MUTU 89
Petulo Anakana Yesu
Yesu ali m’chipinda chapamwamba, anauza atumwi ake kuti ‘Usiku uno, nonse mundithawa n’kundisiya ndekha.’ Koma Petulo anati: ‘Koma ine ayi. Ngakhale ena onsewa atathawa, ine ndekha sindingakusiyeni.’ Koma Yesu anamuuza kuti: ‘Tambala asanalire, iweyo udzanena katatu kuti sukundidziwa.’
Pa nthawi imene anthu anagwira Yesu kupita naye kwa Kayafa, atumwi onse anathawa komabe awiri ankatsatira gululo. Mmodzi wa amene ankatsatirawo anali Petulo. Iye analowa nawo m’nyumba ya Kayafayo n’kumawotha moto ndi anthu ena. Ndiyeno mtsikana wina wantchito anazindikira Petulo n’kunena kuti: ‘Bambo inu ndakudziwani. Munali ndi Yesu.’
Petulo anayankha kuti: ‘Ayi, ine sindinali ndi ameneyo. Komanso zimene ukunenazo sindikuzidziwa.’ Zitatero ananyamuka n’kumapita cha kugeti. Koma mtsikana winanso wantchito atamuona anauza anthu kuti: ‘Bambo awa analinso ndi Yesu.’ Koma Petulo anati: ‘Inetu Yesuyo sindikumudziwa ngakhale pang’ono.’ Kenako bambo wina anati: ‘Ndiwe wophunzira wa Yesu. Kalankhulidwe kako kakugwiritsa kuti ndiwe wa ku Galileya.’ Koma Petulo analumbira kuti: ‘Ndithu ine sindikumudziwa ameneyo.’
Nthawi yomweyo tambala analira. Kenako Yesu anatembenuka n’kuyang’ana Petulo. Zitatero, Petulo anakumbukira zimene Yesu ananena zija ndipo anapita kunja n’kukayamba kulira kwambiri.
Oweruza mu Khoti Lalikulu la Ayuda anasonkhana m’nyumba ya Kayafa kuti ayambe kuzenga mlandu wa Yesu. Anali atagwirizana kale zoti aphe Yesu moti apa ankangofuna kupeza chifukwa. Koma sanachipeze. Kenako Kayafa anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?’ Yesu anayankha kuti: ‘Inde.’ Zitatero, Kayafa anati: ‘Sipakufunikanso umboni wina. Ameneyu akunyoza Mulungu.’ Oweruza onse anavomereza ndipo anati: ‘Aphedwe basi.’ Kenako ena anaomba Yesu mbama komanso kumulavulira. Ankamuphimba
nkhope n’kumumenya, kenako n’kumanena kuti: ‘Ngati ndiwe mneneri tiuze amene wakumenya.’Kutacha, anapita naye kubwalo loweruzira milandu ndipo anamufunsanso kuti: ‘Kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?’ Yesu anayankha kuti: ‘Mukunena nokha kuti ndine Mwana wa Mulungu.’ Apa anamupeza ndi mlandu wonyoza Mulungu ndipo anapita naye kwa bwanamkubwa wa Chiroma dzina lake Pontiyo Pilato. Kodi kumeneko zinatha bwanji? Tiona m’mutu wotsatira.
“Nthawi . . . yafika kale, pamene nonse mubalalika, aliyense kupita kunyumba kwake ndipo mundisiya ndekha. Koma sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine.”—Yohane 16:32