MUTU 73
Yohane Anakonza Njira
Yohane anali mwana wa Zekariya ndi Elizabeti. Iye atakula anakhala mneneri. Yehova anagwiritsa ntchito Yohane pophunzitsa anthu kuti Mesiya akubwera. Yohane sankaphunzitsa m’masunagoge kapena m’tauni koma ankalalikira m’chipululu. Anthu ochokera ku Yerusalemu komanso ku Yudeya konse ankapita kwa Yohane kuti akawaphunzitse. Iye ankawaphunzitsa kuti akuyenera kusiya kuchita zoipa kuti azisangalatsa Mulungu. Anthu ambiri akamva uthenga wakewu, ankalapa ndipo iye ankawabatiza mumtsinje wa Yorodano.
Yohane sankakonda chuma. Ankavala chovala chaubweya wa ngamila ndipo ankadya dzombe ndi uchi. Anthu ambiri ankachita chidwi ndi Yohane. Nawonso Afarisi ndi Asaduki ankapita kukamuona ngakhale kuti iwo anali onyada. Koma Yohane ankawauza kuti: ‘Muyenera kusiya zoipa n’kulapa. Musaganize kuti ndinu apadera chifukwa chakuti mumati ndinu ana a Abulahamu. Umenewo si umboni woti ndinu ana a Mulungu.’
Anthu ambiri ankapita kwa Yohane kukamufunsa kuti: ‘Titani kuti tisangalatse Mulungu?’ Yohane ankauza Ayuda kuti: ‘Ngati muli ndi malaya awiri, enawo mupatseko munthu amene alibiretu.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake ananena zimenezi? Ankafuna kuti ophunzira ake adziwe zoti, kuti asangalatse Mulungu ayenera kukhala achikondi.
Okhometsa misonkho ankawauza kuti: ‘Muzichita zinthu mwachilungamo ndipo musamabere aliyense.’ Asilikali ankawauza kuti: ‘Musamalandire ziphuphu komanso musamaname.’
Ansembe ndi Alevi nawonso anapita kwa Yohane ndipo anamufunsa kuti: ‘Kodi ndinu ndani? Anthutu akufuna kukudziwani.’ Koma Yohane ankawayankha kuti: ‘Ndine mawu a winawake wofuula m’chipululu. Ndimathandiza anthu kudziwa Yehova mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera.’
Anthu ankasangalala ndi zimene Yohane ankawaphunzitsa. Ambiri ankaganiza kuti mwina ndi Mesiya. Koma Yohane ankawauza kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwera. Ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake. Paja ine ndimabatiza m’madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.’
“Munthu ameneyu anabwera ngati mboni, kuti adzachitire umboni za kuwala nʼcholinga chakuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye.”—Yohane 1:7