Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 1

‘Mphamvu Zoopsa’

‘Mphamvu Zoopsa’

M’chigawochi, tikambirana nkhani za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zoti angathe kulenga, kuwononga, kuteteza ndiponso kubwezeretsa zinthu. Yehova Mulungu ali ndi ‘mphamvu zoopsa’ komanso ‘zochuluka.’ Kumvetsa mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zakezi kungatithandize kukhala ndi chiyembekezo ndiponso kukhala olimba mtima.​—Yesaya 40:26.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 4

‘Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri’

Kodi tiziopa Mulungu chifukwa choti ali ndi mphamvu? Tingayankhe kuti inde komanso ayi.

MUTU 5

Mphamvu za Kulenga​—“Amene Anapanga Kumwamba Komanso Dziko Lapansi”

Zinthu zimene Mulungu analenga, kuyambira dzuwa lamphamvu mpaka kambalame kakang’ono kotchedwa hummingbird, zingatiphunzitse mfundo zofunika zokhudza iye.

MUTU 6

Mphamvu Zowononga​—‘Yehova Ndi Msilikali Wamphamvu’

N’chifukwa chiyani “Mulungu wamtendere” amamenya nkhondo?

MUTU 7

Mphamvu Zoteteza​—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”

Mulungu amateteza atumiki ake m’njira ziwiri, koma njira inayo ndi yofunika kwambiri.

MUTU 8

Mphamvu Zobwezeretsa​—Yehova ‘Akupanga Zinthu Zonse Kuti Zikhale Zatsopano’

Yehova, wabwezeretsa kale kulambira koona. Kodi ndi zinthu ziti zomwe adzabwezeretse m’tsogolo?

MUTU 9

“Khristu Ndi Mphamvu ya Mulungu”

Kodi zodabwitsa za Yesu Khristu komanso zimene ankaphunzitsa zimasonyeza kuti Yehova ndi wotani?

MUTU 10

“Muzitsanzira Mulungu” Mukamagwiritsa Ntchito Mphamvu

N’kutheka kuti muli ndi mphamvu zambiri kuposa mmene mukuganizira. Kodi mungazigwiritse ntchito bwanji moyenera?