Akatswiri a Zamankhwala
Akatswiri a Zamankhwala
MUNTHU wina wazaka 61, wa ku Belgium dzina lake José, amene amachokera m’katauni kotchedwa Oupeye, anauzidwa kuti adzafunika kuikidwa chiŵindi china. “Sindinadandaulepo choncho chibadwire,” iye anatero. Zaka makumi anayi zapitazo, palibe akanaganiza za kuika munthu chiŵindi china. Ngakhale cha m’ma 1970, mwaŵi wakuti upulumuka ukaikidwa chiŵindi unali pafupifupi 30 peresenti basi. Komabe, lero, kuika munthu chiŵindi china kukuchitidwa kaŵirikaŵiri, ndipo kukuyenda bwino kwambiri.
Koma pali vuto lina lalikulu. Chifukwa chakuti nthaŵi zambiri kuika chiŵindi china kumatayitsa magazi ambiri, madokotala nthaŵi zambiri amaika anthuwo magazi m’kati mwa opaleshoniyo. Chifukwa cha chikhulupiriro chake chachipembedzo José sanafune kulandira magazi. Koma anafuna kuti amuike chiŵindi china. Kodi n’zosatheka? Ena angaganize choncho. Koma dokotala wamkulu wa opaleshoni anaona kuti iye pamodzi ndi om’thandiza adakatha kuchita opaleshoniyo bwinobwino popanda kuika magazi. Ndipo zimenezo n’zimenedi iwo anachita! Patangotha masiku 25 okha atachitidwa opaleshoni, José anabwerera kunyumba kukakhalanso limodzi ndi mkazi wake ndi mwana wake wamkazi. *
Chifukwa cha anthu amene magazini ya Time inawatcha kuti “akatswiri a zamankhwala,” chithandizo ndi opaleshoni zopanda kuika munthu magazi tsopano n’zofala kuposa kale lonse. Koma kodi n’chifukwa chiyani ambiri akuzifuna motere? Kuti tiyankhe funso limenelo, tiyeni tione mbiri yovuta ya kuika anthu magazi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mboni za Yehova zimaona kuti zili kwa munthu kusankha malingana ndi chikumbumtima chake ngati akufuna opaleshoni yomuika chiwalo china kapena ayi.
[Chithunzi patsamba 3]
Pakali pano, padziko lonse pali madokotala oposa 90,000 amene adzidziŵikitsa kuti akufuna kuthandiza Mboni za Yehova popanda magazi