Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 1

“Taonani! Uyu Ndi Mulungu Wathu”

“Taonani! Uyu Ndi Mulungu Wathu”

1, 2. (a) Kodi ndi mafunso ati amene mungakonde kufunsa Mulungu? (b) Kodi Mose anamufunsa chiyani Mulungu?

 KODI mungamve bwanji mutadziwa kuti Mulungu akufuna kulankhula nanu? N’kutheka kuti mungachite mantha komanso kudabwa kwambiri kuti, ‘Ineyo kulankhula ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse!’ Mwina poyamba mungasowe chonena. Koma tiyerekeze kuti kenako mwayamba kukwanitsa kulankhula naye. Iye akumvetsera, kukuyankhani, ndipo akukuchititsani kukhala womasuka kufunsa funso lililonse limene mukufuna. Ndiye kodi mungamufunse funso lotani?

2 Zimenezi zinamuchitikirapo munthu wina zaka zambiri zapitazo. Dzina lake anali Mose. Komatu mukhoza kudabwa ndi funso limene munthuyu anafunsa Mulungu. Mose sanafunse zokhudza moyo wake, tsogolo lake kapenanso za mavuto a anthu. M’malomwake anafunsa zokhudza dzina la Mulungu. Mwina zimenezi zingakudabwitseni, chifukwa Mose ankadziwa kale dzina la Mulungu. Apatu ndiye kuti funso lake linkatanthauza zambiri. Ndipotu funso limene Mose anafunsali linali lofunika kwambiri chifukwa yankho lake ndi lothandiza kwa tonsefe. Lingakuthandizeni kuti muchite chinthu chofunika kwambiri kuti Mulungu akhale mnzanu. Kuti timvetse chifukwa chake tikutero, tiyeni tione zinthu zochititsa chidwi zimene anakambirana.

3, 4. Kodi panachitika zotani Mose asanayambe kulankhula ndi Mulungu, nanga mfundo yaikulu yokhudza zimene anakambirana inali iti?

3 Pa nthawiyi Mose anali ndi zaka 80. Panali patatha zaka 40 kuchokera pamene anathawa ku Iguputo komwe anthu a mtundu wake, Aisiraeli, anali akapolo. Tsiku lina akudyetsa nkhosa za apongozi ake, anaona chinthu chachilendo. Anaona chitsamba chikuyaka moto koma osanyeka. Chinkangoyakabe, ngati kuwala kooneka m’phiri. Mose anayandikira kuti aone chimene chikuchitika. Iye ayenera kuti anadzidzimuka kwambiri atamva mawu kuchokera pamotowo. Kenako Mulungu, pogwiritsa ntchito mngelo, analankhulana ndi Mose kwanthawi yaitali. Mwina mukudziwa zimene zinachitika pa nthawiyi. Mulungu anauza Mose, amene poyamba ankakayikira, kuti asiye moyo wamtendere umene ankakhala n’kubwerera ku Iguputo kukapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo.​—Ekisodo 3:1-12.

4 Apatu Mose akanatha kufunsa Mulungu funso lina lililonse. Koma taonani funso limene anasankha kufunsa: “Nditati ndapita kwa Aisiraeli n’kuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo n’kundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndi ndani?’ Ndikawayankhe kuti chiyani?”​—Ekisodo 3:13.

5, 6. (a) Kodi funso la Mose limatithandiza kudziwa mfundo ya choonadi yosavuta kumva komanso yofunika kwambiri iti? (b)  Ndi chinthu cholakwika chiti chimene anthu achitira dzina la Mulungu? (c)  N’chifukwa chiyani Mulungu anauza anthu dzina lake?

5 Choyamba, funsoli limatithandiza kudziwa kuti Mulungu ali ndi dzina. Mfundo ya choonadi yosavuta kumva imeneyi sitiyenera kuiona mopepuka. Komatu n’zimene ambiri amachita. M’Mabaibulo ambiri anachotsamo dzina la Mulungu ndipo m’malomwake anaikamo mayina audindo ngati “Ambuye” ndi “Mulungu.” Chimenechi ndi chimodzi mwa zinthu zomvetsa chisoni komanso zolakwika kwambiri zimene zachitika pa zifukwa za chipembedzo. Kodi n’chiyani chimene mumayambirira kuchita mukakumana ndi munthu? Kodi simumayamba mwamufunsa dzina lake? N’chimodzimodzinso pa nkhani yodziwa Mulungu. Sikuti alibe dzina kapena sitingathe kumudziwa ndiponso kumumvetsa. Ngakhale kuti sitingamuone, iye alipo komanso ali ndi dzina, lomwe ndi Yehova.

6 Ndiponso Mulungu akauza anthu dzina lake, pamakhala kuti pali chinthu china chachikulu komanso chosangalatsa chomwe chatsala pang’ono kuchitika. Amafuna kuti timudziwe komanso tisankhe kuchita chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu, chomwe ndi kukhala mnzake. Komatu pali zinanso zimene Yehova wachita kuwonjezera pa kutiuza dzina lake. Watiphunzitsanso kuti iyeyo ndi Mulungu wotani.

Tanthauzo la Dzina la Mulungu

7. (a) Kodi dzina la Mulungu liyenera kuti limatanthauza chiyani? (b) Kodi Mose ankafuna kudziwa chiyani pamene anafunsa Mulungu dzina lake?

7 Yehova anadzipatsa yekha dzina, ndipo dzina lakelo limatiuza zambiri zokhudza iyeyo. Zikuoneka kuti dzina lakuti “Yehova” limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” M’chilengedwe chonse, palibe aliyense amene amafanana naye chifukwa ndi amene analenga zinthu zonse. Amakwaniritsanso zofuna zake zonse ndipo angachititse ngakhale atumiki ake amene si angwiro kuti akhale chilichonse chomwe iye akufuna. Tikaganizira mfundo zimenezi, timaona kuti iye ndi Mulungu wogometsa. Koma kodi dzina la Mulungu limatanthauza zokhazi? N’zodziwikiratu kuti Mose ankafuna kudziwa zambiri. Iye ankadziwa kuti Yehova ndi Mlengi ndipo ankadziwanso dzina la Mulungu. Dzinali silinali lachilendo kwa iye. Panali patatha zaka mahandiredi ambiri kuchokera pamene anthu anayamba kuligwiritsa ntchito. Choncho pofunsa dzina la Mulungu, Mose ankafuna kudziwa zambiri zokhudza Mwiniwake wa dzinalo. Zinali ngati akunena kuti: ‘Kodi anthu anu Aisiraeli ndingakawauze chiyani zokhudza inu, zomwe zingawathandize kuti akukhulupirireni komanso kuwatsimikizira kuti mudzawapulumutsadi?’

8, 9. (a) Kodi Yehova anayankha bwanji funso la Mose, nanga cholakwika n’chiyani ndi mmene Mabaibulo ambiri anamasulira yankho limeneli? (b) Kodi mawu akuti “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala” amatanthauza chiyani?

8 Poyankha, Yehova anatchula mfundo yochititsa chidwi kwambiri yokhudza iyeyo. Mfundo imeneyi imagwirizananso ndi tanthauzo la dzina lake. Anauza Mose kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” (Ekisodo 3:14) Mabaibulo ambiri anamasulira vesi limeneli kuti: “Ine ndine yemwe ndili.” Koma Mabaibulo amene anamasulira mosamala amasonyeza kuti sikuti Mulungu ankangotsimikizira zoti alipo. M’malomwake, ankaphunzitsa Mose ndiponso ifeyo kuti iye ‘adzakhala,’ chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse malonjezo ake. Baibulo lomasuliridwa ndi J. B. Rotherham linamasulira vesili kuti: “Ndidzakhala chilichonse chimene ndikufuna.” Ponena za vesili, katswiri wina wa chilankhulo cha Chiheberi cha m’Baibulo anafotokoza kuti: “Kaya zinthu zili bwanji kapena pakufunika zotani . . . , Mulungu ‘adzakhala’ zimene zikufunikazo.”

9 Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani kwa Aisiraeli? Kaya akanakumana ndi mavuto otani, Yehova akanakhala chilichonse chimene chikanafunika kuti awapulumutse ku ukapolo n’kuwalowetsa m’Dziko Lolonjezedwa. Kunena zoona, kudziwa tanthauzo la dzina la Mulungu kunawathandiza kuti azimudalira. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo masiku ano. (Salimo 9:10) Chifukwa chiyani tikutero?

10, 11. Kodi tanthauzo la dzina la Yehova limatithandiza bwanji kuti tizimuona kuti ndi Atate wabwino kwambiri kuposa aliyense? Perekani chitsanzo.

10 Mwachitsanzo, makolo amadziwa kuti ayenera kusinthasintha kuti asamalire ana awo. Pa tsiku limodzi, kholo lingafunike kusintha, pena kukhala nesi, pena wophika, mphunzitsi, wopereka chilango, woweruza ndi zina zambiri. Makolo ambiri amaona kuti zikuwachulukira ndipo sangakwanitse kuchita zonsezi bwinobwino. Amaona kuti ana awo amawakhulupirira kwambiri. Anawo sakayikira kuti bambo kapena mayi awo awathandiza kuti bala lisiye kuwawa, athetsa mikangano yonse, akonza chidole chilichonse chomwe chawonongeka komanso ayankha mafunso onse amene ali nawo. Makolo ena amadziona kuti ndi osayenera kuwakhulupirira chonchi, ndipo nthawi zina amakhumudwa chifukwa cholephera kuchita zinthu zina. Amaona kuti sangakwanitse kuchita zonse zimene ana awowo akuyembekezera.

11 Yehova nayenso ndi bambo wachikondi. Popanda kuphwanya mfundo zake zolungama, iye angathe kukhala chilichonse kuti asamalire bwino kwambiri ana ake apadziko lapansi. Choncho dzina lake limasonyeza kuti tiyenera kuona kuti Yehova ndi Bambo wabwino kuposa wina aliyense. (Yakobo 1:17) Sipanatenge nthawi kuti Mose ndi Aisiraeli onse okhulupirika aone kuti Yehova amachitadi zinthu mogwirizana ndi dzina lake. Iwo anadabwa kwambiri komanso kuchita mantha kumuona akukhala Mkulu wa Asilikali wosagonjetseka, Wolamulira zinthu zonse zachilengedwe, Wopereka Malamulo wabwino, Woweruza, Wolemba Mapulani, Wopereka chakudya ndi madzi, Wosunga zovala ndi nsapato ndi zina zambiri.

12. Kodi Farao ankasiyana bwanji ndi Mose pa nkhani ya mmene ankaonera Yehova?

12 Choncho Mulungu watidziwitsa dzina lake. Watiphunzitsanso zinthu zochititsa chidwi kwambiri zokhudza iyeyo, yemwe ndi Mwiniwake wa dzinalo, ndiponso wasonyeza kuti zimene amanena zokhudza iyeyo ndi zoona. N’zosachita kufunsa kuti Mulungu amafuna kuti timudziwe. Ndiye kodi ifeyo tikuchitapo chiyani? Mose ankafuna kudziwa Mulungu. Zimenezi zinasintha moyo wake ndipo zinachititsa kuti Atate ake akumwamba akhale mnzake wapamtima. (Numeri 12:6-8; Aheberi 11:27) N’zachisoni kuti anthu ochepa okha m’nthawi ya Mose ndi amene anali ndi mtima wofuna kudziwa Yehova. Mwachitsanzo, Mose atatchula dzina la Yehova kwa Farao, yemwe anali mfumu yodzikuza ya ku Iguputo, Faraoyo anayankha mwamwano kuti: “Yehova ndi ndani?” (Ekisodo 5:2) Farao sankafuna kudziwa zambiri za Yehova. M’malomwake, mopanda ulemu anati Mulungu wa Aisiraeli ndi wosafunika kapenanso wosayenera. Masiku anonso anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa. Maganizowa amalepheretsa anthu kudziwa mfundo ya choonadi yofunika kwambiri yakuti Yehova ndi Ambuye Wamkulu Koposa.

Yehova Ambuye Wamkulu Koposa

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amapatsidwa mayina audindo ambirimbiri m’Baibulo, nanga ena mwa mayinawo ndi ati? (Onani  bokosi patsamba 14.) (b) N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene ali woyenera kutchulidwa kuti “Ambuye Wamkulu Koposa”?

13 Popeza Yehova akhoza kuchita kapena kukhala chilichonse, Malemba amasonyeza kuti ali ndi mayina audindo ambirimbiri. Mayina amenewa saposa dzina lake lenileni, koma amatiphunzitsa zinthu zina zokhudza dzina lakelo. Mwachitsanzo, iye amatchulidwa kuti “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.” (2 Samueli 7:22) Dzina laudindo limeneli limapezeka kambirimbiri m’Baibulo ndipo limasonyeza kuti Yehova ali ndi udindo waukulu kwambiri. Iye yekha ndi amene ali ndi ufulu wokhala Wolamulira wa chilengedwe chonse. Taonani chifukwa chake.

14 Yehova ndi wosiyana ndi aliyense chifukwa ndi Mlengi. Lemba la Chivumbulutso 4:11 limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu chifukwa munalenga zinthu zonse ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” Mawu apadera amenewa amanena za Yehova yekha. Chilichonse m’chilengedwechi chinakhalako chifukwa choti iye anachilenga. N’zosachita kufunsa kuti Yehova ndi woyenera kupatsidwa ulemu, mphamvu ndi ulemerero zomwe Ambuye Wamkulu Koposa komanso Mlengi wa zinthu zonse amayenera kupatsidwa.

15. N’chifukwa chiyani Yehova amatchulidwa kuti “Mfumu yamuyaya”?

15 Dzina lina la udindo limene ndi la Yehova yekha ndi lakuti “Mfumu yamuyaya.” (1 Timoteyo 1:17; Chivumbulutso 15:3) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Yehova wakhala alipo nthawi zonse ndipo adzakhalapo mpaka kalekale, koma kwa anthufe zimenezi n’zovuta kumvetsa. Lemba la Salimo 90:2 limati: “Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.” Choncho Yehova alibe chiyambi, wakhala alipo nthawi zonse. M’pake amatchulidwa kuti “Wamasiku Ambiri.” Anakhalapo kalekale wina aliyense kapena chinthu china chilichonse m’chilengedwechi kulibe. (Danieli 7:9, 13, 22) Ndani angakhale ndi chifukwa chomveka chotsutsa kuti Yehova ndi woyenera kukhala Ambuye Wamkulu Koposa?

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani Yehova sitingathe kumuona, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi siziyenera kutidabwitsa? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi weniweni komanso wapamwamba kwambiri kuposa chilichonse chimene tingathe kuchiona kapena kuchigwira?

16 Komatu anthu ena amaganiza kuti Yehova alibe ufulu umenewo, ngati mmene Farao anachitira. Nthawi zina vutoli limakhalapo chifukwa anthu omwe si angwiro amakonda kudalira zinthu zimene amaziona. Sitingathe kuona Ambuye Wamkulu Koposa. Iye ndi mzimu ndipo anthu sangathe kumuona. (Yohane 4:24) Komanso munthu atati aime pamene pali Yehova Mulungu, akhoza kufa. Yehova anauza Mose kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu amene angandione n’kukhalabe ndi moyo.”​—Ekisodo 33:20; Yohane 1:18.

17 Zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Mose anangoona mbali yochepa ya ulemerero wa Yehova, ndipo ayenera kuti anauona kudzera mwa mngelo amene ankaimira Yehovayo. Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani? Nkhope ya Mose ‘inawala’ kwa kanthawi. Aisiraeli anachita mantha kuyang’ana nkhope ya Mose. (Ekisodo 33:21-23; 34:5-7, 29, 30) Choncho palibe munthu aliyense amene angaone Ambuye Wamkulu Koposa pamasom’pamaso. Koma kodi mfundo yoti sitingathe kumuona ndiponso kumukhudza ikutanthauza kuti Mulunguyo kulibe? Ayi. Pali zinthu zambiri zimene sitivutika kuvomereza kuti zilipo ngakhale kuti sitiziona. Mwachitsanzo, timadziwa kuti pali mphepo, maganizo komanso mphepo youlutsira mawu pawailesi. Ndiponso Yehova sasintha ngakhale patapita zaka mabiliyoni ambirimbiri. Choncho iye ndi weniweni komanso wapamwamba kwambiri kuposa chilichonse chimene tingathe kuchigwira kapena kuchiona, chifukwa zinthu zimenezi zimakalamba komanso zimatha. (Mateyu 6:19) Ndiye kodi tiyenera kumaganiza kuti Mulungu wangokhala mphamvu inayake yosadziwika bwino ndipo alibe nafe ntchito? Tiyeni tione.

Mulungu Ali ndi Makhalidwe Abwino

18. Kodi Ezekieli anaona masomphenya otani, nanga nkhope 4 za “angelo” omwe anali pafupi ndi Yehova zikuimira chiyani?

18 Ngakhale kuti sitingathe kuona Mulungu, m’Baibulo muli nkhani zosangalatsa zimene zimatithandiza kudziwa zinthu zina zakumwamba, zomwe sitingazione. Imodzi mwa nkhanizi ndi yomwe imapezeka m’buku la Ezekieli chaputala 1. M’masomphenya, Ezekieli anaona mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, yomwe inali ngati galeta lalikulu kwambiri. Chochititsa chidwi kwambiri, ndi zimene ananena pofotokoza zokhudza angelo amphamvu omwe anazungulira Yehova. (Ezekieli 1:4-10) “Angelo” amenewa amagwira ntchito yawo pafupi kwambiri ndi Yehova, ndipo maonekedwe awo amatiuza mfundo yofunika kwambiri yokhudza Mulungu amene amamutumikira. Mngelo aliyense anali ndi nkhope 4, nkhope ya ng’ombe, ya mkango, ya chiwombankhanga ndiponso ya munthu. Zimenezi zimaimira makhalidwe 4 akuluakulu a Yehova.​—Chivumbulutso 4:6-8, 10.

19. Kodi nkhope zotsatirazi zimaimira khalidwe liti? (a) Nkhope ya ng’ombe. (b) Nkhope ya mkango. (c) Nkhope ya chiwombankhanga. (d) Nkhope ya munthu.

19 M’Baibulo, nthawi zambiri ng’ombe imaimira mphamvu, ndipotu m’pake chifukwa ng’ombe ndi nyama ya mphamvu kwambiri. Pamene mkango kawirikawiri umaimira chilungamo, chifukwa kuti munthu achite chilungamo amafunika kulimba mtima ndipo mikango imadziwika ndi kulimba mtima. Ziwombankhanga zimadziwika kuti zili ndi maso akuthwa moti zimatha kuona tinthu ting’onoting’ono tomwe tili kutali kwambiri. Choncho nkhope ya chiwombankhanga imaimira nzeru za Mulungu zotha kuona patali. Nanga bwanji nkhope ya munthu? Popeza munthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, amasonyeza khalidwe lalikulu la Mulungu, lomwe ndi chikondi ndipo amachita zimenezi m’njira yapadera kwambiri. (Genesis 1:26) Makhalidwe a Yehova amenewa omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru ndi chikondi, amatchulidwa pafupipafupi m’Malemba moti tinganene kuti ndi makhalidwe akuluakulu a Mulungu.

20. Kodi tiyenera kuda nkhawa kuti mwina Yehova anasintha, nanga n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

20 Kodi tiyenera kuda nkhawa kuti mwina Mulungu wasintha chifukwa padutsa zaka masauzande kuchokera pamene anafotokozedwa m’Baibulo? Ayi, Mulungu sasintha. Iye amatiuza kuti: “Ine ndine Yehova ndipo sindisintha.” (Malaki 3:6) M’malo mongosintha mwachisawawa, Yehova amasonyeza kuti ndi Bambo wabwino pa zinthu zonse zomwe amachita. Pakachitika zinazake, amasonyeza khalidwe lomwe likufunikira kwambiri pa nthawiyo. Pa makhalidwe onse a Mulungu, khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Khalidweli limaonekera pa chilichonse chimene amachita. Amasonyeza mphamvu zake, chilungamo chake ndiponso nzeru zake mwachikondi. Ndipotu Baibulo limatchula mfundo inayake yochititsa chidwi yokhudza khalidwe la Mulungu limeneli. Limati: “Mulungu ndi chikondi.” (1 Yohane 4:8) Onani kuti lembali silikunena kuti Mulungu ali ndi chikondi kapena kuti Mulungu ndi wachikondi. Koma likunena kuti Mulungu ndi chikondi. Zilizonse zomwe amachita, amazichita chifukwa cha chikondi, chomwe ndi khalidwe lake lalikulu.

“Taonani! Uyu Ndi Mulungu Wathu”

21. Kodi timamva bwanji tikadziwa bwino makhalidwe a Yehova?

21 Kodi munaonapo mwana akulozera anzake bambo ake ndiyeno mosangalala ndiponso monyadira n’kunena kuti, “Bambo anga awo”? Atumiki a Mulungu ali ndi zifukwa zomveka zowachititsa kuti azimuonanso choncho Yehova. Baibulo linaneneratu za nthawi imene anthu okhulupirika adzafuule kuti: “Taonani! Uyu ndi Mulungu wathu.” (Yesaya 25:8, 9) Tikadziwa zambiri zokhudza makhalidwe a Yehova, m’pamenenso timayamba kumuona kuti ndi Bambo wathu wabwino kwambiri.

22, 23. Kodi Baibulo limasonyeza kuti Atate wathu wakumwamba ndi wotani, nanga timadziwa bwanji kuti amafuna kuti tikhale anzake?

22 Atate wathu Yehova ndi wachikondi komanso amatidera nkhawa. Sikuti iye alibe chidwi ndi anthu kapena ali nafe kutali ngati mmene anthu ena amanenera. Sitingakopeke ndi Mulungu yemwe sasangalala ndipo Baibulo silisonyeza kuti Atate wathu wakumwamba ndi wotero. M’malomwake limati iye ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Komanso Yehova amasangalala kapenanso kukhumudwa ndi zochita za anthu. Pamene anthu komanso angelo sankatsatira malamulo ake amene anawapatsa kuti aziwathandiza, Baibulo limati: “Zinamupweteka kwambiri mumtima.” (Genesis 6:6; Salimo 78:41) Koma tikamachita zinthu mwanzeru mogwirizana ndi Mawu ake, ‘timasangalatsa mtima’ wake.​—Miyambo 27:11.

23 Atate wathu amafuna kuti tikhale anzake. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘timufufuzefufuze n’kumupezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.’ (Machitidwe 17:27) Koma kodi zingatheke bwanji kuti anthu akhale anzake a Yehova yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa wa chilengedwe chonse?