Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

“Woyera, Woyera, Woyera Ndi Yehova”

“Woyera, Woyera, Woyera Ndi Yehova”

1, 2. Kodi mneneri Yesaya anaona masomphenya otani, nanga masomphenyawa amatiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?

 YESAYA ataona masomphenya ochokera kwa Mulungu anachita mantha ndiponso anadabwa kwambiri. Zinkaoneka ngati zenizenidi moti kenako iye analemba kuti ‘anaona Yehova’ atakhala pampando wachifumu wolemekezeka. Chovala chimene Yehova anavala chinadzaza m’kachisi wamkulu wa ku Yerusalemu.​—Yesaya 6:1, 2.

2 Yesaya anachitanso chidwi kwambiri atamva kuimba kwamphamvu komwe kunagwedeza kachisi ndi maziko ake. Amene ankaimba anali aserafi, omwe ndi angelo audindo waukulu kwambiri. Ankaimba mwamphamvu ndiponso momveka bwino mawu omwe anali ndi tanthauzo lapadera akuti: “Woyera, woyera, woyera ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.” (Yesaya 6:3, 4) Mawu akuti “woyera” anatchulidwa katatu pofuna kuwatsindika mwapadera ndipo m’pake kuchita zimenezi chifukwa Yehova ndi woyera kuposa wina aliyense. (Chivumbulutso 4:8) Baibulo limanena mobwerezabwereza kuti Yehova ndi woyera. Ndipotu pali mavesi ambiri m’Baibulo amene amatchula dzina lake limodzi ndi mawu akuti “loyera.”

3. Kodi kukhala ndi maganizo olakwika pa mfundo yoti Yehova ndi woyera kwalepheretsa bwanji anthu ambiri kukhala naye pa ubwenzi?

3 Apa n’zodziwikiratu kuti mfundo ina yofunika kwambiri yokhudza iyeyo imene Yehova amafuna kuti tiidziwe ndi yakuti, iye ndi woyera. Koma masiku ano anthu ambiri ali ndi maganizo olakwika pa nkhani ya kukhala woyera. Ena amaganiza kuti munthu woyera ndi amene amadziona kuti ndi wolungama kapena amanamizira kuti amatumikira Mulungu. Anthu amene amadziona kuti ndi osafunika amaona kuti si oyenera kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu yemwe ndi woyera. Choncho safuna kuyandikira Mulungu chifukwa choti iye ndi woyera. Izi n’zomvetsa chisoni chifukwa mfundo yoti Mulungu ndi woyera iyenera kutithandiza kuti tizifuna kumuyandikira. N’chifukwa chiyani tikutero? Tisanayankhe funso limeneli, tiyeni tione kaye kuti kukhala woyera kumatanthauza chiyani.

Kodi Kukhala Woyera Kumatanthauza Chiyani?

4, 5. (a) Kodi kukhala “woyera” kumatanthauza chiyani, nanga sikutanthauza chiyani? (b) Kodi Yehova ndi “wopatulika” m’njira ziwiri ziti?

4 Mfundo yoti Mulungu ndi woyera sikutanthauza kuti ndi wodzimva, wodzikuza kapenanso wonyada. Ndipotu iye amadana ndi makhalidwe amenewa. (Miyambo 16:5; Yakobo 4:6) Ndiye kodi kukhala “woyera” kumatanthauza chiyani? M’Chiheberi chimene anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, mawuwa amatanthauza “kupatula.” Pa nkhani ya kulambira, mawuwa angatanthauze chinthu kapena munthu amene wapatulidwa kapena kuikidwa padera kuti atumikire Mulungu. Mawu akuti kuyera amatanthauzanso chinthu chaukhondo. Kodi mawu amenewa amagwira ntchito bwanji akamanena za Yehova? Kodi amatanthauza kuti iye ‘amadzipatula’ kwa anthu chifukwa choti ndi woyera kwambiri ndipo sangakhale pafupi ndi anthu ochimwa?

5 Ayi. Yehova, “Woyera wa Isiraeli,” anatsimikizira anthu ake kuti anali pakati pawo ngakhale kuti anthuwo anali ochimwa. (Yesaya 12:6; Hoseya 11:9) Choncho kukhala woyera sikumuchititsa kuti atalikirane ndi anthu. Ndiye kodi Yehova ndi ‘wopatulika’ m’njira ziti? Pali njira ziwiri zofunika kwambiri. Choyamba, iye ndi wosiyana ndi zonse zimene zili m’chilengedwechi chifukwa ndi Wam’mwambamwamba. Iye ndi woyera kwambiri ndipo kuyera kwake kulibe malire. (Salimo 40:5; 83:18) Chachiwiri, Yehova alibe tchimo ngakhale pang’ono, ndipo zimenezi n’zolimbikitsa. N’chifukwa chiyani tikutero?

6. N’chifukwa chiyani mfundo yakuti Yehova alibe uchimo ngakhale pang’ono ndi yolimbikitsa kwambiri?

6 Tikukhala m’dziko limene ndi zovuta kukhala woyera. Chilichonse m’dziko la anthu osadziwa Mulunguli ndi chodetsedwa mwanjira inayake chifukwa cha uchimo komanso kupanda ungwiro. Tonsefe timafunika kulimbana ndi uchimo umene tili nawo. Ndipo ngati sitingasamale, uchimo ukhoza kutigonjetsa. (Aroma 7:15-25; 1 Akorinto 10:12) Koma Yehova zimenezi sizingamuchitikire. Popeza iye alibiretu uchimo, sangachite choipa chilichonse ngakhale pang’ono. Izi zikutsimikiziranso mfundo yakuti Yehova ndi Bambo wabwino kwambiri, ndipo tingamudalire pa chilichonse. Mosiyana ndi abambo ambiri omwe ndi ochimwa ndipo akhoza kutikhumudwitsa, Yehova sangachite zimenezo. Iye sangachite zachinyengo, khalidwe loipa kapenanso nkhanza. Chifukwa choti ndi woyera, n’zosatheka kuti achite makhalidwewa. Nthawi zina Yehova ankalumbira mogwirizana ndi kuyera kwake chifukwa kuyera kwakeko n’kodalirika kwambiri. (Amosi 4:2) Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri.

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi woyera pa chilichonse?

7 Yehova ndi woyera pa chilichonse. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Taganizirani izi, sitingaganize za “anthu” popanda kuganiziranso za “uchimo.” Uchimo unatilowerera ndipo umakhudza chilichonse chimene timachita. Koma sitingaganizire za “Yehova” popanda kuganiziranso za kukhala “woyera.” Yehova ndi woyera nthawi zonse. Chilichonse chokhudza iye ndi chaukhondo, choyera komanso cholungama. Sitingamudziwe bwino Yehova ngati sitingamvetse bwino zimene mawu akuti “kuyera” amatanthauza.

“Yehova Ndi Woyera”

8, 9. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amathandiza anthu omwe si angwiro kukhala oyera ngakhale kuti sangafike pofanana naye?

8 Popeza Yehova ndi woyera, sikulakwa kunena kuti kuyera konse kumachokera kwa iye. Sikuti khalidweli amangokhala nalo yekha, koma amathandizanso ena mowolowa manja kuti nawonso akhale nalo. Mwachitsanzo, pamene Mulungu ankalankhula ndi Mose pogwiritsa ntchito mngelo pachitsamba choyaka moto, malo ozungulira chitsambacho anakhala oyera chifukwa tingati Yehova anali pamenepo.​—Ekisodo 3:5.

9 Kodi n’zotheka kuti anthu ochimwa akhaledi oyera atathandizidwa ndi Yehova? Inde n’zotheka ngakhale kuti sangafike pofanana naye. Iye anauza Aisiraeli, omwe anali anthu ake, kuti adzakhala ‘mtundu woyera.’ (Ekisodo 19:6) Anadalitsa mtunduwo poufotokozera njira yabwino yomulambirira yomwe inali yosadetsedwa. N’chifukwa chake nkhani yokhala woyera inkatchulidwa mobwerezabwereza m’Chilamulo cha Mose. Ndipotu mkulu wa ansembe ankavala kachitsulo kagolide patsogolo pa nduwira yake, komwe kankanyezimira ndipo anthu onse ankatha kukaona. Pakachitsulopo analembapo mochita kugoba mawu akuti: “Yehova ndi Woyera.” (Ekisodo 28:36) Choncho Yehova ankafuna kuti iwowo komanso kulambira kwawo kuzikhala koyera. Yehova anawauza kuti: “Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.” (Levitiko 19:2) Aisiraeli akamayesetsa kutsatira malangizo a Mulungu, iye ankawaona kuti ndi oyera ngakhale kuti sanali angwiro.

10. Pa nkhani ya kukhala oyera, kodi panali kusiyana kotani pakati pa Aisiraeli ndi anthu a mitundu ina?

10 Makhalidwe a Aisiraeli ndiponso kulambira kwawo koyera kunkawasiyanitsa kwambiri ndi anthu a mitundu yowazungulira. Anthu amenewa ankalambira milungu yoti kulibe, imene ankaisonyeza kuti inali yachiwawa, yadyera ndiponso yachiwerewere. Milunguyi sinali yoyera ngakhale pang’ono. Kuilambira kunkachititsa kuti anthu asakhale oyera. N’chifukwa chake Yehova anachenjeza atumiki ake kuti asamagwirizane ndi anthu olambira mafano komanso asamachite nawo miyambo yachipembedzo yonyansayo.​—Levitiko 18:24-28; 1 Mafumu 11:1, 2.

11. N’chiyani chikusonyeza kuti mbali yakumwamba ya gulu la Yehova ndi yoyera?

11 Ngakhale pamene Aisiraeli ankachita bwino pa nkhani yokhala oyera, ankangosonyeza pang’ono kwambiri mfundo yakuti mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu ndi yoyera. Angelo mamiliyoni omwe amamutumikira mokhulupirika amatchulidwa kuti “oyera ake masauzande masauzande.” (Yuda 14; Deuteronomo 33:2, mawu a m’munsi) Angelowa amaonetsa bwino kuyera kosangalatsa kwa Mulungu. Komanso kumbukirani aserafi amene Yesaya anawaona m’masomphenya. Nyimbo yawo ikusonyeza kuti angelo amphamvu amenewa amagwira ntchito yofunika kwambiri podziwitsa chilengedwe chonse kuti Yehova ndi woyera. Komabe pali mngelo wina amene amaposa onsewa. Ameneyu ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Yesu ndi amene amaonetsa kwambiri mmene Yehova alili woyera. M’pake amatchulidwa kuti ndi “Woyera amene Mulungu anamutumiza.”​—Yohane 6:68, 69.

Dzina Loyera, Mzimu Woyera

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani n’zomveka kunena kuti dzina la Mulungu ndi loyera? (b) N’chifukwa chiyani dzina la Mulungu liyenera kuyeretsedwa?

12 Nanga bwanji za dzina la Mulungu? Monga tinaonera m’Mutu 1, dzinali si laudindo kapenanso longomudziwikitsa. Limaimira Yehova Mulungu, limodzi ndi makhalidwe ake onse. N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti “dzina lake ndi loyera.” (Yesaya 57:15) Chilamulo cha Mose chinkanena kuti aliyense wonyoza dzina la Mulungu aziphedwa. (Levitiko 24:16) Pajanso Yesu anatchula chinthu chofunika kwambiri chimene tiyenera kutchula koyamba tikamapemphera. Iye anati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Kuyeretsa chinachake kumatanthauza kuchiika padera monga chopatulika, kuchilemekeza komanso kuchiona kuti n’chosadetsedwa. Koma n’chifukwa chiyani dzina la Mulungu lomwe ndi loyera kale liyenera kuyeretsedwa?

13 Adani a Mulungu akhala akunena mabodza oipa kwambiri kuti adetse dzina loyera la Mulungu. M’munda wa Edeni, Satana ananena zabodza zokhudza Yehova ndipo zimene ananenazo zinasonyeza ngati kuti Yehova salamulira mwachilungamo. (Genesis 3:1-5) Kuyambira nthawi imeneyo, Satana, yemwe ndi wolamulira wa dziko lodetsedwali, akuonetsetsa kuti mabodza onena za Mulungu afalikire. (Yohane 8:44; 12:31; Chivumbulutso 12:9) Zipembedzo zachititsa anthu kuti aziona kuti Mulungu ndi wopanda chilungamo, alibe nafe ntchito ndiponso ndi wankhanza. Komanso zimanena kuti Mulungu amazithandiza pa nkhondo zawo zomwe zimaphetsa anthu ambiri. Ndiponso anthu ambiri m’malo motamanda Mulungu chifukwa cha zinthu zochititsa chidwi zimene analenga, amanena kuti zamoyo zinangokhalako zokha. N’zoonadi kuti anthu akhala akunenera dzina la Mulungu mabodza oipa kwambiri. N’chifukwa chake dzinali liyenera kuyeretsedwa komanso kupatsidwa ulemerero umene limafunikira. Tikufunitsitsa kudzaona Yehova atayeretsa dzina lake ndipo silidzadetsedwanso mpaka kalekale. Iye adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mwana wake. Timasangalala kuchita chilichonse chimene tingathe pothandizira cholinga cha Yehova chimenechi.

14. N’chifukwa chiyani mzimu wa Mulungu umatchedwa woyera, nanga n’chifukwa chiyani kunyoza mzimu woyera ndi nkhani yaikulu?

14 Palinso chinthu china chomwe nthawi zonse chimatchulidwa kuti n’choyera ndipo chimachokera kwa Yehova. Chimenechi ndi mzimu woyera, kapena kuti mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. (Genesis 1:2) Mzimu woyera ndi wamphamvu kuposa chilichonse ndipo Yehova amaugwiritsa ntchito pokwaniritsa zolinga zake. Chilichonse chimene Mulungu amachita chimakhala choyera, choncho mphamvu imene amaigwiritsa ntchito imatchedwa kuti mzimu woyera. (Luka 11:13; Aroma 1:4) Kunyoza mzimu woyera, komwe kumaphatikizapo kuchita mwadala zinthu zosemphana ndi zolinga za Yehova, ndi tchimo losakhululukidwa.​—Maliko 3:29.

Timafuna Kukhala pa Ubwenzi Ndi Yehova Chifukwa Ndi Woyera

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani podziwa kuti Yehova ndi woyera?

15 N’zosavuta kumvetsa chifukwa chake Baibulo limanena kuti anthu ayenera kuopa Mulungu chifukwa choti iye ndi woyera. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 99:3 limati: “Iwo atamande dzina lanu lalikulu, chifukwa ndi lochititsa mantha komanso loyera.” Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kulemekeza kwambiri Mulungu komanso dzina lake. Izi n’zomveka chifukwa Mulungu ndi woyera kwambiri kuposa ifeyo. Ndipo kuyera kwake ndi kwapamwamba komanso kwaulemerero. Komabe sitikuyenera kulephera kumuyandikira chifukwa choti ndi waulemerero. Kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani yoti Mulungu ndi woyera kungachititse kuti tizifuna kuti akhale mnzathu. N’chifukwa chiyani tikutero?

16. (a) Kodi kukhala oyera kumagwirizana bwanji ndi kukongola? Perekani chitsanzo. (b) Kodi Baibulo limafotokoza bwanji mfundo yoti Mulungu wathu woyera ndi wokongola?

16 Chifukwa china n’chakuti Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kuyera ndi kukongola. Lemba la Yesaya 63:15, limafotokoza kuti kumwamba ndi ‘malo a Mulungu okhala apamwamba, oyera ndi aulemerero [kapena kuti okongola, mawu a m’munsi].’ Timakopeka ndi kukongola. Mwachitsanzo, taonani chithunzi chomwe chili patsamba 33. Kodi simukusangalala ndi malo amenewo? N’chifukwa chiyani mukuona kuti malowa ndi osangalatsa? Madziwo akuoneka kuti ndi oyera bwino. Ngakhale mpweya wa pamalopa uyenera kuti ndi wabwino, chifukwa kulibe mitambo ndipo kukuwala bwino. Koma ngati malowa atasintha sangasangalatsenso. Mwachitsanzo, ngati mumtsinjewo mutadzaza zinyalala, mitengo ndi miyalayo italembedwalembedwa mawu oipa komanso mpweya utakhala kuti si wabwinonso, malowa sangaoneke bwino. Mwachibadwa, timaona kuti chinthu ndi chokongola chikakhala chaukhondo komanso chowala. Tingagwiritsenso ntchito mawu omwewa ponena za kuyera kwa Yehova. N’zosadabwitsa kuti timasangalala tikamawerenga masomphenya ofotokoza kukongola kwa Yehova. Mwachitsanzo, Baibulo limafotokoza zokhudza Mulungu wathu woyera atakhala pampando wake wachifumu kumwamba ndipo limati amawala, amanyezimira ngati miyala yamtengo wapatali ndiponso amayaka ngati moto.​—Ezekieli 1:25-28; Chivumbulutso 4:2, 3.

Timatengeka mtima ndi kukongola, tiyeneranso kutengeka ndi chiyero

17, 18. (a) Kodi poyamba Yesaya anakhudzidwa bwanji ndi masomphenya omwe anaona? (b) Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji mserafi polimbikitsa Yesaya, nanga zimene mserafiyo anachita zinkatanthauza chiyani?

17 Popeza Mulungu ndi woyera, kodi tiyenera kumadziona kuti ndife otsika poyerekeza ndi iyeyo? Yankho ndi lakuti inde. Ndipotu ndifedi otsika poyerekeza ndi Yehova komanso kumeneku n’kuyerekezera zinthu ziwiri zomwe n’zosiyana kwambiri. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti sangakhale mnzathu? Taganizirani zimene Yesaya anachita atamva aserafi akulengeza kuti Yehova ndi woyera. Timawerenga kuti: “Kenako ndinanena kuti: ‘Tsoka kwa ine! Maso anga aona Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Ndifa ine basi, chifukwa ndine munthu wa milomo yodetsedwa, ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.’” (Yesaya 6:5) Kudziwa kuti Yehova ndi woyera kwambiri, kunakumbutsa Yesaya kuti anali wochimwa komanso sanali wangwiro. Poyamba zimenezi zinamuchititsa kuti adzimvere chisoni. Koma Yehova sanafune kuti munthu wokhulupirikayu azidzimvera chisoni choncho.

18 Nthawi yomweyo Yehova anatumiza mserafi wina kuti akalimbikitse mneneriyu. Kodi anamulimbikitsa bwanji? Mngelo wamphamvuyo unaulukira kuguwa la nsembe n’kutenga khala la moto, n’kulikhudzitsa pamilomo ya Yesaya. Zimenezi zingaoneke kukhala zopweteka kwambiri m’malo mokhala zolimbikitsa. Komabe kumbukirani kuti awa anali masomphenya amene ankaimira zambiri. Yesaya, yemwe anali Myuda wokhulupirika, ankadziwa bwino kuti nsembe zinkaperekedwa tsiku lililonse paguwa la nsembe lapakachisi pofuna kuphimba machimo. Ndipo mserafiyo anakumbutsa mneneriyu mwachikondi kuti ngakhale kuti anali wa “milomo yodetsedwa” kapena kuti sanali wangwiro, Mulungu akanathabe kumuona kuti ndi woyera. a Yehova ankafunitsitsa kumuona kuti ndi woyera munthu amene sanali wangwiro komanso wochimwayu, ngakhale kuti iye sakanakhala woyera kufika pofanana ndi Mulungu.​—Yesaya 6:6, 7.

19. Kodi zingatheke bwanji kuti anthu ochimwafe tikhale oyera, ngakhale kuti sitingafike pofanana ndi Mulungu?

19 N’chimodzimodzinso masiku ano. Nsembe zonse zimene ankapereka paguwa la nsembe ku Yerusalemu zinkangoimira nsembe ina yaikulu. Imeneyi ndi nsembe yangwiro yomwe Yesu Khristu anapereka mu 33 C.E. (Aheberi 9:11-14) Tikalapa machimo athu moona mtima, kusiya zoipazo komanso kukhulupirira nsembe imeneyi, Mulungu amatikhululukira. (1 Yohane 2:2) Ifenso Mulungu akhoza kumationa kuti ndife oyera. N’chifukwa chake mtumwi Petulo anatikumbutsa kuti: “Malemba amati: ‘Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.’” (1 Petulo 1:16) Onani kuti Yehova sananene kuti tikhale oyera ngati iyeyo. Sayembekezera kuti tichite zimene sitingathe. (Salimo 103:13, 14) M’malomwake, Yehova amatiuza kuti tizikhala oyera chifukwa iye ndi woyera. “Monga ana ake okondedwa,” timayesetsa kumutsanzira mmene tingathere monga anthu oti siife angwiro. (Aefeso 5:1) Choncho nthawi zonse timafunika kuyesetsa kuti tizikhala oyera. Tikamakula mwauzimu, tsiku lililonse timayesetsabe kuti “tikhale oyera.”​—2 Akorinto 7:1.

20. (a) Kodi kumvetsa mfundo yoti Mulungu akhoza kumationa kuti ndife oyera kungatithandize bwanji? (b) Kodi Yesaya anatani atadziwa kuti machimo ake akhululukidwa?

20 Yehova amakonda zinthu zolungama komanso zosadetsedwa. Iye amadana ndi tchimo. (Habakuku 1:13) Koma sikuti amadana nafe. Tikamaona tchimo mmene iye amalionera, kutanthauza kudana ndi zoipa n’kumakonda zabwino, komanso tikamayesetsa kutsatira mapazi a Khristu Yesu, Yehova amatikhululukira machimo athu. (Amosi 5:15; 1 Petulo 2:21) Tikamvetsa mfundo yoti Yehova akhoza kumationa kuti ndife oyera, zotsatira zake zimakhala zabwino. Kumbukirani kuti mfundo yoti Yehova ndi woyera poyamba inakumbutsa Yesaya kuti iyeyo ndi wodetsedwa. Anati: “Tsoka kwa ine!” Koma anasintha maganizo atadziwa kuti machimo ake akhululukidwa. Moti Yehova atapempha amene angadzipereke kugwira ntchito inayake, nthawi yomweyo Yesaya anadzipereka, ngakhale kuti sankadziwa kuti ntchito yake ndi yotani. Iye anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”​—Yesaya 6:5-8.

21. N’chiyani chikutitsimikizira kuti tikhoza kukwanitsa kukhala oyera?

21 Tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu woyera choncho tingathe kutsanzira makhalidwe ake abwino komanso kukhala naye pa ubwenzi. (Genesis 1:26) Aliyense akhoza kukwanitsa kukhala woyera. Tikamayesetsa kuti tikhale oyera, Yehova amasangalala kutithandiza. Pamene tikuyesetsa kuchita zimenezi, timakhalanso kuti tikulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu yemwe ndi woyera. Tikamaphunzira zokhudza makhalidwe a Yehova m’mitu yotsatirayi, tiona kuti tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuti timuyandikire.

a Mawu akuti “milomo yodetsedwa” ndi oyenera, chifukwa nthawi zambiri m’Baibulo mawu akuti milomo amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa potanthauza zolankhula kapena chilankhulo. Machimo ambiri amene anthu ochimwafe timachita amachokera pa zimene timalankhula.​—Miyambo 10:19; Yakobo 3:2, 6.