MUTU 103
“Ufumu Wanu Ubwere”
Yehova analonjeza kuti: ‘Ndidzapukuta misozi yonse m’maso mwa anthu ndipo sipadzakhalanso kulira, kumva kupweteka, matenda kapena imfa. Zoipa zonse zidzaiwalika.’
Yehova anaika Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni kuti azikhala mwamtendere komanso mosangalala. Iwo ankafunika kumalambira Atate wawo wakumwamba komanso kubereka ana mpaka anthu kudzaza dziko lonse. Adamu ndi Hava sanamvere Yehova koma cholinga chake sichinasinthe. Paja Baibulo limanena kuti Mulungu akalonjeza chinthu sichilephereka. Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzabweretsa madalitso osaneneka padzikoli ndipo Ufumu wa Mulungu ndi umene udzabweretse madalitsowo.
Posachedwapa Satana ndi ziwanda zake komanso anthu onse oipa adzawonongedwa. Anthu amene adzapulumuke azidzalambira Yehova. Sipadzakhalanso kudwala kapena kufa. Tsiku lililonse tizidzadzuka amphamvu komanso osangalala. Dziko lonse lidzakhala Paradaiso. Aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira komanso nyumba yabwino. Munthu aliyense adzakhala wachifundo osati wankhanza kapena wachiwawa. Anthu azidzakhala bwinobwino ndi nyama popanda kuopana.
Tidzasangalalanso kwambiri kuona Yehova akuukitsa anthu amene anamwalira. Tidzakumana ndi anthu monga Abele, Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Esitere ndiponso Davide. Tidzathandizana nawo kusintha dzikoli kuti likhale lokongola kwambiri. Padzakhala ntchito zambiri zosangalatsa.
Yehova akufuna kuti inunso mudzakhale m’Paradaiso. Tidzadziwa zambiri zokhudza Yehova kuposa zimene tikudziwa panopa. Choncho tiyeni tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova tsiku lililonse mpaka kalekale.
“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu chifukwa munalenga zinthu zonse ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11