Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 50

Yehova Anathandiza Mfumu Yehosafati

Yehova Anathandiza Mfumu Yehosafati

Yehosafati anali mfumu ya Yuda ndipo anagumula malo operekera nsembe a Baala komanso anawononga mafano onse m’dzikolo. Iye ankafuna kuti anthu adziwe malamulo a Yehova. Choncho anatumiza akalonga ndi Alevi kuti akaphunzitse anthu malamulo a Yehova mu Yuda monse.

Anthu a m’mayiko oyandikana ndi Ayuda ankaopa kuwaukira chifukwa ankadziwa kuti Yehova ali nawo. Anthuwo mpaka ankapereka mphatso kwa Mfumu Yehosafati. Koma Amowabu, Aamoni ndi anthu ochokera ku Seiri anabwera kuti adzamenyane ndi Ayuda. Apa Yehosafati anadziwiratu kuti akufunika kuthandizidwa ndi Yehova. Zitatero anaitanitsa amuna, akazi ndi ana kuti abwere ku Yerusalemu. Anthuwo atafika, iye anapemphera kuti: ‘Yehova, popanda inu sitingapambane nkhondoyi. Chonde tithandizeni chifukwa sitikudziwa chochita.’

Yehova anayankha pempherolo kuti: ‘Musaope chifukwa ndikuthandizani. Aliyense angoima pamalo ake nʼkuona mmene ndingakupulumutsireni.’ Kodi Yehova anawathandiza bwanji?

Tsiku lotsatira, Yehosafati anasankha anthu oimba n’kuwauza kuti aziyenda patsogolo pa asilikali. Anthuwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu mpaka ku Tekowa komwe kunachitikira nkhondoyo.

Iwo ankaimbira Yehova mokweza ndipo iye anamenyera nkhondo anthu ake. Anachititsa kuti Amowabu ndi Aamoni ayambe kuphana okhaokha ndipo palibe amene anapulumuka. Yehova anateteza anthu a ku Yuda, asilikali komanso ansembe. Anthu a m’mayiko oyandikana ndi Ayuda anamva zimene Yehova anachitazi ndipo anadziwa kuti iye akuthandizabe anthu ake. Kodi Yehova amapulumutsa bwanji anthu ake? Amawapulumutsa m’njira zosiyanasiyana ndipo safunika kuthandizidwa ndi anthu kuti achite zimenezi.

“Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo. Aliyense angoima pamalo ake nʼkuona mmene Yehova angakupulumutsireni.”​—2 Mbiri 20:17