MUTU 76
Yesu Anayeretsa Kachisi
M’chaka cha 30 C.E., Yesu anapita ku Yerusalemu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika. Anthu enanso ambiri anapita ku Yerusalemuko kukachita chikondwererochi. Pa nthawiyi, anthu ankapereka nsembe za nyama pakachisi. Ena ankabweretsa nyamazi, koma ena ankagula ku Yerusalemu komweko.
Yesu atalowa m’kachisi anapeza kuti anthu akugulitsa nyama mmenemo. Tangoganiza! Ankachita malonda m’nyumba mwa Yehova mwenimwenimo! Ndiye kodi Yesu anatani? Nthawi yomweyo anatenga zingwe n’kupanga chokwapulira. Ndiyeno anayamba kuthamangitsa nkhosa ndi ng’ombe zimene zinali m’kachisimo. Anagubuduzanso matebulo a anthu amene
ankachita malondawo komanso anakhuthulira pansi ndalama zawo. Iye anauza anthu amene ankagulitsa nkhunda kuti: ‘Chotsani izi muno! Nyumba ya Bambo anga musaisandutse malo ochitira bizinezi!’Anthu anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi. Ophunzira ake anakumbukira ulosi wonena za Mesiya wakuti: ‘Ndidzakhala wodzipereka kwambiri panyumba ya Yehova.’
M’chaka cha 33 C.E., Yesu anayeretsanso kachisi kachiwiri pothamangitsa anthu amene ankachita malonda panyumba ya Yehova. Iye sanalole kuti munthu aliyense azinyoza nyumba ya Yehova.
“Simungakhale akapolo a Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—Luka 16:13