MUTU 25
Chihema Cholambiriramo
Mose ali kuphiri la Sinai, Yehova anamuuza kuti akonze tenti yapadera yolambiriramo ndipo ankaitchula kuti chihema. Iwo anachikonza m’njira yoti azitha kuchinyamula kulikonse kumene akupita.
Yehova anauza Mose kuti: ‘Uza anthu kuti akupatse zinthu zimene angakwanitse kuti upangire chihema.’ Aisiraeli anapereka golide, siliva, kopa, miyala yamtengo wapatali komanso zodzikongoletsera. Anaperekanso ubweya wa nkhosa, nsalu, zikopa zanyama komanso zinthu zina zambiri. Anthuwo anapereka zinthu zambiri mpaka Mose anachita kuwauza kuti: ‘Basi zakwana. Musabweretsenso zina.’
Amuna ndi akazi ambiri aluso anagwira nawo ntchito yomanga chihemachi. Yehova anawapatsa nzeru zowathandiza pogwira ntchitoyi. Ena ankapanga ulusi, kuwomba nsalu komanso kuzikongoletsa. Panalinso ena amene ankapanga zinthu pogwiritsa ntchito miyala, golide kapena mitengo.
Anthuwo anapanga chihema potsatira malangizo amene Yehova anawapatsa. Anapanga katani yokongola imene inagawa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa. M’Malo Oyera Koposa munali bokosi lotchedwa likasa la pangano. Bokosili linapangidwa ndi golide komanso matabwa a mtengo wa mthethe. M’Malo Oyera munali choikapo nyali chagolide, tebulo ndi guwa lansembe zofukiza. Ndipo pabwalo la chihema panali beseni lakopa ndi guwa lalikulu loperekera nsembe zopsereza. Likasa la pangano linkakumbutsa Aisiraeli kuti analonjeza zoti azimvera Yehova. Kodi ukudziwa kuti pangano
n’chiyani? Ndi lonjezo lapadera limene anthu amachita.Yehova anasankha Aroni ndi ana ake aamuna kuti azigwira ntchito kuchihema n’kumapereka nsembe. Ankayenera kusamalira chihemacho komanso kupereka nsembe kwa Yehova. Aroni yekha, yemwe anali mkulu wa ansembe ndi amene ankaloledwa kulowa m’Malo Oyera Koposa. Iye ankachita zimenezi kamodzi chaka chilichonse pokapereka nsembe ya machimo ake, a banja lake komanso a Aisiraeli onse.
Aisiraeli anamaliza kupanga chihemachi patangotha chaka chimodzi kuchokera pamene anatuluka m’dziko la Iguputo. Apa tsopano anali ndi malo olambirira Yehova.
Ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho ndipo mtambo unkakhala pamwamba pake. Mtambowo ukakhala pamwamba pa chihema, Aisiraeli ankakhalabe pamalo omwewo. Koma ukachoka, ankadziwa kuti nthawi yoti anyamuke yakwana. Choncho ankaphwasula chihema chija n’kumatsatira mtambowo ndipo ankakachimanga pamalo ena.
“Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu akuti: ‘Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu ndipo iye azidzakhala nawo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulunguyo adzakhala nawo.’”—Chivumbulutso 21:3