyeza kuti adzachiritsa anthu padziko lonse mu Ulamuliro wa Zaka 1,000. Zaka 1,000 zimenezo zidzakhaladi Sabata lalikulu, pamene anthu onse okhulupirika adzapume ku mavuto amene amakumana nawo chifukwa cha uchimo ndi imfa.

13. Kodi Yesu anapatsa otsatira ake chilamulo chiti, ndipo chimasiyana bwanji ndi Chilamulo cha Mose?

13 Yesu anasonyezanso tanthauzo la chilungamo chenicheni pamene anapatsa otsatira ake chilamulo chatsopano chomwe ndi “chilamulo cha Khristu.” Chilamulochi chinayamba kugwira ntchito iye atamaliza utumiki wake wapadziko lapansi. (Agalatiya 6:2) Chilamulo chatsopanochi ndi chosiyana ndi Chilamulo cha Mose, chifukwa chili ndi mfundo za choonadi osati malamulo ambirimbiri olembedwa. Komabe chili ndi malamulo ena achindunji. Limodzi la malamulo amenewa Yesu analitchula kuti “lamulo latsopano.” Iye anaphunzitsa otsatira ake onse kuti azikondana ngati mmene iyeyo anawakondera. (Yohane 13:34, 35) Zoonadi, chikondi chololera kuvutikira ena chinadzakhala chizindikiro cha anthu onse amene amatsatira “chilamulo cha Khristu.”

Chitsanzo pa Nkhani ya Chilungamo

14, 15. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amadziwa malire a udindo wake, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zolimbikitsa?

14 Sikuti Yesu anangophunzitsa zokhudza chikondi, koma nthawi zonse ankachitanso zinthu zogwirizana ndi “chilamulo cha Khristu.” Tiyeni tione zinthu zitatu zimene Yesu anachita zomwe zinasonyeza tanthauzo la chilungamo chenicheni.

15 Choyamba, Yesu ankasamala kwambiri kuti asachite chilichonse chosemphana ndi chilungamo. Mwina munaona kuti zinthu zambiri zopanda chilungamo zimachitika munthu akadzikuza n’kuchita zinthu zomwe si udindo wake kuzichita. Koma Yesu sankachita zimenezo. Tsiku lina munthu wina anafika kwa Yesu n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, mumuuze mchimwene wanga kuti andigawireko cholowa.” Kodi Yesu anayankha bwanji? Anamuuza kuti: “Munthu iwe, ndi ndani amene anandisankha kuti ndikhale woweruza wanu kapena wogawa chuma chanu?” (Luka 12:13, 14) Kodi zimenezi si zochititsa chidwi? Ngakhale kuti Yesu ndi wanzeru kwambiri, wozindikira komanso Mulungu anamupatsa udindo waukulu kuposa aliyense padzikoli, anakana kulowerera nkhaniyi chifukwa sanapatsidwe udindo wochita zimenezo. Nthawi zonse Yesu amachita zinthu mosapitirira malire ndipo ndi zimene ankachitanso kwa zaka zambirimbiri asanabwere padzikoli. (Yuda 9) Zimenezi zikusonyeza kuti amadzichepetsa n’kumadalira Yehova kuti Yehovayo anene zimene zili zoyenera.

16, 17. (a) Pa nkhani yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, kodi Yesu anasonyeza bwanji chilungamo? (b) Kodi Yesu anasonyeza chilungamo m’njira inanso iti?

16 Chachiwiri, Yesu anasonyeza chilungamo pa zimene ankachita pa nkhani yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iye sankachita zinthu mokondera. M’malomwake ankayesetsa kulalikira kwa anthu onse, kaya olemera kapena osauka. Koma Afarisi ankanyoza anthu wamba powatchula kuti ʽam-ha·ʼaʹrets, kapena kuti “eni dziko.” Molimba mtima Yesu anasonyeza kuti kumeneku kunali kupanda chilungamo. Iye ankaphunzitsa anthu uthenga wabwino, kudya nawo, kuwapatsa zakudya, kuwachiritsa ndiponso kuwaukitsa. Apatu ankatsanzira Mulungu wachilungamo amene amafuna kuti “anthu osiyanasiyana” apulumuke.  c​—1 Timoteyo 2:4.

17 Chachitatu, Yesu anasonyeza chilungamo pokhala wachifundo. Ankathandiza anthu ochimwa. (Mateyu 9:11-13) Komanso ankathandiza mofunitsitsa anthu omwe analibe owateteza. Mwachitsanzo, Yesu sankagwirizana ndi zimene atsogoleri achipembedzo ankauza anthu zoti asamakhulupirire anthu onse amene sanali Ayuda. Mwachifundo anathandiza komanso kuphunzitsa ena mwa anthuwa, ngakhale kuti anatumidwa kwa Ayuda okha. Anavomera kuchiritsa modabwitsa wantchito wa mtsogoleri wa asilikali a Roma ndipo anati: “Mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.”​—Mateyu 8:5-13.

18, 19. (a) Kodi Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza akazi m’njira ziti? (b) Kodi chitsanzo cha Yesu chikutithandiza bwanji kuona kugwirizana pakati pa kulimba mtima ndi kuchita chilungamo?

18 Komanso Yesu sankagwirizana ndi maganizo omwe anali ofala pa nthawiyo onyoza akazi. M’malomwake, iye molimba mtima ankachita zoyenera pa nkhaniyi. Ayuda ankakhulupirira kuti akazi a Chisamariya ndi odetsedwa ngati mmene ankaoneranso anthu onse omwe sanali Ayuda. Koma Yesu analalikira mayi wa Chisamariya pachitsime cha ku Sukari. Ndipotu kwa nthawi yoyamba, Yesu anauza mayi ameneyu kuti ndi Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 4:6, 25, 26) Afarisi ankanena kuti akazi sayenera kuphunzitsidwa Chilamulo cha Mulungu, koma Yesu ankagwiritsa ntchito mphamvu komanso nthawi yake yambiri kuphunzitsa akazi. (Luka 10:38-42) Pa chikhalidwe chawo, Ayuda ankakhulupirira kuti akazi sangapereke umboni wodalirika. Koma Yesu analemekeza akazi angapo powapatsa mwayi wapadera woti akhale oyamba kumuona ataukitsidwa. Moti mpaka anawauza kuti apite kukauza ophunzira ake aamuna za nkhani yofunika kwambiri imeneyi.​—Mateyu 28:1-10.

19 Zoonadi, Yesu anathandiza anthu kudziwa zimene chilungamo chenicheni chimatanthauza. Ndipo nthawi zambiri ankaika moyo wake pangozi kuti achite zimenezi. Chitsanzo cha Yesu chikusonyeza kuti pamafunika kulimba mtima kuti munthu achite chilungamo. M’pake kuti amatchedwa “Mkango wa fuko la Yuda.” (Chivumbulutso 5:5) Kumbukirani kuti mkango ndi chizindikiro cha kulimba mtima posonyeza chilungamo. Posachedwapa Yesu achita zambiri kuposa zomwe anachita ali padziko lapansi. Iye adzaonetsetsa kuti chilichonse padzikoli chikuchitika mwachilungamo.​—Yesaya 42:4.

Mesiya Yemwenso Ndi Mfumu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

20, 21. Masiku ano kodi Yesu, yemwe ndi Mfumu komanso Mesiya, akulimbikitsa bwanji chilungamo padziko lonse komanso mumpingo wa Chikhristu?

20 Kungoyambira pamene anakhala Mfumu mu 1914, Yesu akulimbikitsa chilungamo padzikoli. Kodi akuchita bwanji zimenezi? Akuonetsetsa kuti ulosi wake wopezeka pa Mateyu 24:14 ukukwaniritsidwa. Otsatira ake akuphunzitsa anthu m’mayiko onse choonadi cha Ufumu wa Yehova. Mofanana ndi Yesu, iwo amalalikira mosakondera ndiponso mwachilungamo. Amayesetsa kuti munthu aliyense kaya wamng’ono kapena wamkulu, wolemera kapena wosauka komanso mwamuna kapena mkazi apeze mwayi wodziwa Yehova, Mulungu wachilungamo.

21 Yesu akulimbikitsanso chilungamo mumpingo wa Chikhristu, womwe iye ndi Mutu wake. Mogwirizana ndi ulosi, Yesu amapereka “amuna kuti akhale mphatso.” Amuna amenewa ndi akulu a Chikhristu okhulupirika amene amatsogolera mumpingo. (Aefeso 4:8-12) Akamaweta nkhosa zamtengo wapatali za Mulungu, akulu amatsanzira Yesu Khristu pa nkhani yolimbikitsa chilungamo. Nthawi zonse amakumbukira zoti Yesu amafuna kuti nkhosa zake zizichitiridwa zinthu mwachilungamo, posatengera udindo, kutchuka ngakhalenso chuma cha munthu.

22. Kodi Yehova amamva bwanji akaona zinthu zopanda chilungamo zomwe zafala m’dzikoli, nanga anasankha Mwana wake kuti adzachite chiyani?

22 Posachedwapa Yesu akhazikitsa chilungamo padziko lonse m’njira yoti sinachitikepo. M’dziko lachinyengoli, zinthu zopanda chilungamo zili paliponse. Si chilungamo kuti ana amamwalira chifukwa chosowa chakudya, chonsecho mayiko amawononga ndalama zambirimbiri popanga zida zankhondo. Komanso anthu amawononga ndalama zambiri pa zinthu zongosangalatsa iwowo. Chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambirimbiri amafa chifukwa cha mavuto oti akanatha kupewedwa. Zinthu zopanda chilungamo zimenezi komanso zina zambiri zimakwiyitsa kwambiri Yehova. Choncho iye anasankha Mwana wake kuti adzamenye nkhondo yolungama kuti awononge dziko loipali komanso kuthetseratu zinthu zopanda chilungamo.​—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-15.

23. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, kodi Khristu adzalimbikitsa bwanji chilungamo mpaka kalekale?

23 Komabe sikuti chilungamo cha Yehova chidzachititsa kuti angowononga anthu oipa. Iye anasankhanso Mwana wake kuti alamulire monga “Kalonga Wamtendere.” Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, ulamuliro wa Yesu udzabweretsa mtendere padziko lonse, ndipo iye azidzalamulira ‘mwachilungamo.’ (Yesaya 9:6, 7) Kenako, Yesu adzagwira mosangalala ntchito yothetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene zikuchititsa kuti anthu ambiri azivutika. Ndiyeno mokhulupirika komanso mpaka kalekale adzaonetsetsa kuti zinthu zonse zikuchitika mogwirizana ndi chilungamo cha Yehova. Choncho n’zofunika kwambiri kuti panopa tiziyesetsa kutsanzira Yehova pa nkhani yochita chilungamo. M’mutu wotsatira tiona kuti tingachite bwanji zimenezi.

a Posonyeza mkwiyo chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo, Yesu ankatsanzira Yehova, amene ndi “wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake” pa zoipa zilizonse. (Nahumu 1:2) Mwachitsanzo, Yehova atauza anthu ake osamvera kuti anasandutsa nyumba yake kukhala “phanga la achifwamba,” anati: “Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zidzatsanulidwa pamalo awa.”​—Yeremiya 7:11, 20.

b Mogwirizana ndi zomwe buku lotchedwa Mishnah linanena, patapita zaka zingapo kunachitika chionetsero chotsutsa kudula kwa nkhunda zogulitsidwa pakachisi. Nthawi yomweyo mtengowo unatsitsidwa kwambiri. Kodi ndi ndani amene ankapindula kwambiri ndi malonda apakachisi amenewa? Akatswiri ena a mbiri yakale amati misika yapakachisi inali ya banja la Mkulu wa Ansembe Anasi, ndipo n’kumene kunkachokera chuma chochuluka cha banjali.​—Yohane 18:13.

c Afarisi ankanena kuti anthu wamba osadziwa Chilamulo anali ‘otembereredwa.’ (Yohane 7:49) Ankati munthu sayenera kuphunzitsa anthu amenewo, kuchita nawo malonda, kudya nawo ngakhalenso kupemphera nawo. Ankanenanso kuti kulola mwana wako kuti akwatiwe ndi mwamuna woteroyo chinali chinthu choipa kuposa kumulekerera kuti agwidwe ndi nyama yakutchire. Ankakhulupiriranso kuti anthu wambawa sali m’gulu la anthu odzaukitsidwa.